YouVersion Logo
Search Icon

YAKOBO 5

5
Achuma ouma mtima atsutsidwa
1 # Miy. 11.28; Luk. 8.24 Nanga tsono achuma inu, lirani ndi kuchema chifukwa cha masautso anu akudza pa inu. 2Chuma chanu chaola ndi zovala zanu zajiwa ndi njenjete. 3#Aro. 2.5Golide wanu ndi siliva wanu zachita dzimbiri, ndipo dzimbiri lake lidzachita mboni zoneneza inu, ndipo zidzadya nyama yanu ngati moto. Mwadzikundikira chuma masiku otsiriza. 4#Deut. 24.15; Mala. 3.5Taonani, mphotho ya antchitowo anasenga m'minda yanu, yosungidwa ndi inu powanyenga, ifuula; ndipo mafuulo a osengawo adalowa m'makutu a Ambuye wa makamu. 5#Luk. 16.19, 25Mwadyerera padziko, ndipo mwachita zokukondweretsani; mwadyetsa mitima yanu m'tsiku lakupha. 6Munamtsutsa, munapha wolungamayo, iye sakaniza inu.
Apirire. Za kulumbira, kupemphera, kubweza wosochera
7 # Deut. 11.14 Potero, lezani mtima, abale, kufikira kudza kwake kwa Ambuye. Taonani, wolima munda alindira chipatso chofunikatu cha dziko, ndi kuleza mtima nacho kufikira chikalandira mvula ya chizimalupsa ndi masika. 8#Afi. 4.5Lezani mtima inunso, limbitsani mitima yanu; pakuti kudza kwake kwa Ambuye kuyandikira. 9#Mat. 24.33; Yak. 4.11Musaipidwe wina ndi mnzake, abale, kuti mungaweruzidwe. Taonani, woweruza aima pakhomo. 10#Aheb. 11.35-38Tengani, abale, chitsanzo cha kumva zowawa ndi kuleza mtima, aneneri amene analankhula m'dzina la Ambuye. 11#Yob. 1.21; Mas. 103.8; Mat. 5.10Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo. 12#Mat. 5.34-37Koma makamaka, abale anga, musalumbire, kungakhale kutchula kumwamba kapena dziko, kapena lumbiro lina lililonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iai wanu akhale iai; kuti mungagwe m'chiweruziro. 13Kodi wina wa inu akumva zowawa? Apemphere. Kodi wina asekera? Aimbire. 14#Mrk. 6.13Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu a Mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye: 15#Mat. 9.2ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye. 16#Gen. 20.17; 1Sam. 12.18; 1Yoh. 3.22Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake. 17#1Maf. 17.1; 18.1; Luk. 4.25Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife, ndipo anapemphera chipempherere kuti isavumbe mvula; ndipo siinagwa mvula pa dziko zaka zitatu kudza miyezi isanu ndi umodzi. 18#1Maf. 18.41-45Ndipo anapempheranso; ndipo m'mwamba munatsika mvula, ndi dziko lidabala zipatso zake.
19 # Mat. 18.15 Abale anga, ngati wina wa inu asochera posiyana ndi choonadi, ndipo ambweza iye mnzake; 20#1Ako. 9.22; 1Pet. 4.8azindikire, kuti iye amene abweza wochimwa kunjira yake yosochera adzapulumutsa munthu kwa imfa, ndipo adzavundikira machimo aunyinji.

Currently Selected:

YAKOBO 5: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in