YouVersion Logo
Search Icon

YESAYA 8

8
Choneneratu chakuti Aasiriya adzagonjetsa Israele
1Ndipo Yehova anati kwa ine, Tenga iwe polembapo papakulu, nulembe pamenepo ndi malembedwe odziwika, Kangazakufunkha Fulumirakusakaza. 2#2Maf. 16.10Ndipo ndidzadzitengera ine mboni zokhulupirika, Uriya wansembe, ndi Zekariya mwana wa Yeberekiya. 3Ndipo ndinanka kwa mneneri wamkazi; ndipo iye anatenga pakati nabala mwana wamwamuna. Ndipo Yehova anati kwa ine, Utche dzina lake, Kangazakufunkha Fulumirakusakaza. 4#Yes. 7.16Chifukwa kuti mwana asakhale ndi nzeru yakufuula, Atate wanga, ndi Amai wanga, chuma cha Damasiko ndi chofunkha cha Samariya chidzalandidwa pamaso pa mfumu ya Asiriya.
5Ndipo Yehova ananena kwa ine kachiwirinso, nati, 6#Neh. 3.15; Yoh. 9.7Popeza anthu awa akana madzi a Siloamu, amene ayenda pang'onopang'ono, nakondwerera mwa Rezini ndi mwa mwana wa Remaliya; 7#Yes. 7.20; 10.12chifukwa chake, taonani, Ambuye atengera pa iwo madzi a mtsinje wa Yufurate, olimba ndi ambiri, kunena mfumu ya Asiriya ndi ulemerero wake wonse; ndipo iye adzadzala mphaluka zake zonse, nadzasefukira pamtunda ponse. 8Ndipo iye adzapitapita kulowa m'Yuda; adzasefukira, napitirira; adzafikira m'khosi; ndi kutambasula kwa mapiko ake, kudzakwanira dziko lanu m'chitando mwake, inu Imanuele.
9 # Yow. 3.9, 11 Chitani phokoso, anthu inu, koma mudzathyokathyoka; tcherani khutu, inu nonse a maiko akutali; kwindani nokha, koma mudzathyokathyoka; kwindani nokha, koma mudzathyokathyoka. 10#Mac. 5.38-39; Aro. 8.31Panganani upo, koma udzakhala chabe; nenani mau, koma sadzachitika; pakuti Mulungu ali pamodzi ndi ife. 11Pakuti Yehova watero kwa ine ndi dzanja lolimba, nandilangiza ine kuti ndisayende m'njira ya anthu awa, nati, 12#1Pet. 3.14-15Musachinene, Chiwembu; chilichonse chimene anthu awa adzachinena, Chiwembu; musaope monga kuopa kwao kapena musachite mantha. 13#1Pet. 3.14-15Yehova wa makamu, Iye mudzamyeretsa; muope Iye, akuchititseni mantha Iye. 14#Ezk. 11.16; Luk. 2.34; Aro. 9.33Ndipo Iye adzakhala malo opatulika; koma mwala wophunthwitsa, ndi thanthwe lolakwitsa la nyumba zonse ziwiri za Israele, khwekhwe ndi msampha wa okhala m'Yerusalemu. 15#Mat. 21.44Ndipo ambiri adzaphunthwapo, nagwa, nathyoka, nakodwa, natengedwa.
16Manga umboni, mata chizindikiro pachilamulo mwa aphunzi anga. 17#Deut. 31.17; Hab. 2.3; Luk. 2.25, 38Ndipo ndidzalindira Yehova, amene wabisira a nyumba ya Yakobo nkhope yake, ndipo ndidzamyembekeza Iye. 18#Zek. 3.8; Aheb. 2.13Taonani, ine ndi ana amene Yehova wandipatsa ine, tili zizindikiro ndi zodabwitsa mwa Israele, kuchokera kwa Yehova wa makamu, amene akhala m'phiri la Ziyoni.
19 # 1Sam. 28.8 Ndipo pamene iwo adzati kwa iwe, Funa kwa olaula, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang'ung'udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wao? Chifukwa cha amoyo, kodi adzafuna kwa akufa? 20#Luk. 16.29Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha. 21Ndipo iwo adzapitirira ovutidwa ndi anjala, ndipo padzakhala kuti pokhala ndi njala iwo adzadziputa okha, ndi kutemberera mfumu yao, ndi Mulungu wao; ndi kugadamira nkhope zao kumwamba; 22nadzayang'ana padziko, koma taonani, nkhawa ndi mdima, kuziya kwa nsautso; ndi mdima woti bii udzaingitsidwa.

Currently Selected:

YESAYA 8: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in