YESAYA 7
7
Rezini ndi Peka akwerera Yerusalemu
1 #
2Maf. 16.5
Ndipo panali masiku a Ahazi, mwana wa Yotamu, mwana wa Uziya, mfumu ya Yuda, kuti Rezini, mfumu ya Aramu, ndi Peka, mwana wa Remaliya, mfumu ya Israele, anakwera kunka ku Yerusalemu, kumenyana nao; koma sanathe kuupambana. 2Ndipo anauza a nyumba ya Davide, kuti Aramu wapangana ndi Efuremu. Ndipo mtima wake unagwedezeka, ndi mtima wa anthu ake, monga mitengo ya m'nkhalango igwedezeka ndi mphepo. 3Ndipo Yehova anati kwa Yesaya, Tuluka tsopano kukachingamira Ahazi, iwe ndi Seari-Yasubu, mwana wamwamuna wako, pa mamaliziro a mcherenje wa thamanda la pamtunda, kukhwalala la pa mwaniko wa wotsuka nsalu; 4nukati kwa iye, Chenjera, khala ulipo; usaope, mtima wako usalefuke, chifukwa cha zidutswa ziwirizi za miuni yofuka, chifukwa cha mkwiyo waukali wa Rezini ndi Aramu, ndi wa mwana wa Remaliya. 5Chifukwa Aramu ndi Efuremu, ndi mwana wa Remaliya anapangana kukuchitira zoipa, nati, 6Tiyeni, tikwere, timenyane ndi Yuda, timvute; tiyeni, tidzigumulire mpata, pamenepo tikhazike mfumu pakati pake, ngakhale mwana wamwamuna wa Tabeele; 7#Miy. 21.30atero Ambuye Yehova, Upo wao sudzaimai, sudzachitidwa. 8Pakuti mutu wa Aramu ndi Damasiko, ndi mutu wa Damasiko ndi Rezini, zisadapite zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu Efuremu adzathyokathyoka, sadzakhalanso mtundu wa anthu; 9#2Mbi. 20.20ndipo mutu wa Efuremu ndi Samariya, ndi mutu wa Samariya ndi mwana wa Remaliya, mukapanda kukhulupirira ndithu simudzakhazikika.
Lonjezo lakunena za Imanuele
10Ndipo Yehova ananenanso kwa Ahazi nati, 11#Ower. 6.36, 37; Mat. 12.38Udzipemphere wekha chizindikiro cha kwa Yehova Mulungu wako; pempha cham'mwakuya, kapena cham'mwamba. 12Koma Ahazi anati, Sindipemphai ngakhale kumyesa Yehova. 13Ndipo iye anati, Mverani inu tsopano, inu a nyumba ya Davide; kodi ndi kanthu kakang'ono kwa inu kutopetsa anthu, kuti inu mutopetsa Mulungu wanga? 14#Yes. 8.8; 9.6; Mat. 1.23Chifukwa chake Ambuye mwini yekha adzakupatsani inu chizindikiro; taonani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, nadzamutcha dzina lake Imanuele. 15Iye adzadya mafuta ndi uchi, pamene adziwa kukana choipa ndi kusankha chabwino. 16#Yes. 8.4Popeza kuti asanadziwe mwanayo kukana choipa ndi kusankha chabwino, dziko limene mafumu ake awiri udana nao lidzasiyidwa. 17#2Mbi. 28.19Yehova adzatengera pa iwe, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba ya atate wako, masiku, akuti sanadze oterewa kuyambira tsiku limene Efuremu analekana ndi Yuda; kunena mfumu ya Asiriya.
18Ndipo padzakhala tsiku limenelo kuti Yehova adzaimbira mluzu ntchentche ili m'mbali ya kumtunda kwa nyanja za Ejipito, ndi njuchi ili m'dziko la Asiriya. 19Ndipo zidzafika nizitera zonse m'zigwa zabwinja, ndi m'maenje a matanthwe, ndi paminga ponse, ndi pamabusa ponse.
20 #
2Maf. 16.7-8
Tsiku limenelo Ambuye adzameta mutu, ndi ubweya wa m'mapazi, ndi lumo lobwereka lili tsidya lija la nyanja, kunena mfumu ya Asiriya; ndilo lidzamalizanso ndevu.
21Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti munthu adzaweta ng'ombe yaikazi yaing'ono, ndi nkhosa ziwiri; 22ndipo padzakhala, chifukwa cha kuchuluka kwa mkaka umene zidzapatsa, iye adzadya mafuta; pakuti mafuta ndi uchi adzadya yense wosiyidwa pakati pa dziko.
23Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti paliponse panali mipesa chikwi chimodzi ya mtengo wake wa sekeli chikwi chimodzi, padzakhala lunguzi ndi minga. 24Munthu adzafikako ndi mivi ndi uta; pakuti dziko lonse lidzakhala la lunguzi ndi minga. 25Ndipo zitunda zonse zinalimidwa ndi khasu, iwe sudzafikako chifukwa cha kuopa lunguzi ndi minga, koma pomwepo padzakhala potumizira ng'ombe ndi popondaponda nkhosa.
Currently Selected:
YESAYA 7: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi