YESAYA 6
6
Masomphenya a Yesaya
1 #
1Maf. 22.19
Chaka chimene mfumu Uziya anafa, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando wachifumu wautali, ndi wotukulidwa, ndi zovala zake zinadzala m'Kachisi. 2Pamwamba pa Iye panaima aserafi; yense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi; awiri anaphimba nao nkhope yake, awiri naphimba nao mapazi ake, awiri nauluka nao. 3#Chiv. 4.8; Mas. 72.19Ndipo wina anafuula kwa mnzake, nati, Woyera, Woyera, Woyera, Yehova wa makamu; dziko lonse lapansi ladzala ulemerero wake. 4#1Maf. 8.10Ndipo maziko a ziundo anasunthika ndi mau amene anafuula, ndipo nyumba inadzazidwa ndi utsi. 5#Yer. 1.6; Luk. 5.8Ndipo ine ndinati, Tsoka kwa ine! Chifukwa ndathedwa; chifukwa ndili munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; chifukwa kuti maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu.
Yesaya akonzedwa akhale mneneri
6Pompo anaulukira kwa ine mmodzi wa aserafi, ali nalo khala lamoto m'dzanja mwake, limene analichotsa ndi mbaniro pa guwa la nsembe; 7#Yer. 1.9nakhudza nalo kukamwa kwanga nati, Taona ichi chakhudza milomo yako; ndipo mphulupulu zako zachotsedwa, zochimwa zako zaomboledwa. 8#Gen. 1.26Ndipo ndinamva mau a Ambuye akuti, Ndidzatumiza yani, ndipo ndani adzatimukira ife? Ndipo ine ndinati, Ndine pano; munditumize ine. 9#Mat. 13.14, 15; Mac. 28.26, 27; Aro. 11.8Ndipo Iye anati, Kauze anthu awa, Imvani inu ndithu, koma osazindikira; yang'anani inu ndithu, koma osadziwitsa. 10#Yer. 5.21Nenepetsa mtima wa anthu awa, lemeretsa makutu ao, nutseke maso ao; angaone ndi maso ao, angamve ndi makutu ao, angazindikire ndi mtima wao, nakabwerenso, nachiritsidwe. 11#Mik. 3.12Pompo ndinati ine, Ambuye mpaka liti? Ndipo anayankha, Mpaka midzi ikhala bwinja, yopanda wokhalamo, ndi nyumba zopanda munthu, ndi dziko likhala bwinja ndithu, 12#2Maf. 25.21ndipo Yehova wasunthira anthu kutali, ndi mabwinja adzachuluka pakati pa dziko. 13#Aro. 11.5Ndipo likatsala limodzi la magawo khumi m'menemo, lidzadyedwanso; monga kachere, ndi monganso thundu, imene tsinde lake likhalabe ataigwetsa; chotero mbeu yopatulika ndiyo tsinde lake.
Currently Selected:
YESAYA 6: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi