YESAYA 5
5
Fanizo la munda wamphesa ndi kumasulira kwake
1 #
Yer. 2.21; Mat. 21.33 Ndiimbire wokondedwa wanga nyimbo ya wokondedwa wanga ya munda wake wamphesa. Wokondedwa wanga anali ndi munda wamphesa m'chitunda cha zipatso zambiri; 2ndipo iye anakumba mcherenje kuzungulira kwete, natolatola miyala pamenepo naokapo mpesa wosankhika, namangapo pakati pake nsanja, nasema mopondera mphesa, nayembekeza kuti udzabala mphesa, koma unangobala mphesa zosadya. 3#Aro. 3.4Ndipo tsopano, inu okhala m'Yerusalemu, ndi anthu a Yuda, weruzanitu mlandu wa ine ndi munda wanga wamphesa. 4Ndikanachitanso chiyani ndi munda wanga wamphesa, chimene sindinachite m'menemo; muja ndinayembekeza kuti udzabala mphesa, wabaliranji mphesa zosadya? 5#Mas. 80.8, 12Ndipo tsopano ndidzakuuzani chimene nditi ndichite ndi munda wanga wamphesa; ndidzachotsapo tchinga lake, ndipo zidzadyedwa; ndidzagumula linga lake ndipo zidzapondedwa pansi; 6ndipo ndidzaupasula; sudzadzomboleredwa kapena kulimidwa; koma padzamera lunguzi ndi minga; ndidzalamuliranso mitambo kuti isavumbwepo mvula. 7Chifukwa kuti munda wamphesa wa Yehova wa makamu ndiwo banja la Israele, ndi anthu a Yuda, mtengo wake womkondweretsa; Iye nayembekeza chiweruziro, koma onani kuphana; nayembekeza chilungamo, koma onani kufuula.
8Tsoka kwa iwo amene aphatikiza nyumba ndi nyumba, amene alumikiza munda ndi munda, kufikira padzapanda malo, ndipo inu mudzasiyidwa nokha pakati pa dziko! 9M'makutu anga, ati Yehova wa makamu, Zoonadi nyumba zambiri zidzakhala bwinja, ngakhale zazikulu ndi zokoma zopanda wokhalamo. 10Chifukwa kuti munda wamphesa wa madera khumi udzangobala bati imodzi ya vinyo, ndi mbeu za maefa khumi zidzangobala efa imodzi.
11 #
Miy. 23.29, 30 Tsoka kwa iwo amene adzuka m'mamawa kuti atsate zakumwa zaukali; amene achezera usiku kufikira vinyo awaledzeretsa! 12Ndipo zeze ndi mngoli, ndi lingaka ndi chitoliro, ndi vinyo, zili m'maphwando ao; koma iwo sapenyetsa ntchito ya Yehova; ngakhale kuyang'ana pa machitidwe a manja ake. 13#Hos. 4.6; Luk. 19.44Chifukwa chake anthu anga amuka m'nsinga, chifukwa cha kusowa nzeru; ndi amuna ao olemekezeka ali ndi njala, ndi khamu lao lauma kukhosi. 14Ndipo manda akuza chilakolako chake, natsegula kukamwa kwake kosayeseka; ndi ulemerero wao, ndi unyinji wao, ndi phokoso lao, ndi iye amene akondwerera mwa iwo atsikira mommo. 15Munthu wonyozeka waweramitsidwa, ndi munthu wotchuka watsitsidwa, ndi maso a wodzikweza atsitsidwa; 16koma Yehova wa makamu wakwezedwa m'chiweruziro, ndipo Mulungu Woyera wayeretsedwa m'chilungamo. 17Pamenepo anaankhosa adzadyapo ngati m'busa mwao, ndi malo a bwinja a zonenepa zachilendo zidzadyapo.
18Tsoka kwa iwo amene akoka mphulupulu ndi zingwe zachabe, ndi tchimo ngati ndi chingwe cha galeta; 19amene ati, Mlekeni iye akangaze, mlekeni iye afulumize ntchito yake kuti ife tione; ndipo lekani uphungu wa Woyera wa Israele uyandikire, udze kuti tiudziwe!
20Tsoka kwa iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa; amene aika mdima m'malo mwa kuyera, ndi kuyera m'malo mwa mdima; amene aika zowawa m'malo mwa zotsekemera, ndi zotsekemera m'malo mwa zowawa!
21 #
Aro. 12.16
Tsoka kwa iwo amene adziyesera anzeru ndi ochenjera!
22 #
Yes. 5.11
Tsoka kwa iwo amene ali a mphamvu yakumwa vinyo, ndi anthu olimba akusanganiza zakumwa zaukali; 23#Miy. 17.15amene alungamitsa woipa pa chokometsera mlandu, nachotsera wolungama chilungamo chake! 24#Eks. 15.7Chifukwa chake monga ngati lilime la moto likutha chiputu, ndi monga udzu wouma ugwa pansi m'malawi, momwemo muzu wao udzakhala monga wovunda, maluwa ao adzauluka m'mwamba ngati fumbi; chifukwa kuti iwo akana chilamulo cha Yehova wa makamu, nanyoza mau a Woyera wa Israele.
25 #
2Maf. 22.13-17
Chifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayaka pa anthu ake, ndipo Iye watambasulira iwo dzanja lake, nawakantha, ndipo zitunda zinanthunthumira, ndi mitembo yao inali ngati zinyatsi pakati pa makwalala. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire. 26#Yes. 11.12Ndipo Iye adzakwezera a mitundu yakutali mbendera, nadzawaimbira mluzu, achokere ku malekezero a dziko; ndipo taonani, iwo adzadza ndi liwiro msangamsanga; 27palibe amene adzalema, kapena adzaphunthwa mwa iwo, palibe amene adzaodzera kapena kugona tulo; ngakhale lamba la m'chuuno mwao silidzamasuka, kapena chomangira cha nsapato zao sichidzaduka; 28amene mivi yao ili yakuthwa, ndi mauta ao onse athifuka; ziboda za akavalo ao zidzayesedwa ngati mwala, ndi njinga zao ngati kamvulumvulu; 29kubangula kwao kudzafanana ndi mkango, iwo adzabangula ngati ana a mikango, inde iwo adzabangula, nadzagwira nyama, naichotsa bwino opanda wakupulumutsa. 30Ndipo iwo adzawabangulira tsiku limenelo ngati kukokoma kwa nyanja; ndipo wina ayang'ana padziko, taonani mdima ndi nsautso, kuyera kwadetsedwanso m'mitambo yake.
Currently Selected:
YESAYA 5: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi