YESAYA 4
4
Tsiku la Mulungu, kuyeretsedwa kwa Yerusalemu
1 #
Gen. 30.33; Yes. 2.11 Ndipo akazi asanu ndi awiri adzagwira mwamuna mmodzi tsiku limenelo, nati, Ife tidzadya chakudya chathuchathu ndi kuvala zovala zathuzathu; koma titchedwe dzina lako; chotsa chitonzo chathu.
2 #
Zek. 3.8
Tsiku limenelo mphukira ya Yehova idzakhala yokongola ndi ya ulemerero, chipatso cha nthaka chidzakhala chokometsetsa ndi chokongola, kwa iwo amene adzapulumuka a Israele. 3#Yes. 60.21; Afi. 4.3Ndipo padzakhala, kuti iye amene asiyidwa m'Ziyoni, ndi iye amene atsala m'Yerusalemu adzatchedwa woyera; ngakhale yense amene walembedwa mwa amoyo m'Yerusalemu; 4#Mala. 3.2-3pamene Ambuye adzasambitsa litsiro la ana akazi a Ziyoni, nadzatsuka mwazi wa Yerusalemu, kuchokera pakatipo, ndi mzimu wa chiweruziro, ndi mzimu wakutentha. 5#Eks. 13.21; Zek. 2.5Ndipo Yehova adzalenga pokhala ponse pa phiri la Ziyoni, ndi pa masonkhano ake, mtambo ndi utsi usana, ndi kung'azimira kwa malawi a moto usiku; chifukwa kuti pa ulemerero wonse padzayalidwa chophimba. 6#Yes. 25.4Ndipo padzakhala chihema cha mthunzi, nthawi ya usana yopewera kutentha, pothawira ndi pousa mvula ndi mphepo.
Currently Selected:
YESAYA 4: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
![None](/_next/image?url=https%3A%2F%2Fimageproxy.youversionapi.com%2F58%2Fhttps%3A%2F%2Fweb-assets.youversion.com%2Fapp-icons%2Fen.png&w=128&q=75)
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi