YESAYA 3
3
1Ndipo onani, Ambuye, Yehova wa makamu, wachotsa ku Yerusalemu ndi ku Yuda mchirikizo wochirikiza chakudya chonse ndi madzi onse, zimene zinali mchirikizo; 2munthu wamphamvu, ndi munthu wankhondo; woweruza ndi mneneri, ndi waula, ndi nkhalamba; 3kapitao wa makumi asanu, ndi munthu wolemekezeka, ndi mphungu, ndi mmisiri waluso, ndi wodziwa matsenga. 4#Mlal. 10.16Ndipo ndidzapereka ana, kuti akhale akulu ao, mwachibwana adzawalamulira. 5Ndi anthu adzavutidwa, yense ndi wina, yense ndi mnansi wake; mwana adzadzinyaditsa yekha pa akulu, ndi onyozeka pa olemekezedwa. 6Pamene mwamuna adzamgwira mbale wake m'nyumba ya atate wake, nadzati, Iwe uli ndi chovala, khala wolamulira wathu, ndi kupasula kumeneku kukhale m'dzanja lako; 7tsiku limenelo adzakweza mau ake, kuti, Sindine wochiritsa, chifukwa kuti m'nyumba mwanga mulibe chakudya kapena chovala; inu simudzandiyesa ine wolamulira anthu. 8#Mik. 3.12Chifukwa kuti Yerusalemu wapasulidwa, ndi Yuda wagwa; chifukwa kuti lilime lao ndi machitidwe ao akana Yehova, kuti autse mkwiyo wa m'maso a ulemerero wake. 9#Gen. 18.20, 21Maonekedwe a nkhope zao awachitira iwo mboni; ndipo amaonetsa uchimo wao monga Sodomu, saubisa. Tsoka kwa moyo wao! Chifukwa iwo anadzichitira zoipa iwo okha. 10#Deut. 28.1-14Nenani za wolungama, kuti kudzamkomera iye; chifukwa oterowo adzadya zipatso za machitidwe ao. 11#Deut. 28.15-68Tsoka kwa woipa! Kudzamuipira; chifukwa kuti mphotho ya manja ake idzapatsidwa kwa iye. 12#Yes. 3.4Anthu anga awavuta ndi ana, awalamulira ndi akazi. Anthu anga inu, iwo amene akutsogolerani, ndiwo akuchimwitsani, naononga njira zanu zoyendamo. 13#Mik. 6.2Yehova aimirira kuti atsutsane, naimiriranso kuti aweruze mitundu ya anthu. 14Yehova adzalowa m'bwalo la milandu ndi okalamba a anthu ake, ndi akulu ake: Ndinu amene mwadya munda wamphesa, zofunkha za waumphawi zili m'nyumba zanu; 15#Mik. 3.2, 3muti bwanji inu, amene mupsinja anthu anga, ndi kupera nkhope ya wosauka? Ati Ambuye Yehova wa makamu.
16Komanso Yehova ati, Chifukwa kuti ana akazi a Ziyoni angodzikuza atakweza makosi ao, ndi maso ao adama nayenda nanyang'ama poyenda pao naliza zigwinjiri za mapazi ao; 17chifukwa chake Ambuye adzachita nkanambo pa liwombo la ana akazi a Ziyoni, ndipo Yehova adzavundukula m'chuuno mwao. 18Tsiku limenelo Ambuye adzachotsa zigwinjiri zao zokoma, ndi zitunga, ndi mphande; 19mbera, ndi makoza, ndi nsalu za pankhope; 20ndi zisada, ndi maunyolo a kumwendo, ndi mipango, ndi nsupa zonunkhira, ndi mphinjiri; 21mphete, ndi zipini; 22malaya a paphwando, ndi zofunda, ndi zimbwi, ndi timatumba; 23akalirole, ndi nsalu zabafuta, ndi nduwira, ndi zophimba. 24Ndipo padzakhala m'malo mwa zonunkhiritsa mudzakhala zovunda; ndi m'malo mwa lamba chingwe; ndipo m'malo mwa tsitsi labwino dazi; m'malo mwa chovala chapachifuwa mpango wachiguduli; zipsera m'malo mwa ukoma. 25Amuna ako adzagwa ndi lupanga, ndi wamphamvu wako m'nkhondo. 26#Yer. 14.2Ndipo zipata zake zidzalira maliro; ndipo iye adzakhala bwinja, nadzakhala pansi.
Currently Selected:
YESAYA 3: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
![None](/_next/image?url=https%3A%2F%2Fimageproxy.youversionapi.com%2F58%2Fhttps%3A%2F%2Fweb-assets.youversion.com%2Fapp-icons%2Fen.png&w=128&q=75)
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi