YouVersion Logo
Search Icon

YESAYA 2

2
Ulemerero wa Israele m'tsogolomo, maweruzo a Mulungu pakatipo
1Mau amene Yesaya mwana wa Amozi anaona, onena za Yuda ndi Yerusalemu. 2#Zek. 8.20-23Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko. 3#Yoh. 4.22Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m'mayendedwe ake; chifukwa m'Ziyoni mudzatuluka chilamulo, ndi mau a Yehova kuchokera m'Yerusalemu. 4#Zek. 9.10Iye adzaweruza pakati pa akunja, adzadzudzula mitundu yambiri ya anthu; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale zolimira, ndi nthungo zao zikhale makasu; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.
5 # Aef. 5.8 Inu a nyumba ya Yakobo, tiyeni, tiyende m'kuwala kwa Yehova. 6Chifukwa inu mwasiya anthu anu a nyumba ya Yakobo, chifukwa kuti iwo adzazidwa ndi miyambo ya kum'mawa, ndipo ali olaula ngati Afilisti, naomba m'manja ndi ana a achilendo. 7Dziko lao ladzala siliva ndi golide, ngakhale chuma chao nchosawerengeka; dziko lao lidzalanso akavalo, ngakhale magaleta ao ngosawerengeka. 8#Yer. 2.28Dziko lao ladzalanso mafano; iwo apembedza ntchito ya manja aoao, imene zala zaozao zinaipanga. 9Munthu wachabe agwada pansi, ndi munthu wamkulu adzichepetsa, koma musawakhululukire. 10#Chiv. 6.15-17Lowa m'phanga, bisala m'fumbi, kuchokera pa kuopsa kwa Yehova, ndi pa ulemerero wachifumu wake. 11#Zek. 9.16; 2Ako. 10.5Maso a munthu akuyang'anira kumwamba adzatsitsidwa, ndi kudzikweza kwa anthu kudzaweramitsidwa pansi; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo. 12Chifukwa padzakhala tsiku la Yehova wa makamu pa zonse zonyada ndi zakudzikuza, ndi pa zonse zotukulidwa; ndipo zidzatsitsidwa; 13ndi pa mitengo yonse yamkungudza ya Lebanoni, yaitali ndi yotukulidwa, ndi pa mitengo yonse yathundu ya Basani; 14ndi pa mapiri onse atali, ndi pa zitunda zonse zotukulidwa; 15ndi pa nsanja zazitali zonse, ndi pa machemba onse; 16ndi pa ngalawa zonse za Tarisisi, ndi pa zithunzithunzi zonse zokondweretsa. 17#2Ako. 10.5Ndipo kudzikweza kwa munthu kudzaweramitsidwa pansi, kudzikuza kwa munthu kudzatsitsidwa; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo. 18Ndimo mafano adzapita psiti. 19#Yes. 2.10Anthu adzalowa m'mapanga a m'matanthwe, ndi m'maenje apansi, kuthawa kuopsa kwa Yehova, ndi ulemerero wachifumu wake, podzuka Iye kugwedeza dziko ndi mphamvu. 20#Yes. 30.22Tsiku limenelo munthu adzataya kumfuko ndi kumileme mafano ake asiliva ndi agolide amene anthu anampangira iye awapembedze; 21#Luk. 23.30kuti akalowe m'mapanga a m'matanthwe, ndi m'mindala a m'miyala, kuthawa kuopsa kwa Yehova, ndi ulemerero wachifumu wake, podzuka Iye kugwedeza dziko ndi mphamvu. 22#Yer. 17.5Siyani munthu, amene mpweya wake uli m'mphuno mwake; chifukwa m'mene awerengedwamo ndi muti?

Currently Selected:

YESAYA 2: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in