YESAYA 9
9
Choneneratu cha ufumu wa Mesiya
1Koma kumene kunali nsautso sikudzakhala kuziya. Poyamba paja Mulungu ananyozetsa dziko la Zebuloni, ndi dziko la Nafutali, koma potsiriza pake Iye analichitira ulemu, pa khwalala la kunyanja, patsidya pa Yordani, Galileya wa amitundu. 2#Mat. 4.15-16; Aef. 5.8, 14Anthu amene anayenda mumdima, aona kuwala kwakukulu; iwo amene anakhala m'dziko la mthunzi wa imfa, kuwala kwatulukira kwa iwo. 3#1Sam. 30.16; Mas. 4.7; Yoh. 4.36Inu mwachulukitsa mtundu, inu mwaenjezera kukondwa kwao; iwo akondwa pamaso panu monga akondwera m'masika, monga anthu akondwa pogawana zofunkha. 4#Ower. 7.19-25Pakuti goli la katundu wake, ndi mkunkhu wa paphewa pake, ndodo ya womsautsa, inu mwazithyola monga tsiku la Midiyani. 5Pakuti zida zonse za mwamuna wovala zida za nkhondo m'phokosomo, ndi zovala zovimvinika m'mwazi, zidzakhala zonyeka ngati nkhuni. 6#Yes. 7.14; Mat. 28.18; Luk. 2.11; Yoh. 3.16; 1Ako. 15.25; Aef. 2.14; Tit. 2.13Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere. 7#Yer. 23.5; Luk. 1.32-33Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.
Aisraele achenjezedwa kuti adzalangidwa
8Ambuye anatumiza mau kwa Yakobo, ndipo anatsikira pa Israele. 9Ndipo anthu onse adzadziwa, ngakhale Efuremu ndi okhala m'Samariya, amene anena m'kunyada ndi m'kukula kwa mtima, 10Njerwa zagwa, koma ife tidzamanga ndi miyala yosema; mikuyu yagwetsedwa, koma tidzaisinthanitsa ndi mikungudza. 11Chifukwa chake Yehova adzamkwezera Rezini olimbana naye, nautsa adani ake; 12Aramu patsogolo ndi Afilisti pambuyo; ndipo iwo adzadya Israele ndi kukamwa koyasama. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.
13 #
Yer. 5.3
Koma anthu sanatembenukire kwa Iye amene anawamenya, ngakhale kufuna Yehova wa makamu. 14Chifukwa chake Yehova adzadula mutu wa Israele ndi mchira wake; nthambi ya kanjedza ndi mlulu, tsiku limodzi. 15Nkhalamba ndi wolemekezeka ndiye mutu, ndi mneneri wophunzitsa zonama ndiye mchira. 16#Yes. 3.12Pakuti iwo amene atsogolera anthuwa, ndiwo awasokeretsa; ndipo iwo amene atsogoleredwa nao aonongeka. 17#Mas. 147.10-11; Yes. 9.12; Mik. 7.2Chifukwa chake Ambuye sadzakondwera ndi anyamata ao, ngakhale kuwachitira chifundo amasiye ao ana ndi akazi; popeza yense ali wodetsa ndi wochimwa, m'kamwa monse mulankhula zopusa. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.
18 #
Mala. 4.1
Pakuti kuchimwa kwayaka ngati moto kumaliza lunguzi ndi minga, inde kuyaka m'nkhalango ya m'thengo, ndipo zifuka chapamwamba, m'mitambo yautsi yochindikira. 19#Yes. 8.22M'kukwiya kwa Yehova wa makamu, dziko latenthedwa ndithu, anthunso ali ngati nkhuni; palibe munthu wochitira mbale wake chisoni. 20#Lev. 26.26Ndipo wina adzakwatula ndi dzanja lamanja, nakhala ndi njala; ndipo adzadya ndi dzanja lamanzere, osakhutai; iwo adzadya munthu yense nyama ya mkono wake wa iye mwini. 21#Yes. 9.17Manase adzadya Efuremu; ndi Efuremu adzadya Manase, ndipo iwo pamodzi adzadyana ndi Yuda. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.
Currently Selected:
YESAYA 9: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi