YESAYA 10
10
1 #
Mas. 94.20
Tsoka kwa iwo amene alamulira malamulo osalungama, ndi kwa alembi olemba mphulupulu; 2kuwapatulira osowa kuchiweruziro, ndi kuchotsera anthu anga aumphawi zoyenera zao, kuti alande za akazi amasiye, nafunkhire ana amasiye! 3#Hos. 9.7; Luk. 19.44Ndipo mudzachita chiyani tsiku lakudza woyang'anira, ndi chipasuko chochokera kutali? Mudzathawira kwa yani kufuna kuthangatidwa? Mudzasiya kuti ulemerero wanu? 4#Yes. 9.21Adzangoweramira pansi pa andende, ndipo adzagwa pansi pa ophedwa. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.
Aneneratu za kuonongeka kwa Asiriya
5 #
Yer. 51.20
Iwe Asiriya chibonga cha mkwiyo wanga, ndodo m'dzanja lake muli ukali wanga! 6#Yer. 34.22Ine ndidzamtumiza kumenyana ndi mtundu wosalemekeza, ndi pa anthu a mkwiyo wanga ndidzamlangiza, kuti afunkhe, agwire zolanda, awapondereze pansi, monga dothi la pamakwalala. 7Koma iye safuna chotero, ndipo mtima wake suganizira chotero, koma mtima wake ulikufuna kusakaza, ndi kuduladula amitundu osawerengeka. 8Popeza ati, Akalonga anga kodi sali onse mafumu? 9#2Mbi. 35.20Kodi Kalino sali wonga ngati Karikemisi? Kodi Hamati sali ngati Aripadi? Kodi Samariya sali ngati Damasiko? 10Popeza dzanja langa lapeza maufumu a mafano, mafano ao osema anapambana ndi iwo a ku Yerusalemu ndi ku Samariya; 11monga ndachitira Samariya ndi mafano ake, momwemo kodi sindidzachitira Yerusalemu ndi mafano ake?
12 #
2Maf. 19.35-37; Yer. 50.18 Chifukwa chake padzaoneka, kuti pamene Ambuye atatha ntchito yake yonse pa phiri la Ziyoni ndi pa Yerusalemu, ndidzalanga zipatso za mtima wolimba wa mfumu ya Asiriya, ndi ulemerero wa maso ake okwezedwa. 13#Ezk. 28.1-10Popeza anati, Mwa mphamvu ya dzanja langa ndachita ichi, ndi mwa nzeru yanga; pakuti ine ndili wochenjera; ndachotsa malekezero a anthu, ndalanda chuma chao, ndagwetsa monga munthu wolimba mtima iwo okhala pa mipando yachifumu; 14dzanja langa lapeza monga chisa, chuma cha mitundu ya anthu, ndipo monga munthu asonkhanitsa dziko lonse lapansi, ndipo panalibe chogwedeza phiko, kapena chotsegula pakamwa, kapena cholira pyepye. 15#Aro. 9.20, 21Kodi nkhwangwa idzadzikweza yokha, pa iye amene adula nayo? Kodi chochekera chidzadzikweza chokha pa iye amene achigwedeza, ngati chibonga ingamgwedeze iye amene ainyamula, ngati ndodo inganyamule kanthu popeza ili mtengo.
16 #
Mas. 106.15
Chifukwa chake Ambuye, Yehova wa makamu, adzatumiza kuonda mwa onenepa ake; ndipo pansi pa ulemerero wake padzayaka kutentha, konga ngati kutentha kwa moto. 17Ndipo kuwala kwa Israele kudzakhala moto, ndi Woyera wake adzakhala lawi; ndipo lidzatentha ndi kuthetsa minga yake ndi lunguzi wake tsiku limodzi. 18Ndipo adzanyeketsa ulemerero wa m'nkhalango yake, ndi wa m'munda wake wopatsa bwino, moyo ndi thupi; ndipo padzakhala monga ngati pokomoka wonyamula mbendera. 19Ndipo mitengo yotsala ya m'nkhalango yake idzakhala yowerengeka, kuti mwana ailembera.
20 #
2Maf. 19.14
Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti otsala a Israele, ndi iwo amene anapulumuka a nyumba ya Yakobo, sadzatsamiranso iye amene anawamenya; koma adzatsamira Yehova Woyera wa Israele, ntheradi. 21Otsala adzabwera, otsala a Yakobo, kwa Mulungu wamphamvu. 22#Aro. 9.26, 27Popeza ngakhale anthu anu Israele akunga mchenga wa kunyanja, otsala ao okhaokha adzabwera; chionongeko chatsimikizidwa chilungamo chake chisefukira. 23Pakuti Ambuye Yehova wa makamu adzachita chionongeko chotsimikizidwa pakati pa dziko lonse lapansi.
24 #
2Maf. 19.6
Chifukwa chake atero Ambuye Yehova wa makamu, Inu anthu anga okhala m'Ziyoni, musaope Asiriya; ngakhale amenya inu ndi chibonga, kapena kukusamulira iwe ndodo yake, monga amachitira Ejipito. 25Pakuti patsala kamphindi, ndipo ukali udzathedwa ndi mkwiyo wanga wakuwaononga. 26#Eks. 14; Ower. 7.25Ndipo Yehova wa makamu adzamuutsira chikoti, monga m'kuphedwa kwa Midiyani pa thanthwe la Orebu; ndipo chibonga chake chidzakhala pamwamba pa nyanja, ndipo adzaisamula monga anachitira Ejipito, 27Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti katundu wake adzachoka pa phewa lako, ndi goli lake pakhosi pako; ndipo goli lidzathedwa chifukwa cha kudzoza mafuta.
28Wafika ku Ayati, wapitirira kunka ku Migironi; pa Mikimasi asunga akatundu ake; 29wapita pampata; wagona pa Geba, Rama anthunthumira; Gibea wa Saulo wathawa. 30Fuula ndi mau ako iwe mwana wamkazi wa Galimu! Tamva, iwe Laisa! Iwe Anatoti wosauka! 31Madimena ali wothawathawa; okhala m'Gebimu asonkhana kuti athawe. 32Lero lomwe adzaima pa Nobu; agwedezera dzanja lake pa phiri la mwana wamkazi wa Ziyoni, phiri la Yerusalemu.
33Taonani, Ambuye Yehova wa makamu adzasadza nthambi moopsa; ndipo zazitali msinkhu zidzadulidwa, ndipo zazitali zidzagwetsedwa. 34Ndipo adzadula nkhalango za m'thengo ndi chitsulo, ndipo Lebanoni adzagwa ndi wamphamvu.
Currently Selected:
YESAYA 10: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi