YouVersion Logo
Search Icon

HOSEYA 7

7
Kuchimwa ndi kupandukira kwa Israele
1M'mene ndichiritsa Israele, mphulupulu ya Efuremu ivumbuluka, ndi zoipa za Samariya; pakuti achita bodza, ndipo mkhungu alowa m'nyumba, ndi gulu la mbala lilanda kubwalo. 2#Mas. 90.8; Yer. 17.1Ndipo sanena m'mtima mwao kuti Ine ndikumbukira zoipa zao zonse; tsopano machitidwe ao awazinga; ali pamaso panga. 3Akondweretsa mfumu ndi zoipa zao, ndi akalonga ndi mabodza ao. 4Achigololo onsewo; akunga ng'anjo anaitenthetsa woocha mkate; aleka kusonkha moto, poyambira kukanda mtanda kufikira watupa mtandawo. 5Tsiku la mfumu yathu akalonga adzidwalitsa ndi kutentha kwa vinyo; iye anatambasula dzanja lake pamodzi ndi oseka. 6Pakuti asendera nao mtima wao wakunga ng'anjo ya mkate, pokhala alikulalira; woocha mkate wao agona usiku wonse, m'mawa iyaka ngati moto wa malawi. 7Onsewo atentha ngati ng'anjo, natha oweruza ao, agwa mafumu ao onse; palibe mmodzi mwa iwo wakuitana Ine. 8#Mas. 106.35Efuremu asokonezana nayo mitundu ya anthu; Efuremu ndiye kamtanda ka mkate kosatembenuzidwa. 9Alendo anatha mphamvu yake osachidziwa iye; imvi zomwe zampakiza osachidziwa iye. 10Ndipo kudzikuza kwa Israele kumchitira umboni pamaso pake; koma sanabwerere kunka kwa Yehova Mulungu wao, kapena kumfunafuna mwa ichi chonse. 11#2Maf. 15.19; 17.4; Hos. 11.11Ndipo Efuremu ali ngati nkhunda yopusa yopanda nzeru; aitanira kwa Ejipito, amuka kwa Asiriya. 12Pamene amuka ndidzawayalira ukonde wanga, ndidzawagwetsa ngati mbalame za m'mlengalenga, ndidzawalanga monga udamva msonkhano wao. 13#Mik. 6.4Tsoka kwa iwowa! Pakuti anandizembera; chionongeko kwa iwowa! Pakuti anandilakwira; ndikadawalanditsa Ine, koma anandinenera zabodza. 14#Yer. 3.10Ndipo sanafuulire kwa Ine ndi mtima wao, koma alira pakama pao, asonkhanira tirigu ndi vinyo, apikisana ndi Ine. 15Chinkana ndawalangiza ndi lulimbitsa manja ao, andilingiririra choipa. 16#Mas. 78.57Abwerera, koma si kwa Wam'mwambayo; akunga uta wosakhulupirika; akalonga ao adzagwa ndi lupanga mwa chipongwe cha lilime lao; ichi ndicho adzawasekera m'dziko la Ejipito.

Currently Selected:

HOSEYA 7: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in