YouVersion Logo
Search Icon

HOSEYA 6

6
Israele abwerera kunka kwa Yehova
1 # 1Sam. 2.6; Yer. 30.17 Tiyeni, tibwerere kunka kwa Yehova; pakuti wang'amba, nadzatipoletsera; wakantha, nadzatimanga. 2Atapita masiku awiri adzatitsitsimutsa, tsiku lachitatu adzatiutsa; ndipo tidzakhala ndi moyo pamaso pake. 3#Yob. 29.23; Yes. 54.13; Yoh. 7.17Tidziwe tsono, tilondole kudziwa Yehova; kutuluka kwake kwakonzekeratu ngati matanda kucha; ndipo adzatidzera ngati mvula, ngati mvula ya masika yakuthirira dziko.
Efuremu ndi Yuda adzudzulidwa
4 # Hos. 13.3 Efuremu iwe, ndidzakuchitira chiyani? Yuda iwe, ndikuchitire chiyani? Pakuti kukoma mtima kwako kukunga mtambo wam'mawa ndi ngati mame akuphawa mamawa. 5Chifukwa chake ndawalikha mwa aneneri; ndawapha ndi mau a pakamwa panga; ndi maweruzo anga atuluka ngati kuunika. 6#1Sam. 15.22; Mas. 50.8-9; Mat. 9.13; 12.7; Yoh. 17.3Pakuti ndikondwera nacho chifundo, si nsembe ai; ndi kumdziwa Mulungu kuposa nsembe zopsereza. 7Koma iwo analakwira chipangano ngati Adamu, m'mene anandichitira monyenga. 8Giliyadi ndiwo mudzi wa ochita zoipa, wa mapazi a mwazi. 9#Hos. 5.1-2Ndipo monga magulu a mbala alalira munthu, momwemo msonkhano wa ansembe amapha pa njira ya ku Sekemu; indedi achita choipitsitsa. 10#Yer. 5.30-31M'nyumba ya Israele ndinaona chinthu choopsetsa; pamenepo pali uhule wa Efuremu; Israele wadetsedwa. 11#Yer. 51.33Akuikidwiratunso nyengo yakukolola, Yuda iwe, pamene ndikabwezanso undende wa anthu anga.

Currently Selected:

HOSEYA 6: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in