HOSEYA 5
5
Kulowerera kwa Israele
1 #
Hos. 6.9
Imvani ichi, ansembe inu; mverani, inu nyumba ya Israele; tcherani khutu, inu nyumba ya mfumu; pakuti chiweruzochi chinena inu; pakuti munakhala msampha ku Mizipa, ndi ukonde woyalidwa pa Tabori. 2Ndipo opandukawo analowadi m'zovunda; koma Ine ndine wakuwadzudzula onsewo. 3#Amo. 3.1-2Ndimdzaiwa Efuremu, ndi Israele sandibisikira; pakuti Efuremu iwe, wachita uhule tsopano, Israele wadetsedwa. 4#Hos. 4.12Machitidwe ao sawalola kubwerera kwa Mulungu wao; pakuti mzimu wa uhule uli m'kati mwao, ndipo sadziwa Yehova. 5Ndipo kudzikuza kwa Israele kudzamchitira umboni pamaso pake; chifukwa chake Israele ndi Efuremu adzakhumudwa m'mphulupulu mwao; Yudanso adzakhumudwa pamodzi nao. 6#Hos. 6.6Adzamuka ndi zoweta zao zazing'ono ndi zazikulu kufunafuna Yehova: koma sadzampeza; Iye wadzibweza kuwachokera. 7#Mala. 2.11Anachita mosakhulupirika pa Yehova, pakuti anabala ana achilendo; mwezi wokhala udzawatha tsopano, pamodzi ndi maiko ao.
8Ombani mphalasa m'Gibea, ndi lipenga m'Rama; fuulani ku Betaveni; pambuyo pako, Benjamini. 9Efuremu adzasanduka bwinja tsiku lakudzudzula; mwa mafuko a Israele ndadziwitsa chodzachitikadi. 10#Deut. 27.17Akalonga a Yuda akunga anthu osuntha malire; ndidzawatsanulira mkwiyo wanga ngati madzi. 11Efuremu azunzika, apsinjika pa mlanduwo; pakuti anafuna mwini wake kutsata lamulolo. 12Ndipo ndikhala kwa Efuremu ngati njenjete, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati chivundi. 13#2Maf. 15.19Pamene Efuremu anaona nthenda yake, ndi Yuda bala lake, Efuremu anamuka kwa Asiriya, natumiza kwa mfumu Yarebu; koma iye sakhoza kukuchiritsani, kapena kupoletsa bala lanu. 14Pakuti ndidzakhala kwa Efuremu ngati mkango, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati msona wa mkango; ndidzamwetula Ine ndi kuchoka; ndidzanyamula, ndipo palibe wakulanditsa. 15#Lev. 26.40-42; Mas. 78.34Ndidzamuka ndi kubwerera kunka kumalo kwanga, mpaka adzavomereza kupalamula kwao, nafunafuna nkhope yanga; m'msauko mwao adzandifunafuna mwachangu.
Currently Selected:
HOSEYA 5: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi