YouVersion Logo
Search Icon

HOSEYA 8

8
Kupembedza mafano ndi kusamvera kwa Israele
1 # Deut. 28.49 Lipenga kukamwa kwako. Akudza ngati chiombankhanga, kulimbana ndi nyumba ya Yehova; chifukwa analakwira chipangano changa, napikisana nacho chilamulo changa. 2#Mas. 78.34Adzafuulira kwa Ine, Mulungu wanga, ife Aisraele tikudziwani. 3Israele wachitaya chokoma, mdani adzamlondola. 4Analonga mafumu, koma sikunachokera kwa Ine; anaika akalonga, koma sindinadziwa; anadzipangira mafano a siliva wao ndi golide wao, kuti akalikhidwe. 5Mwanawang'ombe wako wakutaya, Samariya iwe; mkwiyo wanga wayakira iwo; adzalephera kuyera mtima mpaka liti? 6Pakuti ichi chomwe chafumira kwa Israele; mmisiri wampanga, koma sali Mulungu; inde mwanawang'ombe wa Samariya adzaphwanyikaphwanyika. 7#Miy. 22.8Pakuti abzala mphepo, nadzakolola kamvulumvulu; alibe tirigu wosasenga; ngala siidzatulutsa ufa; chinkana iutulutsa, alendo adzaumeza. 8#2Maf. 17.6Israele wamezedwa; tsopano ali mwa amitundu ngati chotengera choti munthu sakondwera nacho. 9#2Maf. 15.19Pakuti anakwera kunka ku Asiriya, ngati mbidzi ya pa yokha mwini wake; Efuremu walembera omkonda ngati antchito. 10Inde angakhale alembera mwa amitundu ndidzawasonkhanitsa tsopano; ndipo ayamba kuchepa chifukwa cha katundu wa mfumu ya akalonga. 11Popeza Efuremu anachulukitsa maguwa a nsembe akuchimwako, maguwa a nsembe omwewo anamchimwitsa. 12#Deut. 4.6, 8Ndinamlembera zinthu zambirimbirizo za chilamulo changa, koma zinayesedwa ngati chinthu chachilendo. 13#Amo. 5.22Kunena za nsembe za zopereka zanga, aphera nsembe yanyama, naidya; koma Yehova sazilandira; tsopano adzakumbukira mphulupulu yao, nadzalanga zochimwa zao; adzabwerera kunka ku Ejipito. 14#Deut. 32.18Pakuti Israele waiwala Mlengi wake, namanga akachisi; ndipo Yuda wachulukitsa midzi yamalinga; koma ndidzatumizira midzi yake moto, nudzatha nyumba zake zazikulu.

Currently Selected:

HOSEYA 8: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in