EZEKIELE 11
11
Chiweruzo cha Mulungu pa mafumu a Ayuda
1 #
Ezk. 3.12
Pamenepo unandikweza mzimu, nudza nane kuchipata cha kum'mawa cha nyumba ya Yehova choloza kum'mawa; ndipo taonani, pa chitseko cha chipata amuna makumi awiri mphambu asanu; ndipo ndinaona pakati pao Yazaniya mwana wa Azuri ndi Pelatiya mwana wa Benaya, akalonga a anthu. 2Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, awa ndi anthu olingirira za mphulupulu, ndi kupangira uphungu woipa m'mudzi muno; 3#Yer. 1.13ndiwo akuti, siinafike nyengo yakumanga nyumba; mudzi uwu ndi mphika, ife ndife nyama. 4Chifukwa chake uwanenere, neneratu, wobadwa ndi munthu iwe. 5#Ezk. 2.2Pamenepo mzimu wa Yehova unandigwera, ndipo anati kwa ine, Nena, Atero Yehova, Mwatero nyumba ya Israele, pakuti ndidziwa zimene zimalowa m'mtima mwanu. 6Mwachulukitsa ophedwa anu m'mudzi muno, mwadzazanso makwalala ake ndi ophedwawo. 7#Ezk. 24.3-11Chifukwa chake atero Yehova Mulungu, Ophedwa anu munawaika m'kati mwake, iwo ndiwo nyama imene, ndi mudzi uwu ndiwo mphika; koma inu mudzatulutsidwa m'kati mwake. 8Mwaopa lupanga, tsono ndidzakufikitsirani lupanga, ati Yehova Mulungu. 9Ndipo ndidzakutulutsani m'kati mwake, ndi kukuperekani m'manja a alendo, ndi kuchita maweruzo pakati panu. 10Mudzagwa ndi lupanga, ndidzakuweruzirani kumalire a Israele; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 11Mudzi uno sudzakhala mphika wanu, ndi inu simudzakhala nyama m'kati mwake, ndidzakuweruzirani kumalire a Israele; 12#Deut. 12.30-31ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuti simunayenda m'malemba anga, kapena kuchita maweruzo anga, koma mwachita monga mwa maweruzo a amitundu okhala pozungulira panu. 13#Ezk. 11.1-2; Mac. 5.5Ndipo kunali, pakunenera ine, anamwalira Pelatiya mwana wa Benaya. Pamenepo ndinagwa nkhope yanga pansi, ndi kufuula ndi mau akulu, ndi kuti, Kalanga ine, Yehova Mulungu? Mudzatsiriza kodi otsala a Israele?
14Ndipo mau a Yehova anandidzera kuti, 15Wobadwa ndi munthu iwe, abale ako, inde abale ako amuna a chibale chako, ndi nyumba yonse ya Israele, yonseyi ndiwo amene okhala m'Yerusalemu ananena nao, Muzikhala kutali kwa Yehova; dziko ili lapatsidwa kwa ife, likhale cholowa chathu; 16#Mas. 91chifukwa chake uziti, Atero Yehova Mulungu, Ngakhale ndawachotsa kutali mwa amitundu, ngakhalenso ndawabalalikitsa m'maiko, koma ndidzawakhalira malo opatulika kanthawi kumaiko adafikako. 17#Yer. 24.5Chifukwa chake uziti, Atero Yehova Mulungu, Ndidzakumemezani kumitundu ya anthu, ndi kukusonkhanitsani muchoke m'maiko m'mene munabalalikiramo, ndipo ndidzakuninkhani dziko la Israele. 18Ndipo adzafikako, nadzachotsako zonyansa zake zonse, ndi zake zonse zakuipitsamo. 19#Mas. 51.10; Yer. 32.39; Zek. 7.12; Mac. 4.32; 2Ako. 3.3Ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi, ndi kuika mzimu watsopano m'kati mwao; ndipo ndidzawachotsera mtima wamwala m'thupi mwao, ndi kuwapatsa mtima wamnofu; 20#Mas. 105.45; Yer. 30.22kuti ayende m'malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwachita; ndipo adzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wao. 21#Ezk. 9.10Koma iwo amene mtima wao unatsata mtima wa zonyansa zao, ndi zoipitsitsa zao, ndidzawabwezera njira yao pamtu pao, ati Yehova Mulungu. 22#10.19Pamenepo akerubi anatambasula mapiko ao, ndi njinga zinali pa mbali pao; ndi ulemerero wa Mulungu wa Israele unali pamwamba pao. 23Ndipo ulemerero wa Yehova unakwera kuchoka pakati pa mudzi, nuima pa phiri la kum'mawa kwa mudzi. 24Ndipo mzimu unandikweza, nufika nane m'masomphenya mwa mzimu wa Mulungu kudziko la Ababiloni, kwa andendewo. M'mwemo masomphenya ndidawaona anandichokera, nakwera. 25Pamenepo ndinanena ndi andendewo zonse zija adandionetsa Yehova.
Currently Selected:
EZEKIELE 11: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi