EZEKIELE 12
12
Khoma labooledwa lofanizira ukapolo ndi ubalaliko wao
1Mau a Yehova anandidzeranso, ndi kuti, 2#Mat. 13.13-14Wobadwa ndi munthu iwe, ukhala pakati pa nyumba yampanduko, yokhala nao maso akuonera, koma osaona; ndi makutu akumvera, koma osamva; pakuti iwo ndiwo nyumba yampanduko. 3Potero wobadwa ndi munthu iwe, udzikonzeretu akatundu a pa ulendo wa kundende, nuchoke usana pamaso pao, uchoke pokhala iwepo kunka malo ena pamaso pao; kapena adzachizindikira, angakhale ndiwo nyumba yopanduka. 4Uzitulutsa akatundu ako usana pamaso pao, ngati a pa ulendo wa kundende; ndipo madzulo uzituluka wekha pamaso pao, monga amatuluka olowa kundende. 5Udziboolere khoma pamaso pao, nuwatulutsire akatundu pamenepo. 6Pamaso pao uwasenze paphewa pako, ndi kuwatulutsa kuli mdima, nuphimbe nkhope yako kuti usapenye dziko; popeza ndakuika chizindikiro cha nyumba ya Israele. 7Ndipo ndinachita monga momwe anandilamulira, ndinatulutsa akatundu anga usana, ngati a pa ulendo wa kundende, ndi madzulo ndinaboola pakhoma ndi dzanja langa, ndinawatulutsa pali mdima, ndi kuwasenza paphewa panga pamaso pao. 8Ndipo m'mawa mau a Yehova anandidzera, ndi kuti, 9Wobadwa ndi munthu iwe, kodi nyumba ya Israele, nyumba yampanduko, siinati kwa iwe, Uchitanji? 10Unene nao, Atero Ambuye Yehova, Katundu uyu anena za kalonga wa m'Yerusalemu, ndi nyumba yonse ya Israele yokhala pakati pao. 11#Ezk. 12.6Uziti, Ine ndine chizindikiro chanu, monga ndachita ine momwemo kudzachitidwa nao; adzachotsedwa kunka kundende. 12Kalongayo ali pakati pao adzasenza paphewa pake mumdima, nadzatuluka; adzaboola palinga, nadzatulutsapo; adzaphimba nkhope yake kuti asapenye dziko ndi maso ake. 13#2Maf. 25.2-7Ndidzamphimba ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzafika naye ku Babiloni, ku dziko la Ababiloni; sadzaliona, chinkana adzafako. 14Ndipo onse omzinga kumthandiza, ndi magulu ake onse, ndidzawamwaza kumphepo zonse, ndidzawasololeranso lupanga lakuwatsata. 15#Mas. 9.16Motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuwamwaza Ine mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko. 16Koma ndidzawasiya owerengeka apulumuke lupanga, ndi njala, ndi mliri, kuti afotokoze zonyansa zao kwa amitundu kumene afikako; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
17Anandidzeranso mau a Yehova, akuti, 18#Ezk. 4.10-11, 16Wobadwa ndi munthu iwe, udye mkate wako ndi kunthunthumira, ndi kumwa madzi ako ndi kunjenjemera, ndi kutenga nkhawa; 19nunene kwa anthu a m'dziko, Atero Yehova Mulungu za iwo okhala m'Yerusalemu, ndi za dziko la Israele, Adzadya mkate wao ndi nkhawa, ndi kumwa madzi ao ndi kusumwa; pakuti dziko lao lidzakhala lachipululu, kuleka kudzala kwake chifukwa cha chiwawa cha onse okhalamo. 20Ndi midzi yokhalamo anthu idzapasuka, ndi dziko lidzakhala labwinja; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Aneneratu kutsutsa aneneri onama
21Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti, 22#2Pet. 3.4Wobadwa ndi munthu iwe, ngwotani mwambi umene muli nao m'dziko la Israele, wakuti, Masiku achuluka, ndi masomphenya ali onse apita pachabe? 23#Yow. 2.1Chifukwa chake unene nao, Atero Yehova Mulungu, Ndidzaleketsa mwambi uwu, ndipo sadzautchulanso mwambi m'Israele; koma unene nao, Masiku ayandikira, nadzachitika masomphenya ali onse. 24Pakuti sikudzakhalanso masomphenya achabe, kapena ula wosyasyalika m'nyumba ya Israele. 25#Yes. 55.11; Luk. 21.33Pakuti Ine ndine Yehova, ndidzanena, ndi mau ndidzanenawo adzachitika, osazengerezekanso; pakuti m'masiku anu, nyumba yopanduka inu, ndidzanena mau ndi kuwachita, ati Yehova Mulungu.
26Anandidzeranso mau a Yehova, akuti, 27Wobadwa ndi munthu iwe, taona, iwo a nyumba ya Israele akuti, masomphenya awaona ndiwo a masiku ambiri; ndipo anenera za nthawi zili kutali. 28Chifukwa chake uziti nao, Atero Ambuye Yehova, Palibe amodzi a mau anga adzazengerezekanso; koma mau ndidzanenawo adzachitika, ati Ambuye Yehova.
Currently Selected:
EZEKIELE 12: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi