EZEKIELE 10
10
Masomphenya a akerubi
1Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, kuthambo lokhala pamwamba pa mitu ya akerubi kudaoneka ngati mwala wasafiro, ngati maonekedwe a chifaniziro cha mpando wachifumu pamwamba pao. 2#Ezk. 9.2-3; Chiv. 8.5Ndipo Yehova analankhula ndi munthu wovala bafuta, nati, Lowa pakati pa njingazi pansi pa kerubi, nudzaze manja ako makala a moto ochokera pakati pa akerubi, nuwamwaze pamwamba pa mudzi. Nalowa, ndili chipenyere ine. 3Tsono akerubi anaima kudzanja lamanja la nyumba polowa munthuyo, ndi mtambo unadzaza bwalo la m'kati. 4#1Maf. 8.10-11Ndipo ulemerero wa Yehova unakwera kuchokera kukerubi kunka kuchiundo cha nyumba; ndi nyumba inadzala nao mtambo, ndi bwalo linadzala ndi cheza cha ulemerero wa Yehova. 5Ndipo mkokomo wa mapiko a akerubi unamveka mpaka bwalo lakunja, ngati mau a Mulungu Wamphamvuyonse, pakunena Iye. 6Ndipo kunali pomlamulira munthu wovala bafutayo, ndi kuti, Para moto pakati pa njingazi ndi pakati pa akerubi; iye analowa, naima m'mbali mwa njinga. 7Pamenepo kerubi wina anatambasula dzanja lake pakati pa akerubi kumoto uli pakati pa akerubi, napalako, nauika m'manja mwa iye wovala bafuta, ndiye naulandira, natuluka. 8Ndipo panaoneka pa akerubi chonga dzanja la munthu pansi pa mapiko ao. 9Pamenepo ndinapenya, ndipo taonani, njinga zinai m'mbali mwa akerubi, njinga imodzi m'mbali mwa kerubi mmodzi, ndi njinga ina m'mbali mwa kerubi wina, ndi maonekedwe a njingazi ananga mawalidwe a berulo. 10Ndipo maonekedwe ake, zonse zinai zinafanana, ngati njinga ziwiri zopingasitsana. 11Pakuyenda akerubi anayenda kumbali zao zinai, sanatembenuke poyenda; koma komwe udalozako mutu anatsatako, sanatembenuke poyenda. 12Ndipo thupi lao lonse, ndi misana yao, ndi manja ao, ndi mapiko ao, ndi njinga zomwe, zinadzala ndi maso pozungulira pao, zingakhale njingazi anai aja anali nazo. 13Kunena za njingazi, wina anazifuulira, ndili chimvere ine, Kunkhulirani. 14Ndipo aliyense anali nazo nkhope zinai, nkhope yoyamba ndiyo nkhope ya kerubi, ndi nkhope yachiwiri ndiyo nkhope ya munthu, ndi yachitatu ndiyo nkhope ya mkango, ndi yachinai ndiyo nkhope ya chiombankhanga. 15Pamenepo akerubi anakwera, ndizo zamoyo zija ndinaziona kumtsinje Kebara. 16Ndipo pakuyenda akerubi, njinga zinayenda pambali pao, ndi pakutambasula mapiko ao akerubiwo kuuluka padziko, njingazi sizinatembenuka pambali pao. 17Pakuima iwo zinaima izi, ndi pakukwera iwo izi zinakwera pamodzi nao; pakuti mzimu wa zamoyozo unali mwa izo. 18Ndipo ulemerero wa Yehova unachoka pa chiundo cha nyumba, nuima pamwamba pa akerubi. 19Ndipo akerubi anatambasula mapiko ao, nauluka padziko, ndili chipenyere, pakuchoka iwo ndi njingazi pa mbali pao; ndipo anaima pa chitseko cha chipata cha kum'mawa cha nyumba ya Yehova, ndi ulemerero wa Mulungu wa Israele unali pamwamba pao. 20Awa ndi zamoyozo ndinaziona pansi pa Mulungu wa Israele kumtsinje Kebara, ndipo ndinadziwa kuti ndiwo akerubi. 21Yense anali nazo nkhope zinai, ndi yense mapiko anai, ndi chifaniziro cha manja a munthu pansi pa mapiko ao. 22Ndi chifaniziro cha nkhope zao ndicho nkhope zomwezo ndinaziona kumtsinje Kebara, maonekedwe ao ndi iwo eni; aliyense anayenda, nalunjika m'tsogolo.
Currently Selected:
EZEKIELE 10: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi