EKSODO 9
9
Chozizwitsa chachisanu: Kalira pa zoweta
1Pamenepo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao, numuuze, Atero Yehova Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, kuti anditumikire. 2Pakuti ukakana kuwalola amuke, ndi kuwagwira chigwiritsire, 3taona, dzanja la Yehova lidzakhala pa zoweta zako za kubusa, pa akavalo, pa abulu, pa ngamira, pa ng'ombe, ndi pa zoweta zazing'ono ndi kalira woopsa. 4#Eks. 8.22Ndipo Yehova adzasiyanitsa pakati pa zoweta za Israele ndi zoweta za Ejipito; kuti kasafe kanthu kalikonse ka ana a Israele. 5Ndipo Yehova anaika nthawi yakuti, nati, Mawa Yehova adzachita chinthu ichi m'dzikomu. 6Ndipo m'mawa mwake Yehova anachita chinthucho, ndipo zinafa zoweta zonse za m'Ejipito; koma sichinafa chimodzi chonse cha zoweta za ana a Israele. 7Ndipo Farao anatuma, taonani, sichidafa chingakhale chimodzi chomwe cha zoweta za Aisraele. Koma mtima wa Farao unauma, ndipo sanalole anthu amuke.
Chozizwitsa cha 6: Zilonda pa anthu ndi zoweta
8Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, Tengani phulusa la ng'anjo lodzala manja; ndi Mose aliwaze kuthambo pamaso pa Farao. 9#Yob. 2.7; Chiv. 16.2Ndipo lidzakhala fumbi losalala pa dziko lonse la Ejipito, ndipo lidzakhala pa anthu ndi pa zoweta ngati zilonda zobuka ndi matuza, m'dziko lonse la Ejipito. 10Ndipo anatenga phulusa la m'ng'anjo, naima pamaso pa Farao; ndi Mose analiwaza kuthambo; ndipo linakhala zilonda zobuka ndi matuza pa anthu ndi pa zoweta. 11Ndipo alembi sanakhoza kuima pamaso pa Mose chifukwa cha zilondazo; popeza panali zilonda pa alembi ndi pa Aejipito onse. 12Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, kuti sanamvere iwo; monga Yehova adalankhula ndi Mose.
Chozizwitsa cha 7: Matalala
13Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uka nulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao, nunene naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, akanditumikire. 14Pakuti nthawi yino ndidzatuma miliri yanga yonse pamtima pako, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako; kuti udziwe kuti palibe wina wonga Ine pa dziko lonse lapansi. 15Pakuti ndatambasula dzanja langa tsopano, kuti ndikupande iwe ndi anthu ako ndi mliri, ndi kuti uonongeke pa dziko lapansi. 16#Aro. 9.17Koma ndithu chifukwa chake ndakuimika kuti ndikuonetse mphamvu yanga, ndi kuti alalikire dzina langa pa dziko lonse lapansi. 17Kodi udzikwezanso pa anthu anga, ndi kusawalola amuke? 18Taona, mawa monga nthawi yino ndidzavumbitsa mvumbi wa matalala, sipadakhala unzake m'Ejipito kuyambira tsiku lija lidakhazikika kufikira lero lino. 19Ndipo tsopano, tumiza, thawitsa zoweta zako ndi zonse uli nazo pabwalo; pakuti anthu onse ndi zoweta zonse zopezeka pabwalo, zosasonkhanidwa m'nyumba, matalala adzazigwera, ndipo zidzafa. 20Iyeyu wa anyamata a Farao wakuopa mau a Yehova anathawitsira m'zinyumba anyamata ake ndi zoweta zake; 21koma iyeyu wosasamalira mau a Yehova anasiya anyamata ndi zoweta zake kubusa. 22#Chiv. 16.21Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasula dzanja lako kuthambo, kuti pakhale matalala pa dziko lonse la Ejipito, pa anthu ndi pa zoweta, ndi pa zitsamba zonse za kuthengo, m'dziko la Ejipito. 23#Mas. 78.48-49Pamenepo Mose anasamulira ndodo yake kuthambo, ndipo Yehova anatumiza bingu ndi matalala, ndi moto unatsikira pansi; ndipo Yehova anavumbitsa matalala pa dziko la Ejipito. 24Potero panali matalala, ndi moto wakutsikatsika pakati pa matalala, choopsa ndithu; panalibe chotere m'dziko lonse la Ejipito chiyambire mtundu wao. 25Ndipo matalala anapanda m'dziko lonse la Ejipito zonse za pabwalo, kuyambira anthu kufikira zoweta; ndipo matalala anapanda zitsamba zonse za kuthengo, nathyola mitengo yonse ya kuthengo. 26#Eks. 8.22M'dziko la Goseni mokha, mokhala ana a Israele, munalibe matalala. 27#Eks. 10.16; Dan. 9.14Ndipo Farao anatumiza, naitana Mose ndi Aroni, nanena nao, Ndachimwa tsopano; Yehova ndiye wolungama, ine ndi anthu anga ndife oipa. 28Pembani kwa Yehova; chifukwa akwanira ndithu mabingu a Mulungu ndi matalala; ndipo ndidzakulolani mumuke, osakhalanso. 29#Mas. 143.6Ndipo Mose ananena naye, Potuluka m'mudzi ine, ndidzasasatulira manja anga kwa Yehova; mabingu adzaleka, ndi matalala sadzakhalaponso; kuti mudziwe kuti dziko lapansi nla Yehova. 30Koma inu ndi anyamata anu ndidziwa kuti simudzayamba kuopa nkhope ya Yehova Mulungu. 31Ndipo thonje ndi barele zinayoyoka; pakuti barele lidafula, ndi thonje lidayamba maluwa. 32Koma tirigu ndi rai sizinayoyoka popeza amabzala m'mbuyo. 33Ndipo Mose anatuluka kwa Farao m'mudzi nasasatulira manja ake kwa Yehova; ndipo mabingu ndi matalala analeka, ndi mvula siinavumbanso padziko. 34Pamene Farao anaona kuti mvula ndi matalala ndi mabingu zidaleka anaonjezanso kuchimwa, naumitsa mtima wake, iye ndi anyamata ake. 35Potero mtima wa Farao unalimba, ndipo sanalole ana a Israele amuke; monga Yehova adalankhula mwa Mose.
Currently Selected:
EKSODO 9: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi