YouVersion Logo
Search Icon

EKSODO 8

8
Chozizwitsa chachiwiri: Achule
1Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao, nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, kuti anditumikire. 2#Chiv. 16.13Ndipo ukakana kuwalola amuke, taona, Ine ndidzapanda dziko lako lonse ndi achule; 3ndipo m'nyanjamo mudzachuluka achule, amene adzakwera nadzalowa m'nyumba mwako, ndi m'chipinda chogona iwe, ndi pakama pako, ndi m'nyumba ya anyamata ako, ndi pa anthu ako, m'michembo yanu yoocheramo, ndi m'mbale zanu zoumbiramo. 4Ndipo achule adzakwera pa iwe, ndi pa anthu ako, ndi pa anyamata ako onse. 5Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tambasula dzanja lako ndi ndodo yako, panyanja, pangalande, ndi pamatamanda, nukweretse achule pa dziko la Ejipito. 6Ndipo Aroni anatambasula dzanja lake pa madzi a m'Ejipito; ndipo anakwera achule, nakuta dziko la Ejipito. 7Ndipo alembi anachita momwemo ndi matsenga ao, nakweretsa achule pa dziko la Ejipito. 8Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mundipembere Yehova, kuti andichotsere ine ndi anthu anga achulewo; ndipo ndidzalola anthu amuke, kuti amphere Yehova nsembe. 9Koma Mose anati kwa Farao, Ulemu ndi wanu, wa ine ai; ndipembere inu ndi anyamata anu ndi anthu anu liti, kuti aonongeke achulewo, achokere inu ndi nyumba zanu, atsale m'nyanja mokha? 10#Yes. 46.9Ndipo anati, Mawa. Nati Mose, Kukhale monga mau anu, kuti muziwe, kuti palibe wina wonga Yehova Mulungu wathu. 11Ndipo achule adzachokera inu, ndi nyumba zanu, ndi anyamata anu, ndi anthu anu; adzatsala m'nyanja mokha. 12Ndipo Mose ndi Aroni anatuluka kwa Farao; ndi Mose anafuulira kwa Yehova kunena za achule amene adawaika pa Farao. 13Ndipo Yehova anachita monga mwa mau a Mose; nafa achulewo kuchokera m'zinyumba, ndi m'mabwalo, ndi m'minda. 14Ndipo anawaola miulumiulu; ndi dziko linanunkha. 15Koma pamene Farao anaona kuti panali kupuma, anaumitsa mtima wake, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.
Chozizwitsa chachitatu: Nsabwe
16Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Samula ndodo yako, nupande fumbi lapansi, kuti lisanduke nsabwe m'dziko lonse la Ejipito. 17#Mas. 105.31Ndipo anachita chomwecho; pakuti Aroni anasamula dzanja lake ndi ndodo yake, napanda fumbi lapansi, ndipo panali nsabwe pa anthu ndi pa zoweta; fumbi lonse lapansi linasanduka nsabwe m'dziko lonse la Ejipito. 18Alembi anateronso ndi matsenga ao kuonetsa nsabwe, koma sanakhoza; ndipo panali nsabwe pa anthu, ndi pa zoweta. 19#Luk. 11.20Pamenepo alembi anati kwa Farao, Chala cha Mulungu ichi; koma mtima wa Farao unalimba, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.
Chozizwitsa chachinai: Mizaza
20Ndipo Yehova anati kwa Mose Uuke ulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao; taona, atuluka kunka kumadzi; nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, anditumikire. 21Pakuti ukapanda kulola anthu anga amuke, taona, ndidzatuma mizaza pa iwe, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba zako; ndipo nyumba za Aejipito zidzadzala nayo mizaza, ndi nthaka yomwe imene ikhalapo. 22#Eks. 9.4; 11.7Ndipo tsiku ilo ndidzalemba malire dziko la Goseni, m'mene mukhala anthu anga, kuti pamenepo pasakhale mizaza; kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova pakati pa dzikoli. 23Ndipo ndidzaika chosiyanitsa pakati pa anthu anga ndi anthu ako; mawa padzakhala chizindikiro ichi. 24Ndipo Yehova anachita chomwecho; ndipo kunafika magulu a mizaza m'nyumba ya Farao, ndi m'nyumba za anyamata ake, ndi m'dziko lonse la Ejipito; dziko linaipatu chifukwa cha mizazayo. 25Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mukani, mphereni nsembe Mulungu wanu m'dzikomu. 26#Gen. 43.32Koma Mose anati, Sikuyenera kutero; pakuti tidzamphera Yehova Mulungu wathu chonyansa cha Aejipito; taonani, ngati tikamphera nsembe chonyansa cha Aejipito pamaso pao sadzatiponya miyala kodi? 27#Eks. 3.18Timuke ulendo wa masiku atatu m'chipululu, tikamphere Yehova Mulungu wathu nsembe, monga adzanena nafe. 28Ndipo Farao anati, Ndidzakulolani mumuke, kuti mukamphere nsembe Yehova Mulungu wanu m'chipululu; komatu musamuke kutalitu: mundipembere. 29Ndipo Mose anati, Onani, ndilikutuluka ine kwanu, ndidzapemba Yehova kuti mizaza ichoke mawa kwa Farao, ndi kwa anyamata ake, ndi kwa anthu ake; komatu, Farao asanyengenso ndi kukana kulola anthuwa amuke kukamphera nsembe Yehova. 30Ndipo Mose anatuluka kwa Farao, napemba Yehova. 31Ndipo Yehova anachita monga mwa mau a Mose; nachotsera Farao ndi anyamata ake ndi anthu ake mizazayo, sunatsala ndi umodzi wonse. 32Koma Farao anaumitsa mtima wake nthawi yomweyonso, ndipo sanalola anthu amuke.

Currently Selected:

EKSODO 8: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in