EKSODO 7
7
1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Taona, ndakuika ngati Mulungu kwa Farao; ndi Aroni mkulu wako adzakhala mneneri wako. 2#Eks. 4.14-16Iwe uzilankhula zonse ndikulamulira; ndi Aroni mkulu wako azilankhula kwa Farao, kuti alole ana a Israele atuluke m'dziko lake. 3Koma Ine ndidzaumitsa mtima wake wa Farao, ndipo ndidzachulukitsa zizindikiro ndi zozizwa zanga m'dziko la Ejipito. 4Koma Farao sadzamvera inu, ndipo ndidzaika dzanja langa pa Aejipito, ndipo ndidzatulutsa makamu anga, anthu anga ana a Israele, m'dziko la Ejipito ndi maweruzo akulu. 5Ndipo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakutambasula Ine dzanja langa pa Aejipito, ndikutulutsa ana a Israele pakati pao. 6Ndipo Mose ndi Aroni anachita monga Yehova anawalamulira, momwemo anachita. 7Ndipo Mose anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu, ndi Aroni anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu kudza zitatu, pamene ananena ndi Farao.
Mose ndi amatsenga
8Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, ndi kuti, 9Pamene Farao adzalankhula nanu, ndi kuti, Dzichitireni chodabwitsa; pamenepo uzinena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, iponye pansi pamaso pa Farao, isanduke chinjoka. 10Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao, nachita monga momwe Yehova adawalamulira; ndipo Aroni anaponya pansi ndodo yake pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndipo inasanduka chinjoka. 11#Gen. 41.8Pamenepo Farao anaitananso anzeru, ndi amatsenga; ndipo alembi a Aejipito, iwonso anachita momwemo ndi matsenga ao. 12Pakuti yense anaponya pansi ndodo yake, ndipo zinasanduka zinjoka; koma ndodo ya Aroni inameza ndodo zao. 13#Eks. 7.3Koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvere iwo; monga adalankhula Yehova.
Chozizwitsa choyamba: Madzi asanduka mwazi
14Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Walemera mtima wa Farao, akana kulola anthu apite. 15Muka kwa Farao m'mawa; taona, atuluka kunka kumadzi; nuime kumlinda m'mbali mwa nyanja; ndi ndodo idasanduka njokayo uigwire m'dzanja lako. 16Ndipo ukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri anandituma kwa inu, ndi kuti, Lola anthu anga amuke kuti anditumikire m'chipululu; koma, taona, sunamvera ndi pano. 17#Chiv. 16.4Atero Yehova, Ndi ichi udzadziwa kuti Ine ndine Yehova; taonani, ndidzapanda madzi ali m'nyanja ndi ndodo ili m'dzanja langa, ndipo adzasanduka mwazi. 18Ndi nsomba zili m'nyanja zidzafa, ndi nyanja idzanunkha; ndi Aejipito adzachita mtima useru ndi kumwa madzi a m'nyanjamo. 19Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, nutambasule dzanja lako pa madzi a m'Ejipito, pa nyanja yao, pa ngalande zao, ndi pa matamanda ao, ndi pa matawale ao onse amadzi, kuti asanduke mwazi; mukhale mwazi m'dziko lonse la Ejipito, m'zotengera zamtengo, ndi zamwala. 20#Mas. 78.44; 105.29Ndipo Mose ndi Aroni anachita monga momwe Yehova adawalamulira; nasamula ndodo, napanda madzi ali m'nyanjamo pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake; ndipo madzi onse a m'nyanjamo anasanduka mwazi. 21Ndi nsomba za m'nyanjamo zinafa; ndi nyanjayo inanunkha; ndipo Aejipito sanakhoze kumwa madzi a m'nyanjamo; ndipo munali mwazi m'dziko lonse la Ejipito. 22Ndipo alembi a Aejipito anachita momwemo ndi matsenga ao; koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvere iwo; monga adalankhula Yehova. 23Ndipo Farao anatembenuka, nalowa m'nyumba yake, osasamalira ichi chomwe mumtima mwake. 24Koma Aejipito onse anakumba m'mphepete mwa nyanja kufuna madzi akumwa; pakuti sanakhoze kumwa madzi a m'nyanjamo. 25Ndipo anafikira masiku asanu ndi awiri atapanda nyanja Yehova.
Currently Selected:
EKSODO 7: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi