Taona, mawa monga nthawi yino ndidzavumbitsa mvumbi wa matalala, sipadakhala unzake m'Ejipito kuyambira tsiku lija lidakhazikika kufikira lero lino. Ndipo tsopano, tumiza, thawitsa zoweta zako ndi zonse uli nazo pabwalo; pakuti anthu onse ndi zoweta zonse zopezeka pabwalo, zosasonkhanidwa m'nyumba, matalala adzazigwera, ndipo zidzafa.