Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao; pakuti ndaumitsa mtima wake, ndi mtima wa anyamata ake, kuti ndiike zizindikiro zanga izi pakati pao; ndi kuti ufotokozere m'makutu a ana ako, ndi a zidzukulu zako, chomwe ndidzachita m'Ejipito, ndi zizindikiro zanga zimene ndinaziika pakati pao; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.