YouVersion Logo
Search Icon

EKSODO 10

10
Chozizwitsa cha 8: Dzombe
1Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao; pakuti ndaumitsa mtima wake, ndi mtima wa anyamata ake, kuti ndiike zizindikiro zanga izi pakati pao; 2#Deut. 4.9; Yow. 1.3ndi kuti ufotokozere m'makutu a ana ako, ndi a zidzukulu zako, chomwe ndidzachita m'Ejipito, ndi zizindikiro zanga zimene ndinaziika pakati pao; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova. 3#1Maf. 21.29Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzichepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire; 4#Chiv. 9.3pakuti ukakana kulola anthu anga amuke, taona, mawa ndidzafikitsa dzombe m'dziko lako; 5ndipo lidzakuta nkhope ya dziko, kotero kuti palibe munthu adzakhoza kuona dziko; ndipo lidzadya zotsalira zidapulumuka, zidatsalira inu pamatalala, ndipo lidzadya mtengo uliwonse wokuphukirani kuthengo; 6ndipo lidzadzaza m'nyumba zako, ndi m'nyumba za anyamata ako onse, ndi m'nyumba za Aejipito onse; sanachione chotere atate ako kapena makolo ako, kuyambira tsiku lija lakukhala iwo pa dziko lapansi kufikira lero lino. Ndipo anatembenuka, natuluka kwa Farao. 7Ndipo anyamata ake a Farao ananena naye, Ameneyo amatichitira msampha kufikira liti? Lolani anthuwo amuke, akatumikire Yehova Mulungu wao. Kodi simunayambe kudziwa kuti Ejipito laonongeka? 8Ndipo anawabwereretsa Mose ndi Aroni kwa Farao, nanena nao, Mukani, katumikireni Yehova Mulungu wanu. Koma amene adzapitawo ndiwo yani? 9Ndipo Mose anati, Tidzamuka ndi ana athu ndi akulu athu, ndi ana athu aamuna ndi aakazi; tidzamuka nazo nkhosa zathu ndi ng'ombe zathu; pakuti tili nao madyerero a Yehova. 10Ndipo ananena nao, Momwemo, Yehova akhale nanu ngati ndilola inu ndi ana ang'ono anu mumuke; chenjerani pakuti pali choipa pamaso panu. 11Chotero ai, mukani tsopano, inu amuna akulu, tumikirani Yehova pakuti ichi muchifuna. Ndipo anawapirikitsa pamaso pa Farao.
12Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako pa dziko la Ejipito, lidze dzombe, kuti likwere pa dziko la Ejipito, lidye zitsamba zonse za m'dziko, ndizo zonse adazisiya matalala. 13Pamenepo Mose analoza ndodo yake pa dziko la Ejipito; ndipo Yehova anaombetsa padziko mphepo ya kum'mawa usana wonse, ndi usiku womwe; ndipo kutacha mphepo ya kum'mawa inadza nalo dzombe. 14Ndipo dzombe linakwera pa dziko lonse la Ejipito, ndipo linatera pakati pa malire onse Ejipito, lambirimbiri; lisanafike ili panalibe dzombe lotere longa ili, ndipo litapita ili sipadzakhalanso lotere. 15Pakuti linakuta nkhope ya dziko lonse kuti dziko linada; ndipo linadya zitsamba zonse za m'dziko, ndi zipatso zonse za mitengo zimene matalala adazisiya; ndipo sipanatsala chabiriwiri chilichonse, pamitengo kapena pa zitsamba za kuthengo, m'dziko lonse la Ejipito. 16#Eks. 9.27Pamenepo Farao anafulumira kuitana Mose ndi Aroni; nati, Ndalakwira Yehova Mulungu wanu, ndi inu. 17Ndipo tsopano, ndikhululukiretu kulakwa kwanga nthawi yino yokha, nimundipembere kwa Yehova Mulungu wanu, kuti andichotsere imfa yino yokha. 18Ndipo anatuluka kwa Farao, napemba Yehova. 19Ndipo Yehova anabweza mphepo yolimbatu ya kumadzulo, imene inapita nalo dzombe niliponya m'Nyanja Yofiira: silinatsala dzombe limodzi pakati pa malire onse a Ejipito. 20Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, ndipo sanalole ana a Israele amuke.
Chozizwitsa cha 9: Mdima
21Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako kuthambo, ndipo padzakhala mdima pa dziko la Ejipito, ndiwo mdima wokhudzika. 22#Mas. 105.28Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kuthambo; ndipo munali mdima bii m'dziko lonse la Ejipito masiku atatu; 23sanaonane, sanaukenso munthu pamalo pake, masiku atatu; koma kwa ana onse a Israele kudayera m'nyumba zao. 24Ndipo Farao anaitana Mose, nati, Mukani, tumikirani Yehova; nkhosa zanu ndi ng'ombe zanu zokha zitsale; mumuke nao ana anu ang'ononso. 25Koma Mose anati, Mutipatsenso m'dzanja mwathu nsembe zophera ndi nsembe zopsereza, kuti timkonzere Yehova Mulungu wathu. 26Zoweta zathu zomwe tidzapita nazo; chosatsala chiboda chimodzi; pakuti mwa izo tiyenera kutenga zakutumikira nazo Yehova Mulungu wathu; ndipo tisanafikeko, sitidziwa umo tidzamtumikira Yehova. 27Koma Yehova analimbitsa mtima wake wa Farao, ndipo anakana kuwaleka amuke. 28Ndipo Farao ananena naye, Choka pano, uzichenjera usaonenso nkhope yanga; pakuti tsiku limene uonanso nkhope yanga udzafa. 29Ndipo Mose anati, Mwanena bwino; sindidzaonanso nkhope yanu.

Currently Selected:

EKSODO 10: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in