YouVersion Logo
Search Icon

EKSODO 27

27
Za guwa la nsembe
1 # Eks. 38.1-7; Ezk. 43.13 Ndipo upange guwa la nsembe la mtengo wakasiya, utali wake mikono isanu, ndi kupingasa kwake mikono isanu, guwa la nsembelo likhale laphwamphwa, ndi msinkhu wake mikono itatu. 2Ndipo uzipanga nyanga zake pangodya zake zinai; nyanga zake zikhale zotuluka m'mwemo: nulikute ndi mkuwa. 3Ndipo uzipanga zotayira zake zakulandira mapulusa ake, ndi zoolera zake, ndi mbale zowazira zake, ndi mitungo yake, ndi zopalira moto zake; zipangizo zake zonse uzipanga zamkuwa. 4Ndipo ulipangire sefa, malukidwe ake ndi amkuwa; nupange pa malukidwewo ngodya zake zinai mphete zinai zamkuwa. 5Nuwaike pansi pa khoma lamkati la guwa la nsembelo posungulira, kuti malukidwe alekeze pakati pa guwa la nsembelo. 6Ndipo upangire guwa la nsembe mphiko, mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi mkuwa. 7Ndipo apise mphiko m'mphetezo kuti mphikozo zikhale pa mbali ziwiri za guwa la nsembe polinyamula. 8#Eks. 25.40Ulipange lagweregwere ndi matabwa; monga anakuonetsa m'phirimo; alipange momwemo.
Za bwalo la chihema
9 # Eks. 38.9 Upangenso bwalo la chihema; pa mbali yake ya kumwera, kumwera, pakhale nsalu zochingira za kubwalo za nsalu yabafuta wa thonje losansitsa, utali wake wa pa mbali imodzi mikono zana; 10ndi nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri akhale amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zikhale zasiliva. 11Momwemonso pa mbali ya ku kumpoto m'utali mwake pakhale nsalu zochingira za mikono zana limodzi m'utali mwake; ndi nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao akhale amkuwa; zokowera za nsichizo ndi mitanda yake zikhale zasiliva. 12Ndipo m'kupingasa kwa bwaloli pa mbali ya kumadzulo mukhale nsalu zochingira za mikono makumi asanu; nsichi zake zikhale khumi, ndi makamwa ao khumi. 13Ndipo m'kupingasa kwake kwa bwalo pa mbali ya kum'mawa, kum'mawa, mukhale mikono makumi asanu. 14Ndi nsalu zochingira za pa mbali imodzi ya kuchipata zikhale za mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zikhale zitatu, ndi makamwa ao atatu. 15Ndi pa mbali ina pakhale nsalu zochingira za mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zikhale zitatu, ndi makamwa ao atatu. 16Ndipo pa chipata cha bwalolo pakhale nsalu yotsekera ya mikono makumi awiri, ya lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula; nsichi zake zikhale zinai, ndi makamwa ao anai. 17Nsichi zonse za pabwalo pozungulira zimangike pamodzi ndi mitanda yasiliva; zokowera zao zasiliva, ndi makamwa ao amkuwa. 18Utali wake wa bwalolo ukhale wa mikono zana limodzi, ndi kupingasa kwake makumi asanu monsemo, ndi msinkhu wake wa mpanda mikono isanu; ukhale wabafuta wa thonje losansitsa; ndi makamwa a nsichizo akhale amkuwa. 19Zipangizo zonse za Kachisi, m'machitidwe ake onse, ndi zichiri zake zonse, ndi zichiri zonse za bwalo lake, zikhale zamkuwa.
Za mafuta a nyaliyo
20 # Lev. 24.2 Ndipo uuze ana a Israele akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti awalitse nyali kosalekeza. 21Aroni ndi ana ake aikonze m'chihema chokomanako, kunja kwa nsalu yotchinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israele.

Currently Selected:

EKSODO 27: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in