YouVersion Logo
Search Icon

EKSODO 26

26
Kachisi ndi nsalu zophimba zake
1 # Eks. 36 Ndipo uzipanga Kachisi ndi nsalu zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemo akerubi, ntchito ya mmisiri. 2Utali wake wa nsalu yophimba imodzi ndiwo mikono makumi awiri kudza isanu ndi itatu, ndi kupingasa kwa nsalu imodzi ndiko mikono inai; nsalu zonse zikhale za muyeso umodzi. 3Nsalu zisanu zilumikizane ina ndi inzake; ndi nsalu zisanu zina zilumikizane ina ndi inzake. 4Ndipo uziika magango a nsalu ya madzi m'mphepete mwake mwa nsalu imodzi, ku mkawo wa chilumikizano; nuchite momwemo m'mphepete mwake mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china. 5Uziika magango makumi asanu pa nsalu yochingira imodzi, nuikenso magango makumi asanu m'mphepete mwake mwa nsalu ya chilumikizano china; ndipo magango akomanizane lina ndi linzake. 6Uzipanganso zokowera makumi asanu zagolide, ndi kumanga nsaluzo pamodzi ndi zokowerazo; kuti Kachisi akhale mmodzi. 7Ndipo uziomba nsalu zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale hema pamwamba pa Kachisi; uziomba nsalu khumi ndi imodzi. 8Utali wake wa nsalu imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi ndiko mikono inai; nsalu khumi ndi imodzi zikhale za muyeso womwewo. 9Nuzisoka pamodzi nsalu zisanu pa zokha, ndi nsalu zisanu ndi imodzi pa zokha, nupinde nsalu yachisanu ndi chimodziyo pa khomo la hema. 10Ndipo uziika magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu imodzi, ya kuthungo ya chilumikizano, ndi magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china. 11Ndipo uzipanga zokowera makumi asanu zamkuwa, ndi kukowetsa zokowerazo m'magangomo, ndi kumanga pamodzi hemalo likhale limodzi. 12Ndipo chotsalacho pa nsalu za hemalo, hafu yake ya nsalu yotsalirayo, ichinge pambuyo pake pa Kachisi. 13Ndi mkono wa pa mbali yino, ndi mkono wa pa mbali inzake, wakutsalira m'utali wake wa nsalu za hemalo, ichinge pambali zake za Kachisi, mbali yino ndi mbali ina, kumphimba. 14Ndipo uzipangira hema chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi chophimba za zikopa za akatumbu pamwamba pake.
Za matabwa oimirika a Kachisi
15Ndipo uzipangira Kachisi matabwa oimirika, a mtengo wakasiya. 16Utali wake wa thabwa limodzi ndiwo mikono khumi, ndi kupingasa kwake kwa thabwali mkono ndi hafu. 17Pa thabwa limodzi pakhale mitsukwa iwiri, yomangika pamodzi; uzitero pa matabwa onse a Kachisi. 18Ndipo uzipanga matabwa a Kachisi, matabwa makumi awiri ku mbali ya kumwera, kumwera. 19Nuzipanga makamwa makumi anai asiliva pansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yake iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yake iwiri; 20ndi pa mbali yake ina ya Kachisi, mbali ya kumpoto, pakhale matabwa makumi awiri; ndi makamwa asiliva makumi anai; 21makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina. 22Ndipo uzipanga matabwa asanu ndi limodzi kwa mbali ya Kachisi ya kumbuyo. 23Nupange matabwa awiri angodya za Kachisi za kumbuyo. 24Ndipo akhale ophatikizika pamodzi patsinde, nakhalenso ophatikizika pamodzi kumutu kwake ndi mphete imodzi; azitero onse awiri; azikhala angodya ziwiri. 25Ndipo pakhale matabwa asanu ndi atatu, ndi makamwa ao asiliva, ndiwo makamwa khumi mphambu asanu ndi limodzi; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina. 26Ndipo uzipanga mitanda ya mtengo wakasiya; isanu ya matabwa a pa mbali ina ya Kachisi, 27ndi mitanda isanu ya matabwa a pa mbali ina ya Kachisi, ndi mitanda isanu ya matabwa a pa mbali ya Kachisi ya kumbuyo kumadzulo. 28Ndi mtanda wa pakati pa matabwa ufikire kuthungo. 29Ndipo uzikuta matabwa ndi golide, ndi kupanga mphete zao zagolide zopisamo mitandayo; uzikutanso mitandayo ndi golide. 30#Aheb. 8.5Ndipo uutse Kachisi monga mwa makhalidwe ake amene anakusonyeza m'phiri.
Za nsalu yosiyanitsa ya pakhomo
31 # Eks. 36.35 Ndipo uziomba nsalu yotchinga ya thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi la bafuta wa thonje losansitsa, aiombe ndi akerubi ntchito ya mmisiri; 32ndipo uichinge pa mizati inai ya mitengo wakasiya, zokuta ndi golide; zokowera zao zikhale zagolide, ndi makamwa anai asiliva. 33Ndipo uzitchinga nsalu yotchinga pa zokowerazo, nulowetse likasa la mboni kukati kwa nsalu yotchinga; ndipo nsalu yotchingayo idzakugawirani pakati pa malo opatulika ndi malo opatulika kwambiri. 34Ndipo uziika chotetezerapo pa likasa la mboni, m'malo opatulika kwambiri. 35Nuziika gomelo kunja kwa nsalu yotchinga, ndi choikapo nyali pandunji pa gome, pa mbali ya kumwera ya Kachisi; koma uike gomelo pa mbali ya kumpoto. 36Ndipo uziomba nsalu yotsekera pa khomo la hema, ya lakuda, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula. 37Ndipo uzipangira nsalu yotsekerayo nsanamira zisanu za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide; zokowera zao zikhale zagolide; nuziyengera makamwa asanu amkuwa.

Currently Selected:

EKSODO 26: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in