YouVersion Logo
Search Icon

EKSODO 25

25
Zopereka zaufulu zakumanga Malo Opatulika
1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, 2#1Mbi. 29.9; Ezr. 2.68; 2Ako. 8.12; 2Ako. 9.7Lankhula ndi ana a Israele, kuti anditengere chopereka; ulandire chopereka changa kwa munthu aliyense mtima wake umfunitsa mwini. 3Ndipo choperekacho uchilandire kwa iwo ndi ichi: golide, ndi siliva, ndi mkuwa, 4ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi; 5ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wakasiya; 6mafuta akuunikira, zonunkhira za mafuta odzoza, ndi za chofukiza cha fungo lokoma; 7miyala yaberulo, ndi miyala yoika paefodi, ndi pachapachifuwa. 8#Chiv. 21.3Ndipo andimangire malo opatulika; kuti ndikhale pakati pao. 9Monga mwa zonse Ine ndilikuonetsa iwe, chifaniziro cha Kachisi, ndi chifaniziro cha zipangizo zake zonse, momwemo uchimange.
Za likasa, chotetezerapo, ndi akerubi
10Ndipo azipanga likasa la mtengo wakasiya: utali wake mikono iwiri ndi hafu, kupingasa kwake mkono ndi hafu, msinkhu wake mkono ndi hafu. 11Ndipo ulikute ndi golide woona, ulikute m'kati ndi kubwalo, nulipangire mkombero wagolide pozungulira pake. 12Ndipo uliyengere mphete zinai zagolide, ndi kuziika kumiyendo yake inai; mphete ziwiri pa mbali yake ina, ndi mphete ziwiri pa ina. 13#Aheb. 9.4Ndipo uzipanga mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide. 14Nupise mphiko m'mphetezo pa mbali zake za likasa, zakunyamulira nazo likasalo. 15Mphiko zikhale m'zimphete za likasa; asazisolole. 16Ndipo uziika m'likasamo mboni imene ndidzakupatsa. 17#Aheb. 9.5Ndipo uzipanga chotetezerapo cha golide woona; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu. 18Uzipanganso akerubi awiri agolide; uwasule mapangidwe ake, pa mathungo ake awiri a chotetezerapo. 19#Aheb. 9.5Nupange kerubi mmodzi ku thungo lino, ndi kerubi wina ku thungo lina; upange akerubi ochokera kuchotetezerapo, pa mathungo ake awiri. 20Ndipo akerubi afunyululire mapiko ao m'mwamba, ndi kuphimba chotetezerapo ndi mapiko ao, ndi nkhope zao zipenyane; nkhope za akerubi zipenye kuchotetezerapo. 21#Aheb. 9.4-5Ndipo uziika chotetezerapo pamwamba pa likasa, ndi kuikamo mboni ndidzakupatsayo m'likasamo. 22#Num. 7.89Ndipo pomwepo ndidzakomana ndi iwe, ndi kulankhula ndi iwe, ndili pamwamba pa chotetezerapo, pakati pa akerubi awiriwo okhala pa likasa la mboni, zonse zimene ndidzakuuza za ana a Israele.
Za gome la mkate woonekera
23Ndipo uzipanga gome la mtengo wakasiya; utali wake mikono iwiri, ndi kupingasa kwake mkono umodzi, ndi msinkhu wake mkono ndi hafu. 24Ndipo ulikute ndi golide woona ndi kulipangira mkombero wagolide pozungulira pake. 25Nulipangire mitanda pozungulirapo yoyesa chikhato m'kupingasa kwake, ndi pamitanda pake pozungulira upangirepo mkombero wagolide. 26Nulipangire mphete zinai zagolide, ndi kuika mphetezo pangodya zinai zokhala pa miyendo yake inai. 27Mphetezo zikhale pafupi pa mitanda, zikhale zopisamo mphiko za kunyamulira nazo gome. 28Ndipo uzipanga mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide, kuti anyamulire nazo gome. 29Ndipo uzipanga mbale zake, ndi zipande zake, ndi mitsuko yake, ndi zikho zake zakuthira nazo; uzipanga za golide woona. 30Ndipo uziika mkate woonekera pa gomelo pamaso panga nthawi zonse.
Za choikapo nyali
31 # Chiv. 1.12, 13 Ndipo uzipanga choikapo nyali cha golide woona; choikapocho chisulidwe mapangidwe ake, tsinde lake ndi thupi lake; zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zikhale zochokera m'mwemo; 32ndipo m'mbali zake mutuluke mphanda zisanu ndi imodzi; mphanda zitatu za choikapo nyalicho zituluke m'mbali yake ina, ndi mphanda zitatu za choikapo nyalicho zituluke m'mbali inzake. 33Ku mphanda ina kukhale zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; ndi ku mphanda inzake zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; zitere mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikapo nyalicho. 34Ndipo pa choikapo nyali chomwe pakhale zikho zinai zopangika ngati katungurume, mitu yake ndi maluwa ake; 35pakhale mutu pansi pa mphanda ziwiri zotuluka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri zotuluka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri zotuluka m'mwemo; itere ku mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikapo nyalicho. 36Mitu yao ndi mphanda zao zikhale zotuluka m'mwemo; chonsechi chikhale chosulika chimodzi cha golide woona. 37Ndipo uzipanga nyali zake, zisanu ndi ziwiri; ndipo ayatse nyali zake, ziwale pandunji pake. 38Ndipo mbano zake, ndi zoolera zake, zikhale za golide woona. 39Achipange ichi ndi zipangizo izi zonse za talente wa golide woona. 40#Aheb. 8.5Ndipo uyang'anire uzipanga monga mwachifaniziro chao, chimene anakuonetsa m'phirimo.

Currently Selected:

EKSODO 25: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in