Ndipo uuze ana a Israele akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti awalitse nyali kosalekeza. Aroni ndi ana ake aikonze m'chihema chokomanako, kunja kwa nsalu yotchinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israele.