YouVersion Logo
Search Icon

EKSODO 28

28
Za zovala zopatulika
1Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ake amuna pamodzi naye, mwa ana a Israele, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni. 2Ndipo usokere Aroni mbale wako zovala zopatulika, zikhale zaulemerero ndi zokoma. 3Ndipo ulankhule ndi onse a mtima waluso, amene ndawadzaza ndi mzimu waluso, kuti amsokere Aroni zovala apatulidwe nazo, andichitire Ine ntchito ya nsembe. 4Ndipo zovala azisoka ndizi: chapachifuwa ndi efodi, ndi mwinjiro, ndi malaya opikapika, ndi nduwira, ndi mpango; tero apangire Aroni mbale wako ndi ana ake zovala zopatulika, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe. 5Ndipo atenge golide, ndi lamadzi ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
Za Efodi
6Naombe efodi ndi golide, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya mmisiri. 7Akhale nazo zapamapewa ziwiri zomangika ku nsonga zake ziwiri, kuti amangike nazo. 8Ndipo mpango wa efodi, wokhala pamenepo, kuti ammange nao, ukhale wa chiombedwe chomwecho, ndi woombera kumodzi, wagolide, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. 9Ndipo utenge miyala iwiri yaberulo, nulochepo maina a ana a Israele; 10maina asanu ndi limodzi pa mwala wina, ndi maina asanu ndi limodzi otsala pa mwala unzake, mwa kubadwa kwao. 11Uloche miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israele, monga mwa ntchito ya wolocha miyala, monga malembedwe a chosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolide. 12Ndipo uiike miyala iwiriyo pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya chikumbutso cha ana a Israele; ndipo Aroni azinyamula maina ao pa mapewa ake awiri, akhale chikumbutso pamaso pa Yehova.
13Ndipo upange zoikamo za golide; 14ndi maunyolo awiri a golide woona; uwapote ngati zingwe, ntchito yopota; numange maunyolo opotawo pazoikamo. 15Upangenso chapachifuwa cha chiweruzo, ntchito ya mmisiri; uchiombe mwa chiombedwe cha efodi; uchiombe ndi golide, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. 16Chikhale chaphwamphwa, chopindika, utali wake dzanja limodzi, ndi kupingasa kwake dzanja limodzi. 17#Chiv. 21.19-20Ndipo uikepo miyala yoikikapo, mizere inai ya miyala; mzere wa odemu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba; 18ndi mzere wachiwiri wa nofeki, safiro, ndi yahaloni; 19ndi mizere wachitatu wa lesemu, sibu, ndi akalama; 20ndi mzere wachinai wa tarisisi, sohamu, ndi yasefe; zikhale zogwirika ndi golide m'zoikamo zao. 21Ndi miyalayi ikhale monga mwa maina a ana a Israele, khumi ndi awiri, monga maina ao; monga malochedwe a chosindikizira, yonse ikhale monga maina ao, kwa mafuko khumi ndi awiri. 22Upangenso maunyolo pa chapachifuwa ngati zingwe, ntchito yopota, ya golide woona. 23Nupangire pa chapachifuwa mphete ziwiri zagolide, ndi kuzika mphete ziwirizo pa nsonga zake ziwiri za chapachifuwa. 24Numange maunyolo awiri opota agolide ku mphete ziwirizo pa nsonga pake pa chapachifuwa. 25Koma nsonga zake ziwiri za maunyolo opotawo uzimange ku zoikamo ziwiri, ndi kuziika pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'tsogolo mwake. 26Ndipo upange mphete ziwiri zagolide, ndi kuzimanga pa nsonga zake ziwiri za chapachifuwa, m'mphepete mwake, m'katimo ku mbali ya kuefodi. 27Upangenso mphete ziwiri zagolide, ndi kuzimanga pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'munsi, ku mbali yake ya kutsogolo, pafupi pa msoko wake, pamwamba pa mpango wa efodi. 28Ndipo amange chapachifuwa pa mphete zake ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti chikhale pa mpango wa efodi; ndi kuti chapachifuwa chisamasuke paefodi. 29Ndipo Aroni azinyamula maina a ana a Israele pa chapachifuwa cha chiweruzo pamtima pake, pakulowa iye m'malo opatulika, akhale chikumbutso pankhope pa Yehova kosalekeza. 30Ndipo uike Urimu ndi Tumimu mwa chapachifuwa cha chiweruzo; ndipo zikhale pa mtima wa Aroni, pakulowa iye pamaso pa Yehova; ndipo Aroni azinyamula chiweruzo cha ana a Israele pamtima pake pamaso pa Yehova kosalekeza.
31Ndipo uombe mwinjiro wa efodi ndi lamadzi lokha. 32Ndipo polowa mutu pakhale pakati pake; pakhale mkawo pozungulira polowa pake, wa ntchito yoomba, ngati polowa pa malaya otchinjiriza, pangang'ambike. 33Ndipo pa mbinyiru wake upange makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, pambinyiru pake pozungulira, ndi kuwapakiza ndi miliu yagolide pozungulira; 34mliu wa golide ndi khangaza, mliu wagolide ndi khangaza, pa mbinyiru wa mwinjiro pozungulira. 35Ndipo Aroni auvale kuti atumikire nao; ndipo limveke liu lake pakulowa iye m'malo opatulika pamaso pa Yehova, ndi pakutuluka iye, kuti asafe.
Za golide waphanthiphanthi
36 # Eks. 39.30; Zek. 14.20 Ndipo upange golide waphanthiphanthi woona, ndi kulochapo, monga malochedwe a chosindikizira, Kupatulikira Yehova. 37Nuchiike pamkuzi wamadzi, ndipo chikhale panduwira, chikhale patsogolo pake pa nduwira. 38#Ezk. 4.4-6; Aheb. 9.28Ndipo chizikhala pamphumi pake pa Aroni, ndipo Aroni azinyamula mphulupulu ya zopatulidwa, zimene ana a Israele azipatulira, ndi zopereka zao zonse zopatulira; ndipo chizikhala pamphumi pake kosalekeza, kuti alandiridwe pamaso pa Yehova. 39Ndipo upikule malaya am'kati abafuta a thonje losansitsa, nusoke nduwira wabafuta, nusokenso mpango wopikapika. 40Ndipo usokere ana a Aroni malaya am'kati, nuwasokere mipango; uwasokerenso akapa akhale aulemerero ndi okoma. 41#Lev. 21.10; Aheb. 7.28Ndipo uveke nazo Aroni mbale wako, ndi ana ake omwe; ndi kuwadzoza, ndi kudzaza dzanja lao, ndi kuwapatula, andichitire Ine ntchito ya nsembe. 42Uwasokerenso zovala za miyendo za bafuta wa thonje losansitsa kubisa maliseche ao; ziyambire m'chuuno zifikire kuntchafu. 43Ndipo azivale Aroni ndi ana ake, pakulowa iwo ku chihema chokomanako, kapena poyandikiza iwo kuguwa la nsembe kutumikira m'malo opatulika; anganyamule mphulupulu, nangafe; likhale lemba losatha la iye ndi mbumba zake pambuyo pake.

Currently Selected:

EKSODO 28: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in