EKSODO 29
29
Mapatulidwe a ansembe
1Ichi ndicho uwachitire kuwapatula, andichitire ntchito ya nsembe: tenga ng'ombe yamphongo, ndi nkhosa ziwiri zamphongo zangwiro, 2ndi mkate wopanda chotupitsa, ndi timitanda topanda chotupitsa tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa, todzoza ndi mafuta; utipange ndi ufa wosalala watirigu. 3Ndipo uziike mu dengu limodzi, ndi kubwera nazo mudengu, pamodzi ndi ng'ombe yamphongo ndi nkhosa ziwiri zamphongo. 4Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ake amuna ku khomo la chihema chokomanako, ndi kuwasambitsa m'madzi. 5Pamenepo utenge zovalazo ndi kuveka Aroni malaya am'kati, ndi mwinjiro wa efodi, ndi efodi, ndi chapachifuwa, ndi kummangira m'chuuno ndi mpango wa efodi woluka mwanzeru; 6ndipo uike nduwira pamutu pake, ndi kuika korona wopatulika panduwirapo. 7Pamenepo utenge mafuta odzoza nao nuwatsanulire pamutu pake, ndi kumdzoza. 8Ndipo ubwere nao ana ake amuna ndi kuwaveka malaya am'kati. 9Uwamangirenso Aroni ndi ana ake amuna mipango m'chuuno mwao, nuwamangire akapa pamutu pao; ndipo akhale ansembe mwa lemba losatha; nudzaze dzanja la Aroni ndi dzanja la ana ake amuna. 10Ndipo ubwere nayo ng'ombe yamphongo patsogolo pa chihema chokomanako; ndipo Aroni ndi ana ake amuna aike manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo. 11Nuphe ng'ombe yamphongoyo pamaso pa Yehova, pa khomo la chihema chokomanako. 12Pamenepo utapeko pa mwazi wa ng'ombe yamphongo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe ndi chala chako, nutsanulire mwazi wonse pa tsinde la guwa la nsembe. 13Nutenge mafuta onse akukuta matumbo, ndi chokuta cha mphafa ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pa izo, ndi kuzitentha pa guwa la nsembe. 14#Aheb. 13.11-12Koma nyama ya ng'ombeyo, ndi chikopa chake, ndi chipwidza chake, uzitentha izi ndi moto kunja kwa chigono; ndiyo nsembe yauchimo. 15Utengenso nkhosa yamphongo imodziyo; ndi Aroni ndi ana ake amuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo. 16#Aheb. 9.19Nuiphe nkhosa yamphongoyo, ndi kutenga mwazi wake, ndi kuuwaza pa guwa la nsembe pozungulira. 17Ndipo upadzule nkhosa yamphongo m'ziwalo zake, ndi kutsuka matumbo ake, ndi miyendo yake, ndi kuziika pa ziwalo zake, ndi pamutu pake. 18#Gen. 8.21Pamenepo upsereze nkhosa yamphongo yonse pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza ya Yehova, ya fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova. 19Ndipo utenge nkhosa yamphongo yinayo; ndi Aroni ndi ana ake amuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo. 20Pamenepo uiphe nkhosa yamphongoyo, nutapeko pa mwazi wake, ndi kuupaka pa ndewerere ya khutu lamanja la Aroni, ndi pa ndewerere ya khutu lamanja ana ake amuna, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lao lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lao lamanja ndi kuuwaza mwaziwo pa guwa la nsembe posungulira. 21Ndipo utapeko pamwazi uli pa guwa la nsembe, ndi pa mafuta akudzoza nao, ndi kuwaza pa Aroni, ndi pa zovala zake, ndi pa ana ake amuna, ndi pa zovala za ana ake amuna, pamodzi ndi iye; kuti akhale wopatulidwa, ndi zovala zake zomwe, ndi ana ake amuna ndi zovala zao zomwe pamodzi ndi iye. 22Utengenso mafuta a nkhosa yamphongoyo, ndi mchira, chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pamenepo, ndi mwendo wam'mwamba wa ku dzanja lamanja; pakuti ndiyo nkhosa yamphongo ya kudzaza manja; 23ndi mkate wamphumphu umodzi, ndi kamtanda ka mkate wosanganiza ndi mafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, zili mu dengu la mkate wopanda chotupitsa wokhala pamaso pa Yehova; 24ndipo uike zonsezi m'manja a Aroni, ndi m'manja a ana ake amuna; nuziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova. 25#Eks. 29.18, 41Pamenepo uzilandire m'manja mwao, ndi kuzipsereza pa guwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, zichite fungo lokoma pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova. 26Ndipo utenge nganga ya nkhosa yamphongo yodzaza manja ya Aroni, ndi kuiweyula ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo ikhale gawo lako. 27Ndipo upatule nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wam'mwamba wa nsembe yokweza, imene anaiweyula, ndi imene anaikweza, za nkhosa yamphongo yakudzaza manja; zili za Aroni, ndi za ana ake amuna; 28ndipo zikhale za Aroni ndi za ana ake amuna, mwa lemba losatha, ziwadzere kwa ana a Israele; popeza ndiyo nsembe yokweza; ndipo ikhale nsembe yokweza yodzera kwa ana a Israele, ya kwa nsembe zamtendere zao, ndiyo nsembe yao yokweza ya Yehova. 29Ndipo zovala zopatulika za Aroni zikhale za ana ake amuna pambuyo pake, kuti awadzoze atazivala, nadzaze manja ao atazivala; 30mwana wake wamwamuna amene adzakhala wansembe m'malo mwake azivala masiku asanu ndi awiri, pakulowa iye m'chihema chokomanako kutumikira m'malo opatulika. 31Ndipo utenge nkhosa yamphongo yodzaza manja, nuphike nyama yake m'malo opatulika. 32Ndipo Aroni ndi ana ake amuna adye nyama ya nkhosa yamphongoyo, ndi mkate uli mudengu, pa khomo la chihema chokomanako. 33Ndipo adye zimene anachita nazo choteteza, kuti awadzaze manja ndi kuwapatulitsa; koma mlendo asadyeko, pakuti nzopatulika izi. 34Ndipo ikatsalako nyama yodzaza manja, kapena mkate kufikira m'mawa, pamenepo utenthe zotsalazo ndi moto; asazidye popeza nchopatulika ichi. 35Ndipo utero nao Aroni, ndi ana ake amuna, monga mwa zonse ndakuuza; udzaze manja ao masiku asanu ndi awiri. 36Nukonze ng'ombe yamphongo, ndiyo nsembe yauchimo yakuteteza nayo, tsiku ndi tsiku; ndipo uyeretsa guwa la nsembe, pakuchita choteteza pamenepo; ndipo ulidzoze kulipatula. 37#Mat. 23.19Uchitire guwa la nsembe choteteza masiku asanu ndi awiri ndi kulipatula; ndipo guwa la nsembelo likhale lopatulika kwambiri; chilichonse chikhudza guwa la nsembelo chikhale chopatulika.
Nsembe ya masiku onse
38Koma izi ndizo uzikonza pa guwa la nsembelo; anaankhosa awiri a chaka chimodzi, tsiku ndi tsiku kosalekeza. 39Mwanawankhosa wina ukonze m'mawa; ndi mwanawankhosa wina ukonze madzulo; 40ndi pa mwanawankhosa mmodziyo pakhale limodzi la magawo khumi la ufa wosalala, wosanganiza ndi limodzi la magawo anai la hini wa mafuta opera; ndi limodzi la magawo anai la hini wa vinyo, likhale nsembe yothira. 41Ndi mwanawankhosa wina ukonze madzulo; umkonze umo unachitira nsembe yaufa cha m'mawa ndi nsembe yake yothira, akhale fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova. 42Ikhale nsembe yopsereza yosalekeza ya mwa mibadwo yanu, pa khomo la chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kumene ndidzakomana nanu, kulankhula nawe komweko. 43Ndipo pamenepo ndidzakomana ndi ana a Israele; ndipo chihema chidzapatulidwa ndi ulemerero wanga. 44Ndipo ndidzapatula chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; ndidzapatulanso Aroni ndi ana ake amuna omwe, andichitire ntchito ya nsembe. 45#Eks. 25.8; Zek. 2.10; Chiv. 21.3Ndipo ndidzakhala pakati pa ana a Israele, ndi kukhala Mulungu wao. 46Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, amene ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito, kuti ndikhale pakati pao. Ine ndine Yehova Mulungu wao.
Currently Selected:
EKSODO 29: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
![None](/_next/image?url=https%3A%2F%2Fimageproxy.youversionapi.com%2F58%2Fhttps%3A%2F%2Fweb-assets.youversion.com%2Fapp-icons%2Fen.png&w=128&q=75)
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi