DEUTERONOMO 34
34
1Ndipo Mose anakwera kuchokera ku zidikha za Mowabu, kunka kuphiri la Nebo, pamwamba pa Pisiga, popenyana ndi Yeriko. Ndipo Yehova anamuonetsa dziko lonse la Giliyadi, kufikira ku Dani; 2ndi Nafutali lonse, ndi dziko la Efuremu, ndi Manase, ndi dziko lonse la Yuda, kufikira nyanja ya m'tsogolo; 3ndi kumwera, ndi chidikha cha chigwa cha Yeriko, mudzi wa migwalangwa, kufikira ku Zowari. 4#Gen. 12.7Ndipo Yehova anati kwa iye, Si ili dziko ndinalumbirira Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzalipereka kwa mbeu zako. Ndinakuonetsa ili m'maso, koma sudzaolokako. 5Ndipo Mose mtumiki wa Yehova anamwalirako m'dziko la Mowabu, monga mwa mau a Yehova. 6#Yud. 9Ndipo Iye anamuika m'chigwa m'dziko la Mowabu popenyana ndi Betepeori; koma palibe munthu wakudziwa kumanda kwake kufikira lero lino. 7#Yos. 14.11Ndipo zaka zake za Mose ndizo zana limodzi ndi makumi awiri, pakumwalira iye; diso lake silinachita mdima, ndi mphamvu yake siidaleka. 8Ndipo ana a Israele analira Mose m'zidikha za Mowabu masiku makumi atatu; potero anatha masiku akulira maliro a Mose. 9Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anadzala ndi mzimu wanzeru; popeza Mose adamuikira manja ake; ndi ana a Israele anamvera iye, nachita monga Yehova adauza Mose. 10#Eks. 33.11Ndipo sanaukenso mneneri m'Israele ngati Mose, amene Yehova anadziwana naye popenyana maso; 11kunena za zizindikiro ndi zozizwa zonse zimene Yehova anamtumiza kuzichita m'dziko la Ejipito kwa Farao, ndi anyamata ake onse, ndi dziko lake lonse; 12ndi kunena za dzanja la mphamvu lonse, ndi choopsa chachikulu chonse, chimene Mose anachita pamaso pa Israele wonse.
Currently Selected:
DEUTERONOMO 34: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi