YouVersion Logo
Search Icon

DEUTERONOMO 33

33
Mose adalitsa mafuko 12 a Israele asanafe
1Ndipo mdalitso, Mose munthu wa Mulungu anadalitsa nao ana a Israele asanafe, ndi uwu. 2Ndipo anati,
Yehova anafuma ku Sinai,
nawatulukira ku Seiri;
anaoneka wowala pa phiri la Parani,
anafumira kwa opatulika zikwizikwi;
ku dzanja lamanja lake kudawakhalira lamulo lamoto.
3 # Mas. 50.5; Hos. 11.1 Inde akonda mitundu ya anthu;
opatulidwa ake onse ali m'dzanja mwanu;
ndipo akhala pansi ku mapazi anu;
yense adzalandirako mau anu.
4Mose anatiuza chilamulo,
cholowa cha msonkhano wa Yakobo.
5Ndipo Iye anali mfumu m'Yesuruni,
pakusonkhana mafumu a anthu,
pamodzi ndi mafuko a Israele.
6Rubeni akhale ndi moyo, asafe,
koma amuna ake akhale owerengeka.
7 # Gen. 49.8 Za Yuda ndi izi; ndipo anati,
Imvani, Yehova, mau a Yuda,
ndipo mumfikitse kwa anthu ake;
manja ake amfikire;
ndipo mukhale inu thandizo lake pa iwo akumuukira.
8Ndipo za Levi anati,
Tumimu ndi Urimu wanu zikhala ndi wokondedwa wanu,
amene mudamuyesa m'Masa,
amene mudalimbana naye ku madzi a Meriba;
9amene anati za atate wake ndi amai wake,
sindinamuone; Sanazindikire abale ake,
sanadziwe ana ake omwe;
popeza anasamalira mau anu,
nasunga chipangano chanu.
10 # Lev. 10.11 Adzaphunzitsa Yakobo maweruzo anu,
ndi Israele chilamulo chanu;
adzaika chofukiza pamaso panu,
ndi nsembe yopsereza yamphumphu pa guwa la nsembe lanu.
11 # Ezk. 20.40-41 Dalitsani, Yehova, mphamvu yake,
nimulandire ntchito ya manja ake;
akantheni m'chuuno iwo akumuukira,
ndi iwo akumuda, kuti asaukenso.
12Za Benjamini anati,
Wokondedwa wa Yehova adzakhala ndi Iye mokhazikika;
am'phimba tsiku lonse,
inde akhalitsa pakati pa mapewa ake.
13 # Gen. 49.22-25 Ndipo za Yosefe anati,
Yehova adalitse dziko lake;
ndi zinthu zofunikatu za m'mwamba, ndi mame,
ndi madzi okhala pansipo;
14ndi zipatso zofunikatu za dzuwa,
ndi zomera zofunikatu za mwezi,
15ndi zinthu zoposa za mapiri akale,
ndi zinthu zofunikatu za zitunda zosatha,
16 # Eks. 3.2-4 ndi zinthu zofunikatu za dziko lapansi, ndi kudzala kwake,
ndi chivomerezo cha Iye anakhala m'chitsambayo.
Mdalitso ufike pa mutu wa Yosefe,
ndi pakati pa mutu wake wa iye wokhala padera ndi abale ake.
17 # 1Maf. 22.11 Woyamba kubadwa wa ng'ombe yake,
ulemerero ndi wake;
nyanga zake ndizo nyanga zanjati;
adzatunga nazo mitundu ya anthu pamodzi,
kufikira malekezero a dziko lapansi.
Iwo ndiwo zikwi khumi za Efuremu,
iwo ndiwo zikwi za Manase.
18 # Gen. 49.13 Ndi za Zebuloni anati,
Kondwera, Zebuloni, ndi kutuluka kwako;
ndi Isakara, m'mahema mwako.
19Adzaitana mitundu ya anthu afike kuphiri;
apo adzaphera nsembe za chilungamo;
popeza adzayamwa zochuluka za m'nyanja,
ndi chuma chobisika mumchenga.
20 # Gen. 49.19 Ndi za Gadi anati,
Wodala iye amene akuza Gadi;
akhala ngati mkango waukazi,
namwetula dzanja, ndi pakati pa mutu pomwe.
21 # Yos. 1.12-15 Ndipo anadzisankhira gawo loyamba,
popeza kumeneko kudasungika gawo la wolamulira;
ndipo anadza ndi mafumu a anthu,
anachita chilungamo cha Yehova,
ndi maweruzo ake ndi Israele.
22 # Yos. 19.47 Ndi za Dani anati,
Dani ndiye mwana wa mkango,
wakutumpha motuluka m'Basani.
23 # Gen. 49.21 Za Nafutali anati,
Nafutali, wokhuta nazo zomkondweretsa,
wodzala ndi mdalitso wa Yehova;
landira kumadzulo ndi kumwera.
24 # Gen. 49.20; Yob. 29.6 Ndi za Asere anati,
Asere adalitsidwe mwa anawo;
akhale wovomerezeka mwa abale ake,
aviike phazi lake m'mafuta.
25Nsapato zako zikhale za chitsulo ndi mkuwa;
ndipo monga masiku ako momwemo mphamvu yako.
26 # Eks. 15.11 Palibe wina ngati Mulungu, Yesuruni iwe,
wakuyenda wokwera pathambo, kukuthandiza,
ndi pa mitambo m'ukulu wake.
27 # Mas. 90.1 Mulungu wamuyaya ndiye mokhaliramo mwako;
ndi pansipo pali manja osatha.
Ndipo aingitsa mdani pamaso pako,
nati, Ononga.
28Ndipo Israele akhala mokhazikika pa yekha;
kasupe wa Yakobo;
akhala m'dziko la tirigu ndi vinyo;
inde thambo lake likukha mame.
29 # 2Sam. 7.23; Mas. 144.15 Wodala iwe, Israele;
akunga iwe ndani, mtundu wa anthu opulumutsidwa ndi Yehova,
ndiye chikopa cha thandizo lako,
Iye amene akhala lupanga la ukulu wako!
Ndi adani ako adzakugonjera;
ndipo udzaponda pa misanje yao.

Currently Selected:

DEUTERONOMO 33: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in