DEUTERONOMO 32
32
Nyimbo adailemba Mose
1Kumwamba kutchere khutu,
ndipo ndidzanena;
ndi dziko lapansi limve mau a m'kamwa mwanga.
2Chiphunzitso changa chikhale ngati mvula;
maneno anga agwe ngati mame;
ngati mvula yowaza pamsipu,
ndi monga madontho a mvula pazitsamba.
3 #
1Mbi. 29.11
Pakuti ndidzalalika dzina la Yehova.
Nenani kuti Mulungu wathu ndi wamkulu.
4 #
Mas. 18.2, 30; Yer. 10.10 Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro;
pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo;
Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo;
Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.
5 #
Mat. 17.17
Anamchitira zovunda si ndiwo ana ake, chilema nchao;
iwo ndiwo mbadwo wopulukira ndi wokhotakhota.
6 #
Mas. 116.12; Yes. 44.2 Kodi mubwezera Yehova chotero,
anthu inu opusa ndi opanda nzeru?
Kodi si ndiye Atate wanu, Mbuye wanu;
anakulengani, nakukhazikitsani?
7Kumbukirani masiku akale,
zindikirani zaka za mibadwo yambiri;
funsani atate wanu, adzakufotokozerani;
akulu anu, adzakuuzani.
8 #
Mac. 17.26
Pamene Wam'mwambamwamba anagawira amitundu cholowa chao,
pamene anagawa ana a anthu,
anaika malire a mitundu ya anthu,
monga mwa kuwerenga kwao kwa ana a Israele.
9 #
Mas. 78.71
Pakuti gawo la Yehova ndilo anthu ake;
Yakobo ndiye muyeso wa cholowa chake.
10 #
Mas. 17.8
Anampeza m'dziko la mabwinja,
m'chipululu cholira chopanda kanthu;
anamzinga, anamlangiza,
anamsunga ngati kamwana ka m'diso.
11 #
Eks. 19.4
Monga mphungu ikasula chisa chake,
nikapakapa pa ana ake,
Iye anayala mapiko ake, nawalandira,
nawanyamula pa mapiko ake.
12Yehova yekha anamtsogolera,
ndipo palibe mulungu wachilendo naye.
13 #
Mas. 81.16
Anamuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi,
ndipo anadya zipatso za m'minda;
namyamwitsa uchi wa m'thanthwe,
ndi mafuta m'mwala wansangalabwe;
14mafuta a mkaka wang'ombe, ndi mkaka wankhosa,
ndi mafuta a anaankhosa,
ndi nkhosa zamphongo za mtundu wa ku Basani, ndi atonde,
ndi impso zonenepa zatirigu;
ndipo munamwa vinyo, mwazi wamphesa.
15 #
Deut. 31.20; Mas. 89.26 Koma Yesuruni anasanduka wonenepa, natazira;
wasanduka wonenepa, wakula, wakuta ndi mafuta;
pamenepo anasiya Mulungu amene anamlenga,
napeputsa thanthwe la chipulumutso chake.
16 #
1Maf. 14.22; 1Ako. 10.22 Anamchititsa nsanje ndi milungu yachilendo,
anautsa mkwiyo wake ndi zonyansa.
17 #
1Ako. 10.20
Anaziphera nsembe ziwanda, si ndizo Mulungu ai;
milungu yosadziwa iwo,
yatsopano yofuma pafupi,
imene makolo anu sanaiope.
18Mwaleka Thanthwe limene linakubalani,
mwaiwala Mulungu amene anakulengani.
19Ndipo Yehova anachiona, nawanyoza,
pakuipidwa nao ana ake amuna, ndi akazi.
20 #
Deut. 31.17
Ndipo Iye anati, Ndidzawabisira nkhope yanga,
ndidzaona kutsiriza kwao;
popeza iwo ndiwo mbadwo wopulukira,
ana osakhulupirika iwo.
21 #
Deut. 32.16; Aro. 10.19 Anautsa nsanje yanga ndi chinthu chosati Mulungu;
anautsa mkwiyo wanga ndi zopanda pake zao.
Ndidzautsa nsanje yao ndi iwo osakhala mtundu wa anthu;
ndidzautsa mkwiyo wao ndi mtundu wa anthu opusa.
22 #
Yer. 15.14
Pakuti wayaka moto mu mkwiyo wanga,
utentha kumanda kunsi
ukutha dziko lapansi ndi zipatso zake,
nuyatsa maziko a mapiri.
23Ndidzawaunjikira zoipa;
ndidzawathera mivi yanga.
24 #
Lev. 26.22
Adzaonda nayo njala
adzanyekeka ndi makala a moto, chionongeko chowawa;
ndipo ndidzawatumizira mano a zilombo,
ndi ululu wa zokwawa m'fumbi.
25 #
Ezk. 7.15; 2Ako. 7.5 Pabwalo lupanga lidzalanda,
ndi m'zipinda mantha;
lidzaononga mnyamata ndi namwali,
woyamwa pamodzi ndi munthu waimvi.
26Ndinati, Ndikadawauzira ndithu,
ndikadafafaniza chikumbukiro chao mwa anthu.
27Ndikadapanda kuopa mkwiyo wa pa mdani,
angayese molakwa outsana nao,
anganene, Lakwezeka dzanja lathu,
ndipo Yehova sanachite ichi chonse.
28Popeza iwo ndiwo mtundu wa anthu wosowa uphungu konse,
ndipo alibe chidziwitso.
29 #
Mas. 81.13; Luk. 19.42 Akadakhala nazo nzeru, akadazindikira ichi,
akadasamalira chitsirizo chao!
30 #
Yos. 23.10; Yes. 30.17 Mmodzi akadapirikitsa zikwi,
awiri akadathawitsa zikwi khumi,
akadapanda kuwagulitsa Thanthwe lao,
akadapanda kuwapereka Yehova.
31 #
1Sam. 2.2
Popeza thanthwe lao nlosanga Thanthwe lathu,
oweruza a pamenepo ndiwo adani athu.
32Pakuti mpesa wao ndiwo wa ku Sodomu,
ndi wa m'minda ya ku Gomora;
mphesa zao ndizo mphesa zandulu,
matsangwi ao ngowawa.
33Vinyo wao ndiwo ululu wa zinjoka,
ndi ululu waukali wa mphiri.
34Kodi sichisungika ndi Ine,
cholembedwa chizindikiro mwa chuma changa chenicheni?
35 #
Mas. 94.1; Aro. 12.19 Kubwezera chilango nkwanga, kubwezera komwe,
pa nyengo ya kuterereka phazi lao;
pakuti tsiku la tsoka lao layandika,
ndi zinthu zowakonzeratu zifulumira kudza.
36 #
Aheb. 10.30
Popeza Yehova adzaweruza anthu ake,
nadzachitira nsoni anthu ake;
pakuona Iye kuti mphamvu yao yatha,
wosatsala womangika kapena waufulu.
37Pamenepo adzati, Ili kuti milungu yao,
thanthwe limene anathawirako?
38Imene inadya mafuta a nsembe zao zophera,
nimwa vinyo wa nsembe yao yothira?
Iuke nikuthandizeni, Ikhale pobisalapo panu.
39 #
Mas. 102.27; Yes. 41.4 Tapenyani tsopano kuti Ine ndine Iye,
ndipo palibe mulungu koma Ine;
ndipha Ine, ndikhalitsanso ndi moyo,
ndikantha, ndichizanso Ine;
ndipo palibe wakulanditsa m'dzanja langa.
40Pakuti ndikweza dzanja langa kuloza kumwamba,
ndipo nditi, Pali moyo wanga kosatha,
41ndikanola lupanga langa lonyezimira,
ndi dzanja langa likagwira chiweruzo;
ndidzabwezera chilango ondiukira,
ndi kulanga ondida.
42Mivi yanga ndiiledzeretsa nao mwazi,
ndi lupanga langa lidzalusira nyama;
ndi mwazi wa ophedwa ndi ogwidwa,
ndi mutu wachitsitsi wa mdani.
43 #
Chiv. 6.10; 19.2 Kondwerani, amitundu inu, ndi anthu ake;
adzalipsira mwazi wa atumiki ake,
adzabwezera chilango akumuukira,
nadzafafanizira zoipa dziko lake, ndi anthu ake.
44Ndipo anadza Mose nanena mau onse a nyimbo iyi m'makutu mwa anthu, iye, ndi Yoswa mwana wa Nuni. 45Ndipo Mose anatha kunena mau awa onse kwa Israele wonse; 46#Ezk. 40.4nati nao, Ikani mitima yanu pa mau onse ndikuchitirani nao mboni lero; kuti muuze ana anu asamalire kuwachita mau onse a chilamulo ichi. 47#Miy. 3.2; Aro. 10.5Pakuti sichikhala kwa inu chinthu chopanda pake, popeza ndicho moyo wanu, ndipo mwa chinthu ichi mudzachulukitsa masiku anu m'dziko limene muolokera Yordani, kulilandira.
Mulungu auza Mose akwere m'phiri la Nebo
48Ndipo Yehova ananena ndi Mose tsiku lomweli, ndi kuti, 49#Num. 27.12Kwera m'phiri muno mwa Abarimu, phiri la Nebo, lokhala m'dziko la Mowabu, popenyana ndi Yeriko; nupenye dziko la Kanani, limene ndipereka kwa ana a Israele likhale laolao; 50#Num. 20.28nufe m'phiri m'mene ukweramo, nuitanidwe kunka kwa anthu a mtundu wako; monga Aroni mbale wako anafa m'phiri la Hori, naitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake; 51popeza munandilakwira pakati pa ana a Israele ku madzi a Meriba wa Kadesi m'chipululu cha Zini, popeza simunandipatula Ine pakati pa ana a Israele. 52Pakuti udzapenya dzikoli pandunji pako; koma osalowako ku dziko limene ndipatsa ana a Israele.
Currently Selected:
DEUTERONOMO 32: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi