YouVersion Logo
Search Icon

DEUTERONOMO 31

31
Yoswa adzalowa m'malo a Mose
1Ndipo Mose anamuka nanena mau awa kwa Israele wonse, 2#Num. 27.13nati nao, Ndine munthu wa zaka zana ndi makumi awiri lero lino; sindikhozanso kutuluka ndi kulowa; ndipo Yehova anati kwa ine, Sudzaoloka Yordani uyu. 3Yehova Mulungu wanu ndiye adzaoloka pamaso panu, Iye ndiye adzaononga amitundu awo pamaso panu, ndipo mudzawalandira. Yoswa ndiye adzakutsogolerani pooloka, monga ananena Yehova. 4Ndipo Yehova adzawachitira monga anachitira Sihoni ndi Ogi, mafumu a Aamori, ndi dziko lao limene analiononga. 5Yehova akadzawapereka pamaso panu, muziwachitira monga mwa lamulo lonse ndakuuzani. 6#Yos. 1.6-7; Aheb. 13.5Khalani amphamvu, limbikani mitima, musamachita mantha, kapena kuopsedwa chifukwa cha iwowa; popeza Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu; Iye sadzakusowani, kapena kukusiyani. 7#Deut. 31.6Ndipo Mose anaitana Yoswa, nati naye pamaso pa Israele wonse, Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao anthu awa m'dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kuwapatsa ilo; ndipo iwe udzawalandiritsa ilo. 8#Deut. 31.6Ndipo Yehova, Iye ndiye amene akutsogolera; Iye adzakhala ndi iwe, Iye sadzakusowa kapena kukusiya; usamachita mantha, usamatenga nkhawa.
Pakutha zaka 7 zilizonse azilalikira chilamulocho
9Ndipo Mose analembera chilamulo ichi, nachipereka kwa ansembe, ana a Levi, akunyamula likasa la chipangano la Yehova, ndi kwa akulu onse a Israele. 10Ndipo Mose anawauza, ndi kuti, Pakutha pake pa zaka zisanu ndi ziwiri, pa nyengo yoikika ya m'chaka chakulekerera, pa chikondwerero cha Misasa; 11#Yos. 8.34-35pakufika Israele wonse kuoneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m'malo amene adzasankha, muzilalikira chilamulo ichi pamaso pa Israele wonse, m'makutu mwao. 12Sonkhanitsani anthu, amuna ndi akazi ndi ana ang'ono, ndi mlendo wokhala m'midzi mwanu, kuti amve, ndi kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, ndi kusamalira kuchita mau onse a chilamulo ichi; 13#Mas. 78.5-7ndi kuti ana ao osadziwa amve, naphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, masiku onse akukhala ndi moyo inu kudziko kumene muolokera Yordani kulilandira likhale lanulanu.
Yoswa asenza udindo wake
14 # Num. 27.18-19 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ayandikira masiku ako akuti uyenera kufa; kaitane Yoswa, nimuoneke m'chihema chokomanako, kuti ndimlangize. Namuka Mose ndi Yoswa, naoneka m'chihema chokomanako. 15Ndipo Yehova anaoneka m'chihema, m'mtambo njo; ndipo mtambo njo unaima pa khomo la chihema. 16Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, udzagona tulo ndi makolo ako; ndi anthu awa adzauka, nadzatsata ndi chigololo milungu yachilendo ya dziko limene analowa pakati pake, nadzanditaya Ine, ndi kuthyola chipangano changa ndinapangana naocho. 17#Ower. 6.13; Yes. 8.17; Ezk. 39.23Pamenepo ndidzawapsera mtima tsiku ilo, ndipo ndidzawataya, ndi kuwabisira nkhope yanga, ndipo adzathedwa, ndi zoipa ndi zovuta zambiri zidzawafikira; kotero kuti adzati tsiku lija, Sizitifikira kodi zoipa izi popeza Mulungu wathu sakhala pakati pa ife? 18Koma Ine ndidzabisatu nkhope yanga tsiku lija chifukwa cha zoipa zonse adazichita; popeza anadzitembenukira milungu ina. 19#Deut. 31.26Ndipo tsopano mudzilemberere nyimbo iyi, ndi kuphunzitsa ana a Israele iyi; muiike m'kamwa mwao, kuti nyimbo iyi indichitire mboni yotsutsa ana a Israele. 20#Hos. 13.6Pakuti nditakalowetsa awa m'dziko limene ndinalumbirira makolo ao, moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ndipo atadya nakhuta, nanenepa, pamenepo adzatembenukira milungu ina, ndi kuitumikira, ndi kundipeputsa Ine, ndi kuthyola chipangano changa. 21Ndipo kudzakhala, zitawafikira zoipa ndi zovuta zambiri, nyimbo iyi idzachita mboni pamaso pao; popeza siidzaiwalika m'kamwa mwa mbeu zao; popeza ndidziwa zolingirira zao azichita lero lino, ndisanawalowetse m'dziko limene ndinalumbira. 22Potero Mose analembera nyimboyi tsiku lomweli, naiphunzitsa ana a Israele. 23#Deut. 31.7-8Ndipo anauza Yoswa mwana wa Nuni, nati Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao ana a Israele m'dziko limene ndinawalumbirira; ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe.
24Ndipo kunali, Mose atatha kulembera mau a chilamulo ichi m'buku, kufikira atalembera onse, 25Mose anauza Alevi akunyamula likasa la chipangano la Yehova, ndi kuti, 26#2Maf. 22.8Landirani buku ili la chilamulo, nimuliike pambali pa likasa la chipangano la Yehova Mulungu wanu, likhale komweko mboni yakutsutsa inu. 27#Eks. 32.9Pakuti ndidziwa kupikisana kwanu, ndi kupulukira kwanu; taonani, pokhala ndikali ndi moyo pamodzi ndi inu lero, mwapikisana ndi Yehova; koposa kotani nanga nditamwalira ine! 28Ndisonkhanitsire akulu onse a mafuko anu, ndi akapitao anu, kuti ndinene mau awa m'makutu mwao, ndi kuchititsa mboni kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse iwo. 29#Ower. 2.19Pakuti ndidziwa kuti nditamwalira ine mudzadziipsa ndithu, ndi kupatuka m'njira imene ndinakuuzani; ndipo chidzakugwerani choipa masiku otsiriza; popeza mudzachita choipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake ndi ntchito za manja anu. 30Ndipo Mose ananena mau a nyimbo iyi m'makutu mwa msonkhano wonse wa Israele, kufikira adatha.

Currently Selected:

DEUTERONOMO 31: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in