YouVersion Logo
Search Icon

DEUTERONOMO 30

30
Mulungu alonjeza kuwalanditsa akalapa atachimwa
1Ndipo kudzakhala, zikakugwerani zonsezi, mdalitso ndi temberero, ndinaikazi pamaso panu, ndipo mukazikumbukira mumtima mwanu mwa amitundu onse, amene Yehova Mulungu wanu anakupirikitsiraniko; 2#Yow. 2.12-13nimukabwerera kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kumvera mau ake, monga mwa zonse ndikuuzani lero lino, inu ndi ana anu, ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse; 3#Yer. 29.14pamenepo Yehova Mulungu wanu adzauchotsa ukapolo wanu, ndi kukuchitirani chifundo; nadzabwera ndi kukumemezani mwa mitundu yonse ya anthu, kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsiraniko. 4Otayika anu akakhala ku malekezero a thambo, Yehova Mulungu wanu adzakumemezani kumeneko, nadzakutenganiko; 5ndipo Yehova Mulungu wanu adzakulowetsani m'dziko lidakhala laolao la makolo anu, nilidzakhala lanulanu; ndipo adzakuchitirani zokoma, ndi kukuchulukitsani koposa makolo anu. 6#Ezk. 11.19Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudulani mtima wanu, ndi mtima wa mbeu zanu, kuti mukonde Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, kuti mukhale ndi moyo. 7Ndipo Yehova Mulungu wanu adzaika matemberero awa onse pa adani anu, ndi iwo akukwiya ndi inu, amene anakulondolani. 8Pamenepo mutembenuke ndi kumvera mau a Yehova, ndi kuchita malamulo ake onse amene ndikuuzani lero lino. 9#Deut. 28.11Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakuchulukitsirani ntchito zonse za dzanja lanu, zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za zoweta zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, zikukomereni; popeza Yehova Mulungu wanu adzakondweranso kukuchitirani zokoma; monga anakondwera ndi makolo anu; 10ngati mudzamvera mau a Yehova Mulungu wanu, kuwasunga malamulo ake ndi malemba ake olembedwa m'buku la chilamulo ichi; ngati mudzabwerera kudza kwa Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse.
11 # Yes. 45.19 Pakuti lamulo ili ndikuuzani lero lino, silikukanikani kulizindikira, kapena silikhala kutali. 12#Aro. 10.6Silikhala m'mwamba, kuti mukati, Adzatikwerera m'mwamba ndani, ndi kubwera nalo kwa ife, ndi kutimvetsa ili, kuti tilichite? 13Ndipo silikhala tsidya la nyanja, kuti mukati, Adzatiolokera ndani tsidya la nyanja, ndi kutitengera ili, ndi kutimvetsa ili, kuti tilichite? 14Pakuti mauwa ali pafupifupi ndi inu, m'kamwa mwanu, ndi m'mtima mwanu, kuwachita.
15Tapenyani, ndaika pamaso panu lero lino moyo ndi zokoma, imfa ndi zoipa; 16popeza ndikuuzani lero kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake, ndi kusunga malamulo ake ndi malemba ake ndi maweruzo ake, kuti mukakhale ndi moyo ndi kuchuluka, ndi kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni m'dziko limene mulowako kulilandira. 17Koma mukatembenukira mtima wanu, osamvera inu, nimukacheteka, ndi kugwadira milungu ina ndi kuitumikira; 18ndikulalikirani inu lero, kuti mudzatayika ndithu, masiku anu sadzachuluka m'dziko limene muolokera Yordani kulowamo kulilandira. 19Ndichititsa mboni lero, kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse inu; ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbeu zanu; 20#Mas. 27.1; Yoh. 11.25kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mau ake, ndi kummamatira Iye, pakuti Iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka; kuti mukhale m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuwapatsa ili.

Currently Selected:

DEUTERONOMO 30: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in