DEUTERONOMO 29
29
Mulungu abwereza kupangana nao
1Awa ndi mau a chipangano chimene Yehova analamulira Mose achichite ndi ana a Israele m'dziko la Mowabu, pamodzi ndi chipanganocho anachita nao m'Horebu.
2Ndipo Mose anaitana Israele wonse, nati nao, Munapenya inu zonse zimene Yehova anachitira Farao, ndi anyamata ake onse, ndi dziko lake lonse, pamaso panu m'dziko la Ejipito; 3mayesero akuluwa maso anu anawapenya, zizindikirozo, ndi zozizwa zazikulu zija; 4#Yoh. 8.43; Yes. 6.9-10; Aef. 4.18koma Yehova sanakupatseni mtima wakudziwa, ndi maso akupenya, ndi makutu akumva, kufikira lero lino. 5Ndipo ndinakutsogolerani zaka makumi anai m'chipululu; zovala zanu sizinatha pathupi panu, ndi nsapato zanu sizinatha pa phazi lanu. 6#Eks. 16.12Simunadya mkate, simunamwa vinyo kapena chakumwa cholimba; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 7Ndipo pamene munafika pamalo pano, Sihoni mfumu ya Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basani, anatuluka kudzakomana nafe kunkhondo, ndipo tinawakantha; 8#Num. 32.33ndipo tinalanda dziko lao, ndi kulipereka likhale cholowa chao cha Arubeni, ndi Agadi, ndi fuko la hafu la Manase. 9Chifukwa chake sungani mau a chipangano ichi ndi kuwachita, kuti muchite mwanzeru m'zonse muzichita. 10Muimirira inu nonse lero lino pamaso pa Yehova Mulungu wanu; mafumu anu, mafuko anu, akulu anu, ndi akapitao anu, amuna onse a Israele, 11makanda anu, akazi anu, ndi mlendo wanu wakukhala pakati pa zigono zanu, kuyambira wotema nkhuni kufikira wotunga madzi; 12kuti mulowe chipangano cha Yehova Mulungu wanu, ndi lumbiriro lake, limene Yehova Mulungu wanu achita ndi inu lero lino; 13#Eks. 6.7kuti adzikhazikire inu, mtundu wake wa anthu lero lino, ndi kuti akhale kwa inu Mulungu, monga ananena ndi inu, ndi monga analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo. 14#Yer. 31.31-33; Mac. 2.39; Aheb. 8.7-8Koma sindichita chipangano ichi ndi lumbiro ili ndi inu nokha; 15komanso ndi iye wakuimirira pano nafe lero lino pamaso pa Yehova Mulungu wathu, ndiponso ndi iye wosakhala pano nafe lero lino. 16Pakuti mudziwa chikhalidwe chathu m'dziko la Ejipito, ndi kuti tinapyola pakati pa amitundu amene munawapyola; 17ndipo munapenya zonyansa zao, ndi mafano ao, mtengo ndi mwala, siliva ndi golide, zokhala pakati pao; 18#Aheb. 12.15kuti angakhale pakati pa inu mwamuna, kapena mkazi, kapena banja, kapena fuko, mtima wao watembenuka kusiyana naye Yehova Mulungu wathu lero lino, kuti apite ndi kutumikira milungu ya amitundu aja; kuti ungakhale pakati pa inu muzu wakubala ndulu ndi chowawa. 19#Mlal. 11.9Ndipo kungakhale, akamva mau a lumbiro ili adzadzidalitsa m'mtima mwake, ndi kuti, Ndidzakhala nao mtendere, ndingakhale ndiyenda nao mtima wanga wopulukira, kuledzera nditamva ludzu; 20#Ezk. 14.7-8Yehova sadzamkhululukira, koma pamenepo mkwiyo wa Yehova ndi nsanje yake zidzamfukira munthuyo; ndipo temberero lonse lolembedwa m'buku ili lidzamkhalira; ndipo Yehova adzafafaniza dzina lake pansi pa thambo. 21Ndipo Yehova adzamsiyanitsa ndi mafuko onse a Israele ndi kumchitira choipa, monga mwa matemberero onse a chipangano cholembedwa m'buku ili la chilamulo. 22Ndipo mbadwo ukudza, ana anu akuuka mutafa inu, ndi mlendo wochokera ku dziko lakutali, adzati, pakuona iwo miliri ya dziko ili, ndi nthendazi, Yehova awadwalitsa nazo. 23#Gen. 19.24Ndi kuti lidapsa dziko lake lonse ndi sulufure, ndi mchere, kuti sabzalamo, kapena siliphukitsa kanthu kapena sumerapo msipu, monga kupasula kwake kwa Sodomu ndi Gomora, Adima, ndi Zeboimu, imene Yehova anaipasula m'mkwiyo wake ndi ukali wake; 24inde amitundu onse adzati, Yehova anachitira dziko ili chotero chifukwa ninji? Nchiyani kupsa mtima kwakukulu kumene? 25Pamenepo adzati, popeza analeka chipangano cha Yehova, Mulungu wa makolo ao, chimene anachita nao pakuwatulutsa m'dziko la Ejipito; 26napita natumikira milungu ina, naigwadira, milungu imene sanaidziwa, imene sanawagawira; 27chifukwa chake Yehova anapsera mtima dziko ili kulitengera temberero lonse lolembedwa m'buku ili. 28#1Maf. 14.15Ndipo Yehova anawazula m'nthaka mwao mokwiya ndi mozaza, ndi m'ukali waukulu, nawaponya m'dziko lina, monga lero lino. 29Zinsinsi nza Yehova Mulungu wathu; koma zovumbuluka nza ife ndi ana athu kosatha, kuti tichite mau onse a chilamulo ichi.
Currently Selected:
DEUTERONOMO 29: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi