DEUTERONOMO 28
28
Madalitso pa kumvera kwao
1 #
Eks. 15.26; Yes. 55.2 Ndipo kudzali, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu mwachangu, ndi kusamalira kuchita malamulo ake onse amene ndikuuzani lero, kuti Yehova Mulungu wanu adzakukulitsani koposa amitundu onse a pa dziko lapansi; 2#Gen. 39.5; Zek. 1.6ndipo madalitso awa onse adzakugwerani, ndi kukupezani, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu. 3Mudzakhala odala m'mudzi, ndi odala kubwalo. 4#Mas. 107.38; Miy. 10.22Zidzakhala zodala zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, ndi zipatso za zoweta zanu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu. 5Lidzakhala lodala dengu lanu, ndi choumbiramo mkate wanu. 6#Mas. 121.8Mudzakhala odala polowa inu, mudzakhala odala potuluka inu. 7#2Sam. 22.40; Mas. 89.23Yehova adzakantha adani anu akukuukirani; adzakudzerani njira imodzi, koma adzathawa pamaso panu njira zisanu ndi ziwiri. 8#Mas. 133.3; Miy. 3.10Yehova adzakulamulirani dalitso m'nkhokwe zanu, ndi m'zonse mutulutsirako dzanja lanu; ndipo adzakudalitsani m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani. 9#Eks. 19.5Yehova adzakukhazikirani yekha mtundu wa anthu wopatulika, monga anakulumbirirani; ngati mudzasunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zake. 10#Yes. 61.9Ndipo anthu onse a pa dziko lapansi adzaona kuti akutchulani dzina la Yehova; nadzakuopani. 11Ndipo Yehova adzakuchulukitsirani zokoma, m'zipatso za thupi lanu, ndi m'zipatso za zoweta zanu, ndi m'zipatso za nthaka yanu, m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani ilo. 12#Lev. 26.4Yehova adzakutsegulirani chuma chake chokoma, ndicho thambo la kumwamba, kupatsa dziko lanu mvula m'nyengo yake, ndi kudalitsa ntchito zonse za dzanja lanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha. 13Ndipo Yehova adzakuyesani mutu, si mchira ai; ndipo mudzakhala wa pamwamba pokha, si wapansi ai; ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani lero, kuwasunga ndi kuwachita; 14osapatukira mau ali onse ndikuuzani lero, kulamanja, kapena kulamanzere, kutsata milungu ina kuitumikira.
Matemberero pa kusamvera kwao
15 #
Lev. 26.14
Koma kudzali, mukapanda kumvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kuchita malamulo ake onse ndi malemba ake amene ndikuuzani lero, kuti matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani. 16Mudzakhala otembereredwa m'mudzi, ndi otembereredwa pabwalo. 17Lidzakhala lotembereredwa dengu lanu ndi choumbiramo mkate wanu. 18Zidzakhala zotembereredwa zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu. 19Mudzakhala otembereredwa polowa inu, ndi otembereredwa potuluka inu. 20Yehova adzakutumizirani temberero, chisokonezeko, ndi kudzudzula monsemo mukatulutsa dzanja lanu kuchita kanthu, kufikira mwaonongeka, kufikira mwatayika msanga, chifukwa cha zochita inu zoipa, zimene wandisiya nazo. 21Yehova adzakumamatiritsani mliri, kufikira akakuthani kukuchotsani kudziko, kumene mupitako kulilandira. 22Yehova adzakukanthani ndi nthenda yoondetsa ya chifuwa, ndi malungo, ndi chibayo, ndi kutentha thupi, ndi lupanga, chinsikwi ndi chinoni; ndipo zidzakutsatani kufikira mwatayika. 23#Lev. 26.19Ndipo thambo lanu la pamwamba pamutu panu lidzakhala ngati mkuwa, ndi dziko lili pansi panu ngati chitsulo. 24Yehova adzasanduliza mvula ya dziko lanu ikhale fumbi ndi phulusa; zidzakutsikirani kuchokera kumwamba, kufikira mwaonongeka. 25#Yer. 24.9Yehova adzalola adani anu akukantheni; mudzawatulukira njira imodzi, koma mudzawathawa pamaso pao njira zisanu ndi ziwiri, ndipo mudzagwedezeka pakati pa maufumu onse a dziko lapansi. 26Ndipo mitembo yanu idzakhala chakudya cha mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi zilombo zonse za pa dziko lapansi, ndipo palibe wakuziingitsa. 27Yehova adzakukanthani ndi zilombo za ku Ejipito, ndi nthenda yotuluka mudzi, ndi chipere, ndi mphere, osachira nazo. 28#Zek. 12.4Yehova adzakukanthani ndi misala, ndi khungu, ndi kuzizwa mumtima; 29ndipo mudzafufuza usana, monga wakhungu amafufuza mumdima, ndipo simudzapindula nazo njira zanu; koma mudzakhala wopsinjika, nadzakuberani masiku onse, wopanda wina wakukupulumutsani. 30Mudzapalana ubwenzi ndi mkazi, koma mwamuna wina adzagona naye; mudzamanga nyumba, osakhala m'mwemo; mudzaoka munda wamphesa, osalawa zipatso zake. 31Adzapha ng'ombe yanu, pamaso panu, osadyako inu; adzalanda bulu wanu molimbana pamaso panu, osakubwezerani; adzapereka nkhosa zanu kwa adani anu, wopanda wina wakukupulumutsani. 32#2Mbi. 29.9Adzapereka ana anu aamuna ndi aakazi kwa anthu a mtundu wina, ndipo m'maso mwanu mudzada ndi kupenyerera, powalirira tsiku lonse; koma mulibe mphamvu m'dzanja lanu. 33#Yer. 5.17Mtundu wa anthu umene simudziwa udzadya zipatso za nthaka yanu ndi ntchito zanu zonse; ndipo mudzakhala wopsinjika ndi wophwanyika masiku onse; 34nimudzakhala oyeruka chifukwa chomwe muchiona ndi maso anu. 35Yehova adzakukanthani ndi chilonda choipa chosachira nacho kumaondo, ndi kumiyendo, kuyambira pansi pa phazi lanu kufikira pamwamba pa mutu panu. 36#2Maf. 17.6Yehova adzamukitsa inu, ndi mfumu yanu imene mudzadziikira, kwa mtundu wa anthu umene simudziwa, inu kapena makolo anu; ndipo mudzatumikirako milungu ina ya mitengo ndi miyala. 37#2Mbi. 7.20Ndipo mudzakhala chodabwitsa, ndi nkhani, ndi nthanthi, mwa mitundu yonse ya anthu amene Yehova akutsogoleraniko. 38#Mik. 6.15Mudzatuluka nazo mbeu zambiri kumunda, koma mudzakolola pang'ono; popeza dzombe lidzazitha. 39Mudzaoka m'minda yamphesa ndi kuilima, koma osamwa vinyo wake, kapena kutchera mphesa zake, popeza mbozi zidzaidya. 40Mudzakhala nayo mitengo ya azitona m'malire anu onse, osadzola mafuta; popeza zipatso za mitengo ya azitona zidzapululuka. 41Mudzabala ana aamuna ndi aakazi, osakhala nao, popeza adzalowa ukapolo. 42Mitengo yanu yonse ndi zipatso za nthaka yanu zidzakhala zaozao za dzombe. 43Mlendo wokhala pakati panu adzakulirakulira inu, koma inu mudzacheperachepera. 44#Deut. 28.12-13Iye adzakukongoletsani, osamkongoletsa ndinu; iye adzakhala mutu, koma inu ndinu mchira. 45Ndipo matemberero awa onse adzakugwerani, nadzakulondolani, ndi kukupezani, kufikira mwaonongeka, popeza simunamvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ake ndi malemba ake amene anakulamulirani; 46ndipo zidzakukhalirani inu ndi mbeu zanu ngati chizindikiro ndi chozizwa, nthawi zonse. 47#Neh. 9.35-37Popeza simunatumikira Yehova Mulungu wanu ndi chimwemwe ndi mokondwera mtima, chifukwa cha kuchuluka zinthu zonse; 48chifukwa chake mudzatumikira adani anu amene Yehova adzakutumizirani, ndi njala, ndi ludzu, ndi usiwa, ndi kusowa zinthu zonse; ndipo adzaika goli lachitsulo pakhosi panu, kufikira atakuonongani. 49#Luk. 19.43Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wochokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamva malankhulidwe ao; 50#2Mbi. 36.17mtundu wa anthu wa nkhope yaukali, wosamalira nkhope ya wokalamba, wosamchitira chifundo mwana; 51ndipo adzadya zipatso za ng'ombe zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, kufikira mwaonongeka; osakusiyirani tirigu, vinyo, kapena mafuta, zoswana ng'ombe zanu, zoswana nkhosa zanu, kufikira atakuonongani. 52#2Maf. 17.5Ndipo adzakuzingani m'midzi mwanu monse, kufikira adagwa malinga anu atali ndi olimba, amene munawakhulupirira, m'dziko lanu lonse; inde, adzakuzingani m'midzi mwanu monse, m'dziko lanu lonse limene Yehova Mulungu wanu akupatsani. 53#2Maf. 6.28-29Ndipo mudzadya chipatso cha thupi lanu, nyama ya ana anu aamuna ndi aakazi amene Yehova Mulungu wanu anakupatsani; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani adani anu. 54Mwamuna wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, diso lake lidzaipira mbale wake, ndi mkazi wa pa mtima wake, ndi ana ake otsalira; 55osapatsako mmodzi yense wa iwowa nyama ya ana ake alinkudyayo, popeza sikamtsalira kanthu; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdani wanu m'midzi mwanu monse. 56Mkazi wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, wosayesa kuponda pansi ndi phazi lake popeza ndiye wanyonga, ndi wololopoka nkhongono, diso lake lidzamuipira mwamuna wa pamtima pake, ndi mwana wake wamwamuna ndi wamkazi; 57ndicho chifukwa cha matenda akutuluka pakati pa mapazi ake, ndi ana ake adzawabala; popeza adzawadya m'tseri posowa zinthu zonse; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdani wanu m'midzi mwanu. 58#Eks. 6.3Mukapanda kusamalira kuchita mau onse a chilamulo ichi olembedwa m'buku ili, kuopa dzina ili la ulemerero ndi loopsa, ndilo Yehova Mulungu wanu; 59Yehova adzachita miliri yanu ndi ya ana anu ikhale yodabwitsa, miliri yaikulu ndi yokhalitsa, ndi nthenda zoipa ndi zokhalitsa. 60#Deut. 7.15Ndipo adzakubwezerani nthenda zonse za Ejipito, zimene munaziopa; ndipo zidzakumamatirani inu. 61Ndiponso nthenda zonse ndi miliri yonse zosalembedwa m'buku la chilamulo ichi, Yehova adzakutengerani izi, kufikira mwaonongeka. 62Ndipo mudzatsala anthu pang'ono, mungakhale mudachuluka ngati nyenyezi za m'mwamba; popeza simunamvera mau a Yehova Mulungu wanu. 63#Yes. 1.24; Yer. 32.14Ndipo kudzali kuti, monga Yehova anakondwera nanu kukuchitirani zabwino, ndi kukuchulukitsani; momwemo Yehova adzakondwera nanu kutayikitsa ndi kuononga inu, ndipo adzakuzulani kudziko kumene mulowako kulilandira. 64#Neh. 1.8Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu yonse ya anthu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero a dziko lapansi; ndipo kumeneko mudzatumikira milungu ina, imene simunaidziwa, inu ndi makolo anu, yamitengo ndi yamiyala. 65#Amo. 9.4Ndipo mwa a mitundu iyi simudzapumula, inde sipadzakhala popumulira phazi lanu; koma Yehova adzakupatsani kumeneko mtima wonjenjemera, m'maso mwanu mudzada, mudzafa ndi kulefuka mtima. 66Ndipo moyo wanu udzakhala wanjiranjira pamaso panu, ndipo mudzachita mantha usiku ndi usana, osakhazika mtima za moyo wanu. 67#Yob. 7.4M'mawa mudzati, Mwenzi atafika madzulo! Ndi madzulo mudzati, Mwezi utafika m'mawa! Chifukwa cha mantha a m'mtima mwanu amene mudzaopa nao, ndi chifukwa cha zopenya maso anu zimene mudzazipenya. 68#Yer. 43.7Ndipo Yehova adzakubwezerani ku Ejipito ndi ngalawa, pa njira imene ndinati kwa inu, kuti, Simudzaionanso; ndipo kumeneko mudzadzigulitsa kwa adani anu mukhale akapolo ndi adzakazi; koma palibe wogula inu.
Currently Selected:
DEUTERONOMO 28: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi