YouVersion Logo
Search Icon

DEUTERONOMO 27

27
Za kuutsa miyala ya chikumbutso ataoloka Yordani
1Ndipo Mose ndi akulu a Israele anauza anthu, nati, Sungani malamulo onse ndikuuzani lero. 2#Yos. 4.1; 8.30-32Ndipo kudzali, tsiku lakuoloka inu Yordani kulowa dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, kuti mudziutsire miyala yaikulu, ndi kuimata ndi njeresa; 3ndipo mulemberepo mau onse a chilamulo ichi, mutaoloka; kuti mulowe m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, monga Yehova Mulungu wa makolo anu ananena ndi inu. 4Ndipo kudzali, mutaoloka Yordani, muutse miyala iyi ndikuuzani lero, m'phiri la Ebala, ndi kuimata ndi njeresa. 5#Eks. 20.25; Yos. 8.31Ndipo komweko mumangire Yehova Mulungu wanu guwa la nsembe, guwa la nsembe lamiyala; musakwezepo pangizo chachitsulo. 6Mumange guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu lamiyala yosasema; ndi kuperekapo nsembe zopsereza kwa Yehova Mulungu wanu; 7ndi kuphera nsembe zoyamika, ndi kudyapo, ndi kukondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu. 8Ndipo mulembere pa miyalayi mau onse a chilamulo ichi mopenyeka bwino.
9 # Deut. 26.18 Ndipo Mose, ndi ansembe Alevi ananena ndi Israele wonse, ndi kuti, Khalani chete, imvanitu, Israele; lero lino mwasanduka mtundu wa anthu wa Yehova Mulungu wanu. 10Potero muzimvera mau a Yehova Mulungu wanu, ndi kuchita malamulo ake ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero lino.
Mdalitso ndi temberero ku Gerizimu ndi Ebala
11Ndipo Mose anauza anthu tsiku lomwelo, ndi kuti, 12#Yos. 8.33Aimirire awa pa phiri la Gerizimu kudalitsa anthu, mutaoloka Yordani: Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Isakara, ndi Yosefe, ndi Benjamini. 13Naimirire awa pa phiri la Ebala, kutemberera: Rubeni, Gadi, ndi Asere, ndi Zebuloni, Dani ndi Nafutali. 14Ndipo ayankhe Alevi ndi kunena kwa amuna onse a Israele, ndi mau omveka.
15 # Eks. 20.4; Yer. 11.5 Wotembereredwa munthu wakupanga fano losema kapena loyenga, lonyansidwa nalo Yehova, ntchito ya manja a mmisiri, ndi kuliika m'malo a m'tseri. Ndipo anthu onse ayankhe ndi kuti, Amen.
16 # Eks. 20.12 Wotembereredwa iye wakupeputsa atate wake kapena mai wake. Ndi anthu onse anene, Amen.
17 # Deut. 19.14 Wotembereredwa iye wakusendeza malire a mnansi wake. Ndi anthu onse anene, Amen.
18 # Lev. 19.14 Wotembereredwa wakusokeretsa wakhungu m'njira. Ndi anthu onse anene, Amen.
19 # Eks. 22.21 Wotembereredwa iye wakuipsa mlandu wa mlendo, mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye. Ndi anthu onse anene, Amen.
20 # Lev. 18.8 Wotembereredwa iye wakugona ndi mkazi wa atate wake; popeza wavula atate wake. Ndi anthu onse anene, Amen.
21 # Lev. 18.23 Wotembereredwa iye wakugona ndi nyama iliyonse. Ndi anthu onse anene, Amen.
22 # Lev. 18.9 Wotembereredwa iye wakugona ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa atate wake, kapena mwana wamkazi wa make. Ndi anthu onse anene, Amen.
23 # Lev. 18.17 Wotembereredwa iye wakugona ndi mpongozi wake. Ndi anthu onse anene, Amen.
24 # Deut. 19.11 Wotembereredwa iye wakukantha mnansi wake m'tseri. Ndi anthu onse anene, Amen.
25 # Eks. 23.7, 8 Wotembereredwa iye wakulandira chamwazi chakuti akanthe munthu wosachimwa. Ndi anthu onse anene, Amen.
26 # Agal. 3.10 Wotembereredwa iye wosavomereza mau a chilamulo ichi kuwachita. Ndi anthu onse anene, Amen.

Currently Selected:

DEUTERONOMO 27: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in