DEUTERONOMO 26
26
Chopereka cha zipatso zoyamba
1Ndipo kudzali, utakalowa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanu, ndipo mwachilandira ndi kukhala m'mwemo; 2#Eks. 23.19; Miy. 3.9kuti muzitengako zoyamba za zipatso zonse za nthaka, zakubwera nazo inu zochokera m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani; ndi kuziika mudengu, ndi kupita ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake. 3Ndipo mufike kwa wansembe wakukhala m'masiku awa, ndi kunena naye, Ndivomereza lero lino kwa Yehova Mulungu wako, kuti ndalowa m'dziko limene Yehova analumbirira makolo athu, kuti adzatipatsa ili. 4Ndipo wansembe alandire dengu m'manja mwanu, ndi kuuika pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu. 5#Hos. 12.12; Gen. 43; 45—46Ndipo muyankhe ndi kuti pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Kholo langa ndiye Mwaramu wakuti atayike, natsika kunka ku Ejipito, nagoneragonera komweko ali nao anthu pang'ono, nasandukako mtundu waukulu, wamphamvu, ndi wochuluka anthu ake; 6koma Aejipito anatichitira choipa, natizunza, natisenza ntchito yolimba. 7#Eks. 2.23-25Pamenepo tinafuulira kwa Yehova, Mulungu wa makolo athu; ndipo Yehova anamva mau athu, napenya kuzunzika kwathu, ndi ntchito yathu yolemetsa, ndi kupsinjika kwathu; 8#Eks. 12—13ndipo Yehova anatitulutsa m'Ejipito ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi kuopsa kwakukulu, ndi zizindikiro, ndi zodabwitsa; 9ndipo anabwera nafe kumalo kuno, natipatsa dziko ili ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi. 10Ndipo tsopano, taonani, ndabwera nazo zoyamba za zipatso za nthaka, zimene Inu, Yehova, mwandipatsa. Ndipo muziike pamaso pa Yehova Mulungu wanu; 11ndipo mukondwere nazo zokoma zonse zimene Yehova Mulungu wanu akupatsani, inu ndi nyumba zanu, inu ndi Mlevi, ndi mlendo ali pakati panu.
Limodzi la magawo khumi chaka chachitatu
12Mutatha kugawa magawo khumi, zobala zanu zonse chaka chachitatu, ndicho chaka chogawa magawo khumi, muzizipereka kwa Mlevi, kwa mlendo, kwa mwana wamasiye, ndi kwa mkazi wamasiye, kuti adye m'midzi mwanu, ndi kukhuta. 13#Mas. 119.141, 153, 176Ndipo munene pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Ndachotsa zopatulika m'nyumba mwanga, ndi kuzipereka kwa Mlevi, ndi kwa mlendo, ndi kwa mwana wamasiye, ndi kwa mkazi wamasiye, monga mwa lamulo lanu lonse munandilamulira ine; sindinalakwira malamulo anu, kapena kuwaiwala. 14Sindinadyako m'chisoni changa, kapena kuchotsako podetsedwa, kapena kuperekako kwa akufa; ndamvera mau a Yehova Mulungu wanga; ndachita monga mwa zonse munandilamulira ine. 15#Yes. 63.15Penyani muli mokhalamo mwanu mopatulika, m'mwamba, ndipo dalitseni anthu anu Israele, ndi nthaka imene munatipatsa, monga munalumbirira makolo athu, dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.
16Lero lino Yehova Mulungu wanu akulamulirani kuchita malemba ndi maweruzo awa; potero muzimvera ndi kuwachita ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse. 17#Eks. 24.7Mwalonjezetsa Yehova lero kuti adzakhala Mulungu wanu, ndi kuti mudzayenda m'njira zake, ndi kusunga malemba ake, ndi malamulo ake, ndi maweruzo ake, ndi kumvera mau ake. 18#Eks. 19.5Ndipo Yehova wakulonjezetsani lero kuti mudzakhala anthu akeake a pa okha, monga ananena ndi inu, ndi kuti mudzasunga malamulo ake onse; 19#Eks. 19.6kuti akukulitseni koposa amitundu onse anawalenga, wolemekezeka, womveka dzina, ndi waulemu; ndi kuti mukhale mtundu wa anthu wopatulikira Yehova Mulungu wanu monga ananena.
Currently Selected:
DEUTERONOMO 26: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi