YouVersion Logo
Search Icon

DEUTERONOMO 25

25
Za makwapulidwe a wolakwa
1 # Miy. 17.15 Pakakhala ndeu pakati pa anthu, nakapita kukaweruzidwa iwowa, nakaweruza mlandu wao oweruza; azimasula wolungama, namange woipa. 2Ndipo kudzali, wochita choipa akayenera amkwapule, woweruza amgonetse kuti amkwapule pamaso pake, amwerengere zofikira choipa chake. 3#2Ako. 11.24Amkwapule kufikira makumi anai, asaonjezepo; pakuti, akaonjezapo ndi kumkwapula mikwapulo yambiri, angapeputse mbale wanu pamaso panu. 4#Miy. 12.10; 1Ako. 9.9; 1Tim. 5.18Musamapunamiza ng'ombe popuntha tirigu.
Za kukwatibwa mkazi ndi mlamu wake
5 # Mat. 22.24 Abale akakhala pamodzi, nafa wina wa iwowa, wopanda mwana wamwamuna, mkazi wa wakufayo asakwatibwe ndi mlendo wakunja; mbale wa mwamuna wake alowane naye, namtenge akhale mkazi wake, namchitire zoyenera mbale wa mwamuna wake. 6Ndipo kudzali, kuti woyamba kubadwa amene adzambala, adzalowa dzina lake la mbale wake wakufayo, kuti dzina lake lisafafanizidwe m'Israele. 7#Rut. 4Ndipo ngati mwamunayo safuna kutenga mkazi wa mbale wake, mkazi wa mbale wakeyo azikwera kunka kuchipata, kwa akulu, ndi kuti, Mbale wa mwamuna wanga akana kuutsira mbale wake dzina m'Israele; safuna kundichitira ine zoyenera mbale wa mwamuna. 8Pamenepo akulu a mudzi wake amuitane, ndi kulankhula naye; ndipo akaimirira ndi kuti, Sindifuna kumtenga; 9pamenepo mkazi wa mbale wake azimyandikiza pamaso pa akulu, nachotse nsapato yake ku phazi la mwamunayo, ndi kumthira malovu pankhope pake, ndi kumyankha ndi kuti, Atere naye mwamuna wosamanga nyumba ya mbale wake. 10Ndipo azimutcha dzina lake m'Israele, Nyumba ya uje anamchotsa nsapato.
11Akalimbana wina ndi mnzake, nakayandikiza mkazi wa winayo kulanditsa mwamuna wake m'dzanja la wompandayo, nakatulutsa dzanja lake, ndi kumgwira kudzivalo; 12pamenepo muzidula dzanja lake; diso lanu lisamchitire chifundo.
13 # Miy. 11.1 Musamakhala nayo m'thumba mwanu miyala ya miyeso iwiri, waukulu ndi waung'ono. 14Musamakhala nayo m'nyumba yanu miyeso ya efa yosiyana, waukulu ndi waung'ono. 15Muzikhala nao mwala wa muyeso wofikira ndi woyenera; mukhale nao muyeso wa efa wofikira ndi woyenera; kuti masiku anu achuluke m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani. 16#1Ate. 4.6Pakuti onse akuchita zinthu izi, onse akuchita chisalungamo, Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao.
Amaleke afafanizike
17Kumbukirani chochitira inu Amaleke panjira, potuluka inu m'Ejipito; 18#Mas. 36.1; Aro. 3.18kuti anakomana ndi inu panjira, nakantha onse ofooka akutsala m'mbuyo mwanu, pakulema ndi kutopa inu; ndipo sanaope Mulungu. 19#1Sam. 15.3Ndipo kudzali, pamene Yehova Mulungu wanu atakupumulitsirani adani anu onse ozungulira, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanuchanu, kuti muzifafaniza chikumbutso cha Amaleke pansi pa thambo; musamaiwala.

Currently Selected:

DEUTERONOMO 25: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in