YouVersion Logo
Search Icon

DEUTERONOMO 24

24
Za kalata wa chilekaniro, chikole, kuba munthu, khate
1 # Mat. 19.7; Mrk. 10.4 Munthu akatenga mkazi akhale wake, kudzali, ngati sapeza ufulu pamaso pake, popeza anapeza mwa iye kanthu kosayenera, amlembere kalata wa chilekanitso, ndi kumpereka uyu m'dzanja lake, ndi kumtulutsa m'nyumba mwake. 2Ndipo atatuluka m'nyumba mwake, amuke nakhale mkazi wa mwamuna wina. 3Ndipo akamuda mwamuna wachiwiriyo, nakamlemberanso kalata wa chilekanitso, ndi kumpereka uyu m'dzanja lake, nakamtulutsa m'nyumba mwake; kapena akamwalira mwamuna wotsirizayo, amene anamtenga akhale mkazi wake; 4#Yer. 3.1pamenepo mwamuna woyamba anamchotsayo sangathe kumtenganso akhale mkazi wake, atadetsedwa iye; pakuti ichi ndi chonyansa pamaso pa Yehova; ndipo usamachimwitsa dziko, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholandira chanu.
5Munthu akatenga mkazi watsopano, asatuluke nayo nkhondo, kapena asamchititse kanthu kalikonse; akhale waufulu kunyumba yake chaka chimodzi, nakondweretse mkazi adamtengayo. 6Munthu asalandire chikole mphero, ngakhale mwanamphero, popeza alandirapo chikole moyo wa munthu.
7Akampeza munthu waba mbale wake wina wa ana a Israele, namuyesa kapolo, kapena wamgulitsa, afe wakubayo; potero muzichotsa choipacho pakati panu.
8 # Lev. 13—14 Chenjerani nayo nthenda yakhate, kusamaliratu, ndi kuchita monga mwa zonse akuphunzitsani ansembe Alevi; monga ndinalamulira iwo, momwemo muzisamalira kuchita. 9#Num. 12.10; Luk. 17.32; 1Ako. 10.6Kumbukirani chimene Yehova Mulungu wanu anachitira Miriyamu panjira, potuluka inu m'dziko la Ejipito.
Za kukongoletsa
10Mukakongoletsa mnansi wanu ngongole iliyonse, musamalowa m'nyumba mwake kudzitengera chikole chake. 11Muime pabwalo, ndi munthu amene umkongoletsayo azituluka nacho chikolecho kwa inu muli pabwalo. 12Ndipo akakhala munthu waumphawi musagone muli nacho chikole chake; 13#Eks. 22.26; Mas. 112.9polowa dzuwa mumbwezeretu chikolecho, kuti agone m'chovala chake, ndi kukudalitsani; ndipo kudzakukhalirani chilungamo pamaso pa Yehova Mulungu wanu.
Zachifundo pa antchito aumphawi, alendo ndi amasiye
14 # Mala. 3.5 Musamasautsa wolembedwa ntchito, wakukhala waumphawi ndi wosauka, wa abale anu kapena wa alendo ali m'dziko mwanu, m'midzi mwanu. 15#Lev. 19.13; Yer. 22.13; Yak. 5.4Pa tsiku lake muzimpatsa kulipira kwake, lisalowepo dzuwa; pakuti ndiye waumphawi, ndi mtima wake ukhumba uku; kuti angakulirireni kwa Yehova, ndipo kukukhalireni tchimo.
16 # 2Maf. 14.6; Yer. 31.29 Atate asaphedwere ana, ndi ana asaphedwere atate; munthu yense aphedwere tchimo lakelake.
17 # Eks. 22.21-22 Musamaipsa mlandu wa mlendo, kapena wa ana amasiye; kapena kutenga chikole chovala cha mkazi wamasiye; 18koma muzikumbukira kuti munali akapolo m'Ejipito, ndi kuti Yehova Mulungu wanu anakuombolaniko; chifukwa chake ndikuuzani kuchita chinthu ichi.
19 # Lev. 19.9-10 Mutasenga dzinthu zanu m'munda mwanu, ndipo mwaiwala mtolo m'mundamo, musabwererako kuutenga; ukhale wa mlendo, wa mwana wamasiye, ndi wa mkazi wamasiye; kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni m'ntchito zonse za manja anu.
20Mutagwedeza mtengo wanu wa azitona musayesenso nthambi mutatha nazo; akhale a mlendo, a mwana wamasiye, ndi a mkazi wamasiye. 21Mutatchera m'munda wanu wamphesa, musakunkha pambuyo panu; zikhale za mlendo, za mwana wamasiye, ndi za mkazi wamasiye. 22Ndipo muzikumbukira kuti munali akapolo m'dziko la Ejipito; chifukwa chake ndikuuzani kuchita chinthu ichi.

Currently Selected:

DEUTERONOMO 24: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in