YouVersion Logo
Search Icon

DEUTERONOMO 23

23
Oletsedwa ku msonkhano wa Yehova
1Munthu wophwetekwa, wophwanyika kapena wofulika, asalowe m'msonkhano wa Yehova.
2Mwana wa m'chigololo asalowe m'msonkhano wa Yehova, ngakhale mbadwo wake wakhumi usalowe m'msonkhano wa Yehova.
3 # Neh. 13.1-2 Mwamoni kapena Mmowabu asalowe m'msonkhano wa Yehova; ngakhale mbadwo wao wakhumi usalowe m'msonkhano wa Yehova, ku nthawi zonse; 4popeza sanakumana nanu ndi mkate ndi madzi m'njira muja munatuluka m'Ejipito; popezanso anakulembererani Balamu mwana wa Beori wa ku Petori wa Mesopotamiya, kuti akutemberereni. 5Ndipo Yehova Mulungu wanu sanafune kumvera Balamu; koma Yehova Mulungu wanu anakusandulizirani tembererolo likhale mdalitso, popeza Yehova Mulungu wanu anakukondani. 6Musawafunira mtendere, kapena chowakomera masiku anu onse ku nthawi zonse.
7 # Gen. 25.25, 30; Eks. 22.21 Musamanyansidwa naye Mwedomu, popeza ndiye mbale wanu; musamanyansidwa naye Mwejipito, popeza munali alendo m'dziko lake. 8Ana obadwa nao a mbadwo wachitatu alowe m'msonkhano wa Yehova. 9Nkhondo yanu ikatuluka pa adani anu, mudzisunge kusachita choipa chilichonse. 10Pakakhala munthu pakati pa inu, ndiye wosayera chifukwa chochitika usiku, azituluka kunja kwa chigono, asalowe pakati pa chigono; 11koma kudzali pofika madzulo, asambe m'madzi; ndipo litalowa dzuwa alowe pakati pa chigono. 12Mukhale nao malo kunja kwa chigono kumene muzimukako kuthengo; 13nimukhale nacho chokumbira mwa zida zanu; ndipo kudzali, pakukhala inu pansi kuthengo mukumbe nacho, ndi kutembenuka ndi kufotsera chakutulukacho; 14popeza Yehova Mulungu wanu ayenda pakati pa chigono chanu kukupulumutsani ndi kupereka adani anu pamaso panu; chifukwa chake chigono chanu chikhale chopatulika; kuti angaone kanthu kodetsa mwa inu, ndi kukupotolokerani.
Za akapolo opulumuka, za achigololo, za okongoletsa mopindulitsa
15Musamapereka kwa mbuye wake kapolo wopulumuka kwa mbuye wake kuthawira kwa inu; 16akhale nanu, pakati panu, ku malo asankhako iye m'mudzi mwanu mwina momkonda; musamamsautsa.
17Pasakhale mkazi wachigololo pakati pa ana akazi a Israele, kapena wachigololo pakati pa ana amuna a Israele. 18Musamabwera nayo mphotho ya wachigololo, kapena mtengo wake wa galu kulowa nazo m'nyumba ya Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha chowinda chilichonse; pakuti onse awiriwa Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao.
19 # Neh. 5.7; Luk. 6.34-35 Musamakongoletsa mbale wanu mopindulitsa; phindu la ndalama, phindu la chakudya, phindu la kanthu kalikonse kokongoletsa. 20Mukongoletse mlendo mopindulitsa; koma mbale wanu musamamkongoletsa mopindulitsa, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni mwa zonse muzigwira ndi dzanja lanu, m'dziko limene mulowamo kulilandira.
21 # Num. 30.2; Mas. 66.13-14 Mukawindira Yehova Mulungu wanu chowinda, musamachedwa kuchichita; popeza Yehova Mulungu wanu adzakufunsani za ichi ndithu ndipo mukadachimwako. 22Koma mukapanda kulonjeza chowinda, mulibe kuchimwa. 23Chotuluka pa milomo yanu muchisamalire ndi kuchichita; monga munalonjezera Yehova Mulungu wanu, chopereka chaufulu munachilonjeza pakamwa panu.
24Mukalowa m'munda wamphesa wa mnansi wanu, mudyeko mphesa ndi kukhuta nazo monga mufuna eni; koma musaika kanthu m'chotengera chanu.
25 # Mat. 12.1 Mukalowa m'tirigu wosasenga wa mnansi wanu, mubudule ngala ndi dzanja lanu, koma musasengako ndi chisenga tirigu wachilili wa mnansi wanu.

Currently Selected:

DEUTERONOMO 23: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in