1
DEUTERONOMO 28:1
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Ndipo kudzali, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu mwachangu, ndi kusamalira kuchita malamulo ake onse amene ndikuuzani lero, kuti Yehova Mulungu wanu adzakukulitsani koposa amitundu onse a pa dziko lapansi
Compare
Explore DEUTERONOMO 28:1
2
DEUTERONOMO 28:2
ndipo madalitso awa onse adzakugwerani, ndi kukupezani, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu.
Explore DEUTERONOMO 28:2
3
DEUTERONOMO 28:13
Ndipo Yehova adzakuyesani mutu, si mchira ai; ndipo mudzakhala wa pamwamba pokha, si wapansi ai; ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani lero, kuwasunga ndi kuwachita
Explore DEUTERONOMO 28:13
4
DEUTERONOMO 28:12
Yehova adzakutsegulirani chuma chake chokoma, ndicho thambo la kumwamba, kupatsa dziko lanu mvula m'nyengo yake, ndi kudalitsa ntchito zonse za dzanja lanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha.
Explore DEUTERONOMO 28:12
5
DEUTERONOMO 28:7
Yehova adzakantha adani anu akukuukirani; adzakudzerani njira imodzi, koma adzathawa pamaso panu njira zisanu ndi ziwiri.
Explore DEUTERONOMO 28:7
6
DEUTERONOMO 28:8
Yehova adzakulamulirani dalitso m'nkhokwe zanu, ndi m'zonse mutulutsirako dzanja lanu; ndipo adzakudalitsani m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.
Explore DEUTERONOMO 28:8
7
DEUTERONOMO 28:6
Mudzakhala odala polowa inu, mudzakhala odala potuluka inu.
Explore DEUTERONOMO 28:6
8
DEUTERONOMO 28:3
Mudzakhala odala m'mudzi, ndi odala kubwalo.
Explore DEUTERONOMO 28:3
9
DEUTERONOMO 28:4
Zidzakhala zodala zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, ndi zipatso za zoweta zanu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu.
Explore DEUTERONOMO 28:4
10
DEUTERONOMO 28:9
Yehova adzakukhazikirani yekha mtundu wa anthu wopatulika, monga anakulumbirirani; ngati mudzasunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zake.
Explore DEUTERONOMO 28:9
11
DEUTERONOMO 28:5
Lidzakhala lodala dengu lanu, ndi choumbiramo mkate wanu.
Explore DEUTERONOMO 28:5
12
DEUTERONOMO 28:11
Ndipo Yehova adzakuchulukitsirani zokoma, m'zipatso za thupi lanu, ndi m'zipatso za zoweta zanu, ndi m'zipatso za nthaka yanu, m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani ilo.
Explore DEUTERONOMO 28:11
13
DEUTERONOMO 28:10
Ndipo anthu onse a pa dziko lapansi adzaona kuti akutchulani dzina la Yehova; nadzakuopani.
Explore DEUTERONOMO 28:10
14
DEUTERONOMO 28:14
osapatukira mau ali onse ndikuuzani lero, kulamanja, kapena kulamanzere, kutsata milungu ina kuitumikira.
Explore DEUTERONOMO 28:14
15
DEUTERONOMO 28:15
Koma kudzali, mukapanda kumvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kuchita malamulo ake onse ndi malemba ake amene ndikuuzani lero, kuti matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani.
Explore DEUTERONOMO 28:15
Home
Bible
Plans
Videos