YOSWA Mau Oyamba
Mau Oyamba
Bukuli likukamba za m'mene Aisraele adalowera m'dziko la Kanani nkulilanda, Yoswa akuwatsogolera. Kenaka adagawana dzikolo.
Nkhani zodziwika bwino m'bukuli ndizo kuoloka Yordani, kugwa kwa Yeriko, kugonjetsedwa kwa Ai, ndi kukonzanso kwa chipangano pakati pa Mulungu ndi anthu ake.
Mau odziwika bwino ndi awa: “mudzisankhire lero amene mudzamtumikira…koma ine, ndi a m'nyumba yanga, tidzatumikira Yehova” (24.15).
Za mkatimu
Aisraele atenga dziko la Kanani 1.1—12.24
a. Aoloka mtsinje wa Yordani 1.1—5.15
b. Agonjetsa mzinda la Yeriko 6.1—7.26
c. Agonjetsa mzinda wa Ai ndi mizinda ina 8.1—12.24
Aisraele agawana dziko 13.1—22.34
a. Dziko la kum'mawa kwa Yordani 13.1-33
b. Dziko la kuzambwe kwa Yordani 14.1—19.51
c. Midzi yopulumukirako 20.1-9
d. Mafuko awiri akum'mawa abwerera ku dziko lao 22.1-34
Mau a Yoswa otsanzikana nawo 23.1-16
Abwereza kuchita chipangano ku Sekemu 24.1-33
Currently Selected:
YOSWA Mau Oyamba: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi