YouVersion Logo
Search Icon

DANIELE 11

11
1 # Dan. 9.1 Ndipo ine, chaka choyamba cha Dariusi Mmedi, ndinauka kumlimbikitsa ndi kumkhazikitsa. 2Ndipo tsopano ndikufotokozera choonadi. Taona, adzaukanso mafumu atatu m'Persiya, ndi yachinai idzakhala yolemera ndithu yoposa onsewo; ndipo itadzilimbitsa yokha mwa kulemera kwake idzawautsa onse alimbane nao ufumu wa Agriki. 3#Dan. 8.5Ndipo idzauka mfumu yamphamvu, nidzachita ufumu ndi ulamuliro waukulu, nidzachita monga mwa chifuniro chake. 4#Dan. 8.8Ndipo pakuuka iye ufumu wake udzathyoledwa, nudzagawikira kumphepo zinai za mlengalenga; koma sadzaulandira a mbumba yake akudza m'mbuyo, kapena monga mwa ulamuliro wake anachita ufumu nao; pakuti ufumu wake udzazulidwa, ukhale wa ena, si wa aja ai.
Nkhondo ya pakati pa mfumu ya kumpoto ndi ya kumwera
5Ndipo mfumu ya kumwera, ndiye wina wa akalonga ake, idzamposa mphamvu, nidzakhala nao ulamuliro; ulamuliro wake ndi ulamuliro waukulu. 6Ndipo pakutha zaka adzaphatikizana iwo; ndi mwana wamkazi wa mfumu ya kumwera adzafika kwa mfumu ya kumpoto, kupangana naye zoyenera; koma mkaziyo sadzaisunga mphamvu ya dzanja lake; ngakhale mwamunayo sadzaimika, ngakhale dzanja lake; koma mkaziyo adzaperekedwa, pamodzi ndi iwo adadza naye, ndi iye amene anambala, ndi iye amene anamlimbitsa nthawi zija. 7Koma apo pophukira mizu yake adzauka wina m'malo mwake, ndiye adzafika kulimbana nalo khamu la nkhondo, nadzalowa m'linga la mfumu ya kumpoto, nadzachita molimbana nao, nadzawalaka; 8ndi milungu yao yomwe, pamodzi ndi akalonga ao, ndi zipangizo zao zofunika zasiliva ndi golide adzazitenga kunka nazo ndende ku Ejipito; ndi zaka zake zidzaposa za mfumu ya kumpoto. 9Ndipo adzalowa m'ufumu wa mfumu ya kumwera, koma adzabwera m'dziko lakelake. 10Ndi ana ake adzachita nkhondo, nadzamemeza makamu a nkhondo akulu ochuluka, amene adzalowa, nadzasefukira, nadzapita; ndipo adzabwerera, nadzachita nkhondo mpaka linga lake. 11Ndi mfumu ya kumwera adzawawidwa mtima, nadzatuluka kulimbana naye, ndiye mfumu ya kumpoto imene idzaonetsa unyinji waukulu; koma unyinjiwo udzaperekedwa m'dzanja lake. 12Ndipo atauchotsa unyinjiwo udzakwezeka mtima wake; ndipo adzagwetsa zikwi makumimakumi, koma sadzalakika. 13Ndi mfumu ya kumpoto idzabwera, nidzaimika unyinji wakuposa oyamba aja; nidzafika pachimaliziro cha nthawi, cha zaka, ndi khamu lalikulu la nkhondo ndi chuma chambiri. 14Ndipo nthawi zija ambiri adzaukira mfumu ya kumwera, ndi achiwawa mwa anthu a mtundu wako adzadzikuza kukhazikitsa masomphenyawo, koma adzagwa iwo. 15Ndi mfumu ya kumpoto idzadza, nidzaunda mtumbira, nidzalanda midzi yamalinga; ndi ankhondo a kumwera sadzalimbika, ngakhale anthu ake osankhika; inde sipadzakhala mphamvu yakulimbika. 16#Dan. 8.4, 7Koma iye amene amdzera kulimbana naye adzachita chifuniro chake cha iye mwini; palibe wakulimbika pamaso pake; ndipo adzaima m'dziko lokometsetsalo, ndi m'dzanja mwake mudzakhala chionongeko. 17Ndipo adzalimbitsa nkhope yake, kudza ndi mphamvu ya ufumu wake wonse, ndi oongoka mtima pamodzi naye; ndipo adzachita chifuniro chake, nadzampatsa mwana wamkazi wa akazi kumuipitsa; koma mkaziyo sadzalimbika, kapena kuvomerezana naye. 18Pambuyo pake adzatembenuzira nkhope yake kuzisumbu, nadzalanda zambiri; koma kalonga wina adzaleketsa kunyoza kwake adanyoza nako; inde adzambwezera yekha kunyoza kwake. 19Pamenepo adzatembenuzira nkhope yake kumalinga a dziko lakelake; koma adzakhumudwa, nadzagwa osapezedwanso. 20Ndipo m'malo mwake adzauka wina wakupititsa wamsonkho pa ulemerero wa ufumuwo; koma atatha masiku owerengeka adzathyoledwa iye, si mwamkwiyo, kapena kunkhondo ai. 21Ndi m'malo mwake adzauka munthu woluluka, amene anthu sanampatse ulemu wa ufumu, koma adzafika kachetechete, nadzalanda ufumu ndi mau osyasyalika. 22Ndipo mwa mayendedwe ake a chigumula adzakokololedwa pamaso pake, nadzathyoledwa, ngakhale kalonga yemwe wa chipangano. 23Ndipo atapangana naye adzachita monyenga; pakuti adzakwera, nadzasanduka wamphamvu ndi anthu owerengeka. 24Adzafika kachetechete kuminda yokometsetsa ya derali, nadzachita chosachita atate ake, kapena makolo ake; adzawawazira zofunkha, ndi zankhondo, ndi chuma, nadzalingiririra malinga ziwembu zake; adzatero nthawi. 25Nadzautsa mphamvu yake ndi mtima wake ayambane ndi mfumu ya kumwera ndi khamu lalikulu la nkhondo; ndi mfumu ya kumwera idzachita nkhondo ndi khamu lalikulu ndi lamphamvu ndithu; koma sadzaimika, popeza adzamlingiririra ziwembu. 26Inde iwo akudyako chakudya chake adzamuononga; ndi ankhondo ake adzasefukira, nadzagwa ambiri ophedwa. 27Ndipo mafumu awa onse awiri mitima yao idzakumbuka kuchita zoipa, nadzanena bodza ali pa gome limodzi; koma osapindula nalo; pakuti kutha kwake kudzakhala pa nthawi yoikika. 28Ndipo adzabwerera kudziko lake ndi chuma chambiri; ndi mtima wake udzatsutsana ndi chipangano chopatulika, nadzachita chifuniro chake, ndi kubwerera kudziko lake. 29Pa nthawi yoikika adzabwera, nadzalowa kumwera; koma sikudzakhala monga nthawi yoyamba ija, kapena yotsirizayi. 30#Num. 24.24Pakuti zombo za ku Kitimu zidzafika kuyambana naye; chifukwa chake adzatenga nkhawa, nadzabwerera, nadzaipidwa mtima ndi chipangano chopatulika, nadzachita chifuniro chake; adzabweranso, nadzasamalira otaya chipangano chopatulika. 31Ndipo ankhondo adzamuimirira, nadzadetsa malo opatulika ndi linga lake; nadzachotsa nsembe yosalekezayo, nadzaimitsa chonyansa chopululutsacho. 32Ndipo akuchitira choipa chipanganocho iye adzawaipsa, ndi kuwasyasyalika; koma anthu akudziwa Mulungu wao adzalimbika mtima, nadzachita mwamphamvu. 33#Mala. 2.7Ndipo aphunzitsi a anthu adzalangiza ambiri, koma adzagwa ndi lupanga, ndi lawi lamoto, ndi undende, ndi kufunkhidwa masiku ambiri. 34Ndipo pakugwa iwo adzathandizidwa ndi thandizo laling'ono; koma ambiri adzaphatikizana nao ndi mau osyasyalika. 35Nadzagwa aphunzitsi ena kuwayesa ndi moto, ndi kuwatsutsa, ndi kuwayeretsa, mpaka nthawi ya chitsiriziro; pakuti kukaliko kufikira nthawi yoikika. 36#2Ate. 2.3-4Ndipo mfumu idzachita monga mwa chifuniro chake, nidzadzikweza, ndi kudzikuza koposa milungu iliyonse nidzanena zodabwitsa pa Mulungu wa milungu, nidzapindula, mpaka udzachitidwa ukaliwo; pakuti chotsimikizika m'mtimacho chidzachitika. 37Ndipo sidzasamalira milungu ya makolo ake, kapena choikhumba akazi, kapena kusamalira milungu iliyonse; pakuti idzadzikuza koposa onse. 38Koma kumalo kwake idzachitira ulemu mulungu wa malinga; ndi mulungu amene makolo ake sanaudziwe, adzaulemekeza ndi golide, ndi siliva, ndi miyala ya mtengo wake, ndi zinthu zofunika. 39Ndipo adzachita molimbana ndi malinga olimba koposa, pomthandiza mulungu wachilendo; aliyense womvomereza adzamchulukitsira ulemu, nadzawachititsa ufumu pa ambiri, nadzagawa dziko mwa mtengo wake. 40Ndipo nthawi yotsiriza mfumu ya kumwera idzalimbana naye, ndi mfumu ya kumpoto idzamdzera ngati kamvulumvulu, ndi magaleta, ndi apakavalo, ndi zombo zambiri; nadzalowa m'maiko, nadzasefukira ndi kupitirira. 41Adzalowanso m'dziko lokometsetsalo ndi maiko ambiri adzapasuka; koma opulumuka dzanja lake ndi awa: Edomu, ndi Mowabu, ndi oyamba a ana a Amoni. 42Adzatambalitsiranso dzanja lake kumaiko; dziko la Ejipito lomwe silidzapulumuka. 43Ndipo adzachita mwamphamvu ndi chuma cha golide, ndi siliva, ndi zinthu zofunika zonse za Ejipito; Libiya ndi Akusi adzatsata mapazi ake. 44Koma mbiri yochokera kum'mawa ndi kumpoto idzamvuta; nadzatuluka iye ndi ukali waukulu kupha ndi kuononga konse ambiri. 45Ndipo adzamanga mahema a nyumba yachifumu yake pakati pa nyanja ndi phiri lopatulika lofunika; koma adzafikira chimaliziro chake wopanda wina wakumthandiza.

Currently Selected:

DANIELE 11: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in