DANIELE 12
12
Nthawi ya chimaliziro, mau otsekedwa
1 #
Yes. 26.20-21; Dan. 10.13, 21; Mat. 24.21; Luk. 10.20; Aro. 11.26; Afi. 4.3; Chiv. 16.18 Ndipo nthawi yomweyi adzauka Mikaele kalonga wamkulu wakutumikira ana a anthu a mtundu wako; ndipo padzakhala nthawi ya masautso, siinakhala yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthawi yomwe ija; ndipo nthawi yomweyo anthu ako adzapulumutsidwa, yense amene ampeza wolembedwa m'buku. 2#Mat. 25.46; Yoh. 5.28-29Ndipo ambiri a iwo ogona m'fumbi lapansi adzauka, ena kunka kumoyo wosatha, ndi ena kumanyazi ndi mnyozo wosatha. 3#Mala. 2.6; Mat. 13.43; Yak. 5.20Ndipo aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate chilungamo ngati nyenyezi kunthawi za nthawi. 4#Chiv. 10.4; 22.10Koma iwe Daniele, tsekera mau awa, nukomere chizindikiro buku, mpaka nthawi ya chimaliziro; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziwitso chidzachuluka.
5Pamenepo ine Daniele ndinapenya, ndipo taonani, anaimapo awiri ena, wina m'mphepete mwa mtsinje tsidya lino, ndi mnzake m'mphepete mwa mtsinje tsidya lija. 6#Dan. 10.5Ndipo wina anati kwa munthu wovala bafuta, wokhala pamwamba pa madzi a mumtsinje, Chimaliziro cha zodabwitsa izi chidzafika liti? 7Ndipo ndinamva munthuyo wovala bafuta wokhala pamwamba pa madzi a mumtsinje, nakweza dzanja lake lamanja ndi lamanzere kumwamba, nalumbira pali Iye wokhala ndi moyo kosatha, kuti zidzachitika nthawi, ndi nthawi zina, ndi nusu; ndipo atatha kumwaza mphamvu ya anthu opatulikawo zidzatha izi zonse. 8Ndinachimva ichi, koma osachizindikira; pamenepo ndinati Mbuye wanga, chitsiriziro cha izi nchiyani? 9#Dan. 12.4Ndipo anati, Pita Daniele; pakuti mauwo atsekedwa, nakomeredwa chizindikiro mpaka nthawi ya chitsiriziro. 10#Zek. 13.9Ambiri adzadzitsuka ndi kudziyeretsa, nadzayesedwa ndi moto; koma oipa adzachita moipa; ndipo palibe mmodzi wa oipa adzazindikira; koma aphunzitsi ndiwo adzazindikira. 11#Dan. 8.11Ndipo kuyambira nthawi yoti idzachotsedwa nsembe yachikhalire, nichidzaimika chonyansa chakupululutsa, adzakhalanso masiku chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai. 12Wodala iye amene ayembekeza, nafikira kumasiku chikwi chimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi atatu ndi asanu. 13Koma iwe, muka mpaka chimaliziro; pakuti udzapumula, nudzaima m'gawo lako masiku otsiriza.
Currently Selected:
DANIELE 12: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi