Ndipo ankhondo adzamuimirira, nadzadetsa malo opatulika ndi linga lake; nadzachotsa nsembe yosalekezayo, nadzaimitsa chonyansa chopululutsacho. Ndipo akuchitira choipa chipanganocho iye adzawaipsa, ndi kuwasyasyalika; koma anthu akudziwa Mulungu wao adzalimbika mtima, nadzachita mwamphamvu.