DANIELE 10
10
Daniele aona masomphenya oopsa, mngelo amlimbikitsa
1 #
Chiv. 19.9
Chaka chachitatu cha Kirusi mfumu ya Persiya, chinavumbulutsidwa chinthu kwa Daniele, amene anamutcha Belitesazara; ndipo chinthucho nchoona, ndicho nkhondo yaikulu; ndipo anazindikira chinthucho, nadziwa masomphenyawo. 2Masiku aja ine Daniele ndinali kulira masabata atatu amphumphu. 3Chakudya chofunika osachidya ine, nyama kapena vinyo zosapita pakamwa panga, osadzola ine konse, mpaka anakwaniridwa masabata atatu amphumphu. 4#Gen. 2.14Ndipo tsiku la makumi awiri mphambu anai la mwezi woyamba, pokhala ine m'mphepete mwa mtsinje waukulu, ndiwo Tigrisi, 5#Dan. 12.6-7ndinakweza maso anga, ndinapenya ndi kuona munthu wovala bafuta, womanga m'chuuno ndi golide woona wa ku Ufazi; 6thupi lake lomwe linanga berulo, ndi nkhope yake ngati maonekedwe a mphezi, ndi maso ake ngati nyali zamoto, ndi manja ake ndi mapazi ake akunga mkuwa wonyezimira, ndi kumveka kwa mau ake kunanga phokoso la aunyinji. 7#2Maf. 6.17; Mac. 9.7Ndipo ine Daniele ndekha ndinaona masomphenyawo; pakuti anthu anali nane sanaone masomphenyawo; koma kunawagwera kunjenjemera kwakukulu, nathawa kubisala. 8Momwemo ndinatsala ndekha, ndipo ndinaona masomphenya akuluwa, koma wosakhala ndi mphamvu ine; pakuti kukoma kwanga kunasandulika chivundi mwa ine, wosakhalanso ndi chimphamvu ine. 9Ndipo ndinamva kunena kwa mau ake, ndipo pamene ndinamva kunena kwa mau ake ndinagwidwa ndi tulo tatikulu pankhope panga, nkhope yanga pansi. 10#Yer. 1.9Ndipo taonani, linandikhudza dzanja ndi kundikhalitsa ndi maondo anga, ndi zikhato za manja anga. 11#Dan. 9.23Nati kwa ine, Daniele, munthu wokondedwatu iwe, tazindikira mau ndilikunena ndi iwe, nukhale chilili; pakuti ndatumidwa kwa iwe tsopano. Ndipo pamene adanena mau awa kwa ine ndinaimirira ndi kunjenjemera. 12#Dan. 9.3-4; Mac. 10.4; Chiv. 1.17Pamenepo anati kwa ine, Usaope Daniele; pakuti kuyambira tsiku loyamba lija unaika mtima wako kuzindikira ndi kudzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, mau ako anamveka; ndipo ndadzera mau ako. 13Koma kalonga wa ufumu wa Persiya ananditsekerezera njira masiku makumi awiri ndi limodzi; ndipo taonani, Mikaele, wina wa akalonga omveka, anadza kundithandiza; ndipo ndinakhala komweko ndi mafumu a Persiya. 14#Dan. 8.26Ndadzera tsono kukuzindikiritsa chodzagwera anthu a mtundu wako masiku otsiriza; pakuti masomphenyawo ndiwo a masiku a m'tsogolo. 15Ndipo atanena ndi ine monga mwa mau awa, ndinaweramitsa nkhope yanga pansi ndi kukhala duu. 16#Dan. 10.10Ndipo taonani, wina wakunga ana a anthu anakhudza milomo yanga; pamenepo ndinatsegula pakamwa panga ndi kunena naye woima popenyana nane, Mbuye wanga, chifukwa cha masomphenyawo zowawa zanga zandibwerera, ndipo ndilibenso mphamvu. 17Pakuti mnyamata wa mbuye wanga inu akhoza bwanji kulankhula ndi mbuye wanga inu? Pakuti ine tsopano apa mulibenso mphamvu mwa ine, osanditsaliranso mpweya.
Nkhondo ya pakati pa Persiya ndi Grisi
18Pamenepo anandikhudzanso wina, maonekedwe ake ngati munthu, nandilimbikitsa ine. 19#Ower. 6.23; Dan. 10.11Nati, Munthu wokondedwatu iwe, Usaope, mtendere ukhale nawe; limbika, etu limbika. Ndipo pamene ananena ndi ine ndinalimbikitsidwa, ndinati, Anene mbuye wanga; pakuti mwandilimbikitsa. 20#Dan. 10.13Pamenepo anati, Kodi udziwa chifukwa choti ndakudzera? Ndipo tsopano ndibwerera kulimbana ndi kalonga wa Persiya; ndipo pomuka ine, taonani, adzadza kalonga wa Agriki. 21#Dan. 10.13; Yud. 9; Chiv. 12.7Koma ndidzakufotokozera cholembedwa pa lemba la choonadi; ndipo palibe wina wakudzilimbikitsa pamodzi ndi ine, kutsutsana ndi aja, koma Mikaele kalonga wanu.
Currently Selected:
DANIELE 10: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi