AMOSI 5
5
Nyimbo ya maliro yakunena za kuthyola kwa Israele
1Tamverani mau awa ndinenawa, akhalire inu nyimbo ya maliro, nyumba ya Israele inu. 2Namwali wa Israele wagwa, sadzaukanso; wagwetsedwa pa nthaka yake, palibe womuutsa. 3Pakuti atero Ambuye Yehova, M'nyumba ya Israele, mudzi wotulukamo chikwi chimodzi adzautsalira zana limodzi, ndi uwu wotulukamo zana limodzi adzautsalira khumi. 4#Yes. 55.3Pakuti atero Yehova kwa nyumba ya Israele, Mundifunefune Ine, ndipo mudzakhala ndi moyo; 5#Amo. 4.4koma musamafuna Betele, kapena kumalowa m'Giligala; musamapita ku Beereseba; pakuti Giligala adzalowadi m'ndende, ndi Betele adzasanduka chabe. 6#Yes. 55.3Funani Yehova, ndipo mudzakhala ndi moyo; angabuke ngati moto m'nyumba ya Yosefe, ndipo unganyeke wopanda wakuzima m'Betele; 7inu osintha chiweruzo chikhale chivumulo, nimugwetsa pansi chilungamo. 8#Yob. 9.9; Mas. 104.6-7, 20Iye wakulenga Nsangwe ndi Akamwiniatsatana, nasanduliza mdima wandiweyani ukhale m'mawa, nasanduliza usana ude ngati usiku, wakuitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira pa dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova; 9wakufikitsa chionongeko pa wamphamvu modzidzimuka, chionongeko nichigwera linga. 10#1Maf. 22.8Iwo adana naye wodzudzula kuchipata, nanyansidwa naye wolunjikitsa mau. 11#Deut. 28.15, 30, 38-39Popeza tsono mupondereza aumphawi, ndi kumsokhetsa tirigu; mwamanga nyumba za miyala yosema, koma simudzakhala m'mwemo; mwaoka minda ya mipesa yokonda, koma simudzamwa vinyo wake. 12#Amo. 2.6Pakuti ndidziwa kuti zolakwa zanu nzochuluka, ndi machimo anu ndi olimba, inu akusautsa olungama, akulandira chokometsera mlandu, akukankha osowa kuchipata. 13Chifukwa chake wochenjerayo akhala chete nthawi yomweyo; pakuti ndiyo nthawi yoipa. 14Funani chokoma, si choipa ai; kuti mukhale ndi moyo; motero Yehova Mulungu wa makamu adzakhala ndi inu, monga munena. 15#Mas. 34.14; Aro. 12.9Danani nacho choipa, nimukonde chokoma; nimukhazikitse chiweruzo kuchipata; kapena Yehova Mulungu wa makamu adzachitira chifundo otsala a Yosefe. 16#Yer. 9.17Chifukwa chake atero Yehova, Mulungu wa makamu, Ambuye, M'makwalala onse mudzakhala kulira, ndi m'miseu yonse adzati, Kalanga ine! Kalanga ine! Nadzaitana wakumunda adze kumaliro, ndi odziwa maliridwe a nthetemya alire. 17Ndi m'minda yonse yamipesa mudzakhala kulira, pakuti ndipita pakati pako, ati Yehova. 18#Yow. 2.1-2Tsoka inu akufuna tsiku la Yehova? Mudzapindulanji nalo tsiku la Yehova? Ndilo mdima, si kuunika ai. 19Kudzakhala monga munthu akathawa mkango, ndi chimbalangondo chikomana naye; kapena akalowa m'nyumba, natsamira kukhoma ndi dzanja lake, nimluma njoka. 20Kodi tsiku la Yehova silidzakhala la mdima, si la kuunika ai? Lakuda bii, lopanda kuwala m'menemo? 21#Yes. 1.11-16Ndidana nao, ndinyoza zikondwerero zanu, sindidzakondwera nao masonkhano anu oletsa. 22#Mik. 6.6-7Inde, mungakhale mupereka kwa Ine nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zaufa, sindidzazilandira Ine; ndi nsembe zoyamika za ng'ombe zanu zonenepa, sindidzazisamalira Ine. 23Mundichotsere phokoso la nyimbo zanu; sindifuna kumva mayimbidwe a zisakasa zanu. 24Koma chiweruzo chiyende ngati madzi, ndi chilungamo ngati mtsinje wosefuka. 25#Mac. 7.42Ngati munabwera nazo kwa Ine nsembe zophera ndi zaufa zaka makumi anai m'chipululu, inu nyumba ya Israele? 26#Mac. 7.43Inde mwasenza hema wa mfumu yanu, ndi tsinde la mafano anu, nyenyezi ya mulungu wanu, amene mudadzipangira. 27#2Maf. 17.16M'mwemo ndidzakutengani kunka nanu kundende kutsogolo kwa Damasiko, ati Yehova, amene dzina lake ndiye Mulungu wa makamu.
Currently Selected:
AMOSI 5: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi