YouVersion Logo
Search Icon

AMOSI 4

4
Aisraele adzadulidwa chifukwa cha zoipa ndi kuuma mtima kwao
1Tamverani mau awa, inu ng'ombe zazikazi za ku Basani, zokhala m'phiri la Samariya, zosautsa aumphawi, zopsinja osowa, zonena kwa ambuyao, Bwerani nacho, timwe. 2Ambuye Yehova walumbira pali chiyero chake, kuti taonani, adzakugwerani masiku akuti adzakuchotsani ndi zokowera, ndi otsala anu ndi mbedza. 3Ndipo mudzatulukira popasuka linga, yense m'tsogolo mwake, ndi kutayika ku Harimoni, ati Yehova.
4 # Ezk. 20.39; Hos. 12.11 Idzani ku Betele, mudzalakwe ku Giligala, nimuchulukitse zolakwa, nimubwere nazo nsembe zanu zophera m'mawa ndi m'mawa, magawo anu akhumi atapita masiku atatuatatu; 5#Lev. 7.13nimutenthe nsembe zolemekeza zachotupitsa, nimulalikire nsembe zaufulu, ndi kuzimveketsa; pakuti ichi muchikonda, inu ana a Israele, ati Ambuye Yehova. 6#Yer. 5.3Ndipo Ine ndakupatsaninso mano oyera m'midzi yanu yonse, ndi kusowa mkate m'malo mwanu monse; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova. 7Ndipo Ine ndakumanani mvula, itatsala miyezi itatu isanafika nyengo yakukolola; ndipo ndinavumbitsira mudzi umodzi mvula, osavumbitsira mudzi wina; munda wina unavumbidwa mvula, ndi m'munda mosavumbidwa mvula munafota. 8#Yer. 5.3M'mwemo midzi iwiri kapena itatu inayenda peyupeyu kumudzi umodzi kukamwa madzi, koma sanakhute; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova. 9#Deut. 28.22; Yer. 5.3Ndinakukanthani ndi chinsikwi ndi chinoni; minda yanu yochuluka yamipesa, ndi yamikuyu, ndi ya azitona, yaonongeka ndi dzombe; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova. 10#Deut. 28.27, 60; Yer. 5.3Ndinatumiza mliri pakati panu monga m'Ejipito; anyamata anu ndawapha ndi lupanga, ndi kutenga akavalo anu; ndipo ndinakweretsa kununkha kwa chigono chanu kufikitsa kumphuno kwanu; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova. 11#Gen. 19.24-25; Yer. 5.3; Zek. 3.2Ndinagubuduza ena mwa inu, monga umo Mulungu anagubuduzira Sodomu ndi Gomora; ndipo inu munali ngati muuni wofumulidwa kumoto; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova. 12#2Maf. 20.1Chifukwa chake ndidzatero nawe, Israele; popeza ndidzakuchitira ichi, dzikonzeretu kukomana ndi Mulungu wako, Israele. 13#Mas. 139.2; Yes. 47.4Pakuti taona, Iye amene aumba mapiri, nalenga mphepo, nafotokozera munthu maganizo ake, nasanduliza m'mawa ukhale mdima, naponda pa misanje ya dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova Mulungu wa makamu.

Currently Selected:

AMOSI 4: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in