YouVersion Logo
Search Icon

AMOSI 3

3
Zoipa za Israele; aneneratu kuti adzalangidwa
1Tamverani mau awa akunenerani Yehova motsutsa, inu ana a Israele, kulinenera banja lonse ndinalikweza kulitulutsa m'dziko la Ejipito, ndi kuti, 2#Deut. 7.6; Dan. 9.12; Luk. 12.47; Aro. 2.9Inu nokha ndinakudziwani mwa mabanja onse a pa dziko lapansi, m'mwemo ndidzakulangani chifukwa cha mphulupulu zanu zonse. 3Kodi awiri adzayenda pamodzi asanapanganiranetu? 4Kodi mkango udzabangula m'nkhalango wosakhala nayo nyama? Kodi msona wa mkango udzalira m'ngaka mwake usanagwire kanthu? 5Kodi mbalame idzakodwa mumsampha pansi popanda msampha woitchera? Kodi msampha ufwamphuka pansi wosakola kanthu? 6#Yes. 45.7Kodi adzaomba lipenga m'mudzi osanjenjemera anthu? Kodi choipa chidzagwera mudzi osachichita Yehova? 7#Gen. 18.17; Yoh. 15.15Pakuti Ambuye Yehova sadzachita kanthu osawulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri. 8Mkango ukabangula, ndani amene saopa? Ambuye Yehova wanena, ndani amene sanenera?
9Bukitsani kunyumba zachifumu za Asidodi, ndi kunyumba zachifumu za m'dziko la Ejipito, nimuziti, Sonkhanani pa mapiri a Samariya, ndipo penyani masokosero akulu m'menemo, ndi ozunzika m'kati mwake. 10#Yer. 4.22Pakuti sadziwa kuchita zolungama, amene akundika zachiwawa ndi umbala m'nyumba zao zachifumu, ati Yehova. 11#2Maf. 17.3, 6Chifukwa chake, atero Ambuye Yehova, Padzakhala mdani pozungulira pake pa dziko, nadzatsitsa kukuchotsera mphamvu yako; ndi za m'nyumba zako zachifumu adzazifunkha. 12Atero Yehova, Monga mbusa alanditsa m'kamwa mwa mkango miyendo iwiri, kapena kansonga ka khutu, momwemo adzalanditsidwa ana a Israele okhala pansi m'Samariya, m'ngodya ya guwa logonapo, ndi pa mitsamiro ya kama. 13Tamverani inu, muchitire umboni wotsutsa nyumba ya Yakobo, ati Ambuye Yehova Mulungu wa makamu. 14Pakuti tsiku lakumlanga Israele chifukwa cha zolakwa zake, ndidzalanganso maguwa a nsembe a ku Betele; ndi nyanga za guwa la nsembe zidzadulidwa, nizidzagwa pansi. 15#1Maf. 22.39Ndipo ndidzakantha nyumba ya nyengo yachisanu, pamodzi ndi nyumba zaminyanga zidzaonongeka; ndi nyumba zazikuluzo zidzatha, ati Yehova.

Currently Selected:

AMOSI 3: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in